Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

TEVETA ILIMBIKITSA ACHINYAMATA OMWE ADASIYIRA SUKULU PA NJIRA KULIMBIKIRA NTCHITO ZALUSO

Mkulu wa bungwe lophunzitsa ntchito za luso la manja la Technical Entrepreneur and Vocational Education and Training Authoritiy (TEVETA), a Elwin  Sichiola, alimbikitsa achinyamata amene adasiyira sukulu panjira kuti aphunzire ntchito za manja pofuna kukhala odziimira paokha.

A Sichiola anena izi pomwe amapereka katundu osiyanasiyana pamalo osungira ana amasiye ndi a chikulire a Chisomo Orphanage and Home for the Elderly kwa Nsundwe m’boma la Lilongwe.

Mkulu woyang’anira malowa, a Bernard Chikhasu, wayamikira bungwe la TEVETA ndipo anapemphanso ena akufuna kwabwino kuti awathandizeko ndi m’dadada oti ana ndi achikulire adzigonapo.

“Ambiri mwa anawa akugona mmakomo a anthu akufuna kwabwino kamba koti tilibe malo oti ana komanso achikulire atha kumausapo,” a Chikhasu atero.

Bungwe la TEVETA  lapeleka katundu monga matilesi, sopo, ziwiya, sugar, feteleza ndi zina zambiri.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Nsundwe Stadium construction to begin in September

MBC Online

Boma latsindikanso kuti palibe afe ndi njala

MBC Online

Mayi Banda akufuna thandizo

Davie Umar
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.