Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani Sports Sports

Tabitha ndi katswiri mbambande ku France

Katswiri wampira wamiyendo wa asungwana wadziko lino, Tabitha Chawinga,amene akusewerera timu ya PSG ku France, amusankha kukhala osewera amene wakankha chikopa mododometsa mu ligi yakumeneko season ya 2023/2024.

Tabitha,yemwenso ndi osewera wodalirika wa timu yadziko lino ya The Scorchers, alinso pa mndandanda wa asungwana 11 omwe ndi akatswiri amene akhoza kulowetsedwa koyambilira atati asankhe timu yapadera mu ligi yaku France ko.

Iyeyu,amenenso amadziwika bwino kuti TC11, wamwetsa zigoli zokwana 18 mu season ya 2023/2024 ndikuthandizanso amnzake ena a timu yake ya PSG kumwetsa zigoli khumi (10).

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Vuto lakuthimathima kwa magetsi Latha kunyumba yamalamulo

Mayeso Chikhadzula

PUMP PRICES ADJUSTED

MBC Online

Mabedi waitananso Gaba

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.