Nduna yazofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu yati boma laonetsa chidwi chachikulu kuti shuga apezeke paliponse m’dziko muno.
Poyankhula ndi MBC ku Lilongwe a Kunkuyu ati kampani ya Salima Sugar yomwe panopa ili m’manja mwa boma la Malawi yayamba tsopano kufikitsa shuga msitolo zosiyanasiyana.
Izi zikudza pomwe kampani ya Salima Sugar kudzera mwa Takula Group of Companies, mmawa wa lero lachisanu yatsitsa shuga wokwana matani makumi atatu mu mzinda wa Lilongwe m’ma shop a Tutla’s.
M’modzi mwa akuluakulu a Kampani ya Takula, a Takondwa Kathumba ati akukonzanso dongosolo loti akasiye shuga okwana matani 85 ku Shoprite komanso matani 20 ku sitolo ya Ekhaya.
A Kunkuyu ati anthu ambili andale m’mbuyomu analowelera ntchito za kampani ya Salima Sugar zomwe zinachititsa kuti ntchito yopanga shuga kukampaniyi ilowe pansi.
Iwo ati boma likuchita chilichonse chotheka poonetsetsa kuti shuga azipezeka mdziko muno komanso pa mtengo wabwino.