24/07/17

Written by  Newsroom

Mai wina abindikila kamba ka ngongole

Mai wina ku Likoma akukhalira kubisala chifukwa cha ngongole. Nkhaniyi ikuti maiyo zaka ziwiri zapitazo analowa mgulu losungitsa ndi kubwereketsana ndalama ya banki nkhonde.

24
July

Koma chifukwa choti bizinesi yomwe amachita maiyo inamusokonekera, zinamukoka manja ndipo anayamba kuthawa-thawa poopa kumukwenya ngongoleyo. Pa chifukwachi anthu ena anamulangiza kuti sibwino kuti akhalire kubisala koma afunefune ndalamayo ndikukabweza ngongoleyo. Pochita mantha kuti mwina gululo likhoza kumulanda katundu ndi zina, mayiyo anapempha gululo kuti limupatse nthawi pang’ono kuti abweze ndalamayo. Apa maiyo sanakhale pansi koma kunka nabwereka ndalama kwa anthu ena achifundo ndipo zinathekadi mpaka anabweza ngongole yonse kuguluko. Tsono pano mayiyo zamukokanso manja malinga nkuti anthu omwe anamubwereka ndalama zokabweza ku banki nkhondeko ayamba kufuna ndalama zawo nthawi yomwe anagwirizana yobweza ngongoleyo itatha.Apatu anaganiza zongosamuka mderalo nkukabisala ku tchire. Pamene timalandila nkhaniyi nkuti maiyo akukhalira kubindikira ku tchire kulolera kusiya ana ake akuvutika pakhomo. Maiyo pakadali pano akuuza anthu osiyana-siyana kuti akakwanitsa kubweza ndalama za anthuwo, sadzayambilanso kutenga ngongole kulikonse.

 

Mai wina adabwisa anthu ndi zoyankhula zake

Anthu a mdera la Somba ku Blantyre agwira pakamwa ndi zomwe akulankhula mai wina mderalo. Nkhaniyi ikuti maiyo wakhala ali pa ubwenzi wa mseri ndi mwamuna wina wapa banja ndipo anthu akamudzudzula wakhala akuponyera malangizowo ku nkhongo pouza anthuwo kuti nkutheka kuti iyeyo ndi okongola. Mwini mwamunayo atatopa ndi khalidwe la mwamuna wakeyo anayamba kupemphera dzolimba ncholinga choti Mulungu amuchitile chozizwa. Masiku apitawa mayiyo anamupezerela ndi mwamuna wa mwiniyo ali buno bwamuswe ndipo apa anamenyedwa mpakana thaphya. Anthu omwe anaona izi zikuchitika ati mwamunayo anapeza mpata wothawa mnyumbamo nkusiya mai wachi masomasoyo akupumila madzala mphuno. Masiku otsatila mwini mkaziyo anangoti gululu ndi mai wa chimasomasoyo ndipo apa ndeu ya mtima bii inabuka pakati pao. Anthu ambili anaikira kumbuyo mwini mwamunayo ndipo amai ena okhudzidwa anayamba kuthidzimula nawo mai opanda manyaziyo mpaka kulira ngati mwana. Chodabwitsa ngakhale maiyo anakunthidwa amapitilizabe kulankhula mwa thamo kuti sasiyana ndi mwamuna wa mzakeyo. Pakadali pano mikoko yogona komanso nyakwawa ya mderalo yanenetsa kuti akokera ku bwalo maiyo kuti akayankhe mlandu wosokoneza banja la mwini apo bii amusamutsa mderalo.

 

Mwana adabwitsa makolo

Anthu apa banja lina mdera la Mfumu Mpama ku Chiradzulu agwira pakamwa pa zomwe wachita mwana wao pakhomopo. Nkhaniyi ikuti mwanayo yemwe anakwatila zaka zingapo zapitazo anapita mdziko la South Africa kokagwira ntchito ndikusiya mkazi wake pakhomopo. Ali ku Joni-ko mkaziyo wakhala ali pa ubwenzi wa mseri ndi njonda ina koma anthu apa banjapo akamulangiza paza khalidwe lakelo amangoponyera malangizowo ku nkhongo. Mwa zina maiyo wakhala akulankhula mwa thamo kuti ngati akufuna akubanja kwa mwamunayo akhoza kutenga ana awiri omwe anabereka ndi mwamuna wakeyo. Anthu atafufuza za nkhaniyi zinadziwika kuti maiyo ali pa ubwenzi wa mseri ndi njonda ina yochita malonda mu msika wa Limbe. Chikondicho chitafumbila maiyo anafika potenga katundu wa mwamuna wakeyo ndikukapereka kwa apongozi ake   ati mcholinga choti mwana wawoyo akadzabwera asadzaganizilenso za iye. Makolowo ataona izi anadziwitsa mwana wawo ku joniko yemwe sanatsimikize za nkhniyi. Masiku apitawa mnyamatayo anafika pakhomopo kuchokera ku South Africa koma m’malo moti alonjelane ndi abale ake anathamangira kwa mkazi wakeyo ati ponena kuti amamukonda kwambiri. Usiku wa tsikulo njonda ina ija inafika pakhomopo ndikugogoda koma chodabwitsa mkazi wa chimasomasoyo anadzambatuka ndikukatsekura ndipo apa anangotengana ndi njondayo osabwereranso. Apa mpomwe mwamunayo anatsimikiza kuti mphekeserayo inali yoona. Pamene timalandila nkhaniyi nkuti mwamunayo akukhalira kudandaula koma anthu ambiri akumudzudzula kuti ndi ombwambwana.

 

Khanda ligwilitsa anthu achisembwere

Khanda lina mdera la Mazengera ku Lilongwe linapangitsa kuti anthu ena omwe amachita za chisembwere awapezerere. Nkhaniyi ikuti mai wa khandalo wakhala ali pa ubwenzi wa mseri ndi njonda ina yoyandikana nayo. Anthu awiriwo akhala ali pa ubwenzi wa mseri potengera mwai kuti mwini mkaziyo amakhalitsa kwa mkazi wina. Pa chifukwachi ubwenzi wa anthu awiriwo unafumbila mpaka nthawi zambiri anthu amawaona akuyenda shosholo kuperekezana ku msika. Masiku apitawa anthuwo anapangana kuti akakumane pa tchire lina lapafupi ndipo izi zinachitikadi. Pamene amalowa pa tchirepo maiyo anabereka khanda kumbuyo chifukwa choti pa nthawiyo panalibe munthu yemwe akanamusiila mwanayo. Macheza ali mkazi mwanayo analira zomwe zinapereka chidwi kwa anthu ena omwe amaomba njerwa chapa fupi ndi malowo. Apa anthuwo chifukwa chodabwa ndi kulira kwa khandalo anayenda monyang’ama koma anagwira pakamwa atapezerela njondayo ndi maiyo ali buno bwamuswe. Apa anthuwo mopsya mtima anamenya awiriwo kwa chakwanu leka. Pamene timalandila nkhaniyi nkuti njonda ya mchuunoyo pamodzi ndi mai wachimaso-masoyo atawakokera ku bwalo kuti akayankhe mlandu wonyazitsa mudzi. Komabe ngakhale izi zili chomwecho anthuwo amenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sasiyana . Pakadali pano mabanja a anthu awiriwo atha.

Get Your Newsletter