20/07/17

Written by  Newsroom

Mai wina odziwika ndi zauzimu achita manyazi
Mai wina wodziwika bwino pa nkhani za Ambuye kwa Kaphuka ku dedza akuyenda njira zodula chifukwa cha manyazi.

20
July

Nkhaniyi ikuti mwamuna wa maiyu amakhala ku Lilongwe komwe amagwirako ntchito komano chosangalatsa nchakuti banja lao lakhala likuyenda bwino lomwe kwa zaka zambiri. Miyezi ingapo yapitayi maiyo amafuna ndalana ina kuti agwiritse ntchito pa zofuna zake. Koma ataona kuti ndalama yomwe anamupatsa yatha mosadziwika bwino ndipo anagotsala khwakhwakhwa anakonza mapulani onamiza mwamuna wakeyo kuti kumudzi kwao kwachitika maliro. Mwamunayo sanavute koma anamuuza mkaziyo kuti adikire kwa tsiku limodzi koma osadziwa kuti mwamunayo amafuna kufufuza za zovutazo. Apa anthu aku chikaziwo anauza mwamunayo kuti za malirozo akumvera mkamwini waoyo ndipo mwamunayo analephera kupitiliza nkhaniyo ndipo anangoidula foni. Mphekeserayo inawanda kumudziko kuti mai wa Mulunguyo ndi amene anakonza bodzalo. Nkhaniyi itawanda mdera lonselo komanso ndi kumpingo maiyo akuyenda njira zodula chifukwa cha manyazi. Pakadali pano akuchimuna nawo akhalirana pansi kuti aone chomwe angachite naye mpongozi waoyo.


Chipwilikiti pa maliro
Mwambo wa maliro unasokonezeka mdera la Thomas m’boma la Thyolo. Nkhaniyi ikuti magulu ena omwe anasonkhana pa siwapo, anamfedwa akukhulupilira kuti anayambitsa ndewu zomwe zinakwiyitsa m’modzi mwa mwana wa malemuyo. Pa chifukwachi mwana woyamba wa Malemuyo anadabwitsa anthu pa maliropo polankhula mosimbwa kuti akhoza kuwalipira ndalama chifukwa cha ntchito yomwe agwira pa maliropo. Mwa maguluwo ndi monga anthu ophika, omwe amalira, adzukulu ndi ena . Chipwilikiti chinachitika chifukwa mwambo wa malirowo unachedwa chifukwa mwa zina ana a Malemuyo a m’maiko akunja amafuna kuti aonetse chikondi chomwe anali nacho pa mai awowo zomwe anthu ena sanagwirizane nazo kutengera nthawi yomwe anamwalirila maiyo. Pa chifukwachi kusagwirizana kunabuka zomwe zinachititsa kuti mwamunayo auze anthu onse omwe amathandiza pa zovutazo kuti awalipila ati chifukwa choti iwo ndi omwe anadzetsa chisokonezo. Chifukwa cha mkwiyo adzukulu anasiila mkuluyo ntchito yakumanda. Pakadali pano mwamunayo wadzudzula anthu ena m’mudzipo kuphatikizapo amai kuti ngosazindikira komanso wanenetsa kuti ubale wao ndi anthuwo watha. Mikoko yogona komanso anthu ena ati sakukaika kuti mwina mwamunayo ndi nthakati ndipo ati akokera ku bwalo mkuluyo kuti akayankhe mlandu wolaula mudzi.

 

Banja livuta kamba kokana ufiti

Banja lina kwa gulupu Kamutu mdera la mfumu Nthunduwala m’boma la Kasungu laweyezeka kamba koti mkazi wabanjalo akukana kuphunzira ufiti. Nkhaniyo ikuti mderalo muli mkulu wina yemwe ali ndi akazi atatu. Ndipo masiku apitawo mkuluyo anapempha mkazi wake wachiwiri kuti amupatse tsitsi lake kuti akapangire zizimba. Nkhaniyi inachititsa mantha mkaziyo ndipo anakana kuchita monga njondayo imafunira. Apo mwamunayo sanachitire mwina koma kugwira mkaziyo ndikumuthira makofi kolapisa mpaka mkaziyo kumusiya ali thapsya. Ndipo ataona kuti mkaziyo wakomoka njondayo yathawa pakhomopo ndipo sikudziwika komwe ili. Pakadali pano anthu mderalo ali yakali-yakali kufuna-funa njondayo kuti ikayankhepo mlandu.

Get Your Newsletter