You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma
19
August

ATAYA ZAMBILI POFUNA ZAMBILI

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 1377 times

Mkulu wina ku Thondwe mboma la Zomba wapita ku Lilongwe asakufuna, mbili itamveka kuti wapereketsa ndalama yokwana 200 thousand kwacha chifukwa chofuna kulemera.


Nkhaniyi ikuti mkuluyo amachita geni kuyambira kalekale koma akuti zinthu sizimayenda.  Ali mwapenda-penda chomwecho, m’deralo munafika munthu wina yemwe amanamiza anthu kuti ali ndi mankhwala wothandiza anthu omwe akufuna kulemera.  


Mkuluyo atamva izi, anadololoka mtima mpaka kumufunafuna munthuyo kuti amuthandize pa nkhaniyi.  Awiriwa atakumana, anakambirana zofunika kuchita kulemerako kusanadze ndipo anamuuza mkuluyo kuti apereke K2,00 000 yoti akayankhulirane ndi azimu.   

Chifukwa chotopa ndi umphawi, mkuluyo anakunkhakunkha ndalamayo nkumuninkha munthuyo pomwe anamutsimikizira  kuti sipatha sabata, awona zodabwitsa ku nyumba kwake.   Mwa zina munthuyo anauza mkuluyo kuti akapeze chisaka chabwino chomwe amati mudzifikira ndalamazo azimu akangoyankha. Izitu zimachitika pa uwiri wawo moti palibe amadziwa zomwe anthuwa amakambirana.


Koma nkhaniyi inaululika pamene mkuluyo anadikira mpaka sabata ziwiri koma popanda cholowa mu sakamo. Kenaka atayamba kumufufuza munthuyo, anazindikira kuti ndi mbava chifukwa ambili amati sakumudziwa  ndi wachilendo m’deralo.  Apa mkuluyo anazungulira mutu mpaka kumamusaka munthuyo m’nthumba la buluku. Chifukwa cha manyazi, mkuluyo wangosowa m’deralo pomwe watsanzika achibale ake kuti akupita ku Lilongwe kuti mwina ikamupite mphepo ina.

19
August

AMENYEDWA NDI MWANA KAMBA KOZEMBA

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 1690 times

Anthu a m’mudzi wina mdera la Mfumu Mabulabo mboma la Mzimba anafa ndi phwete pamene mkulu wina anamenyedwa ndi mwana wachichepere chifukwa chozemba kubweza ngongole.  

Nkhaniyi ikuti m’deralo muli mwana wina yemwe amagulitsa mandasi  ndipo akuti anthu ambili anamuzolowera pomwe nthawi zina amatha kuwakongoza nkudzatenga ndalamazo tsiku lotsatira.  

Patsikulo mkuluyo atamuona mwanayo, anamuitanitsa nkutengamo mandasi anayi pa mtengo wa 2 hundred kwacha.  Mwanayo atafunsa za ndalama, anamuyankha kuti akayendayenda abwerenso pamalopo akatenge ndalama yake chifukwa pa nthawiyo anali ndi yosasintha.  

Apatu mwanayo anakhulupilira zimenezi kamba koti anamuonetsa 2 thousand kwacha yosasintha. Koma mwanayo anakhumudwa atapitanso kwa mkuluyo kuti akatenge ndalama yakeyo, kumupeza palibe.  

Kuyambira tsikulo,mkuluyo wakhala akuzemba ngongoleyo, koma poti amati chozemba chidakumana nchokwawa, patsikulo mkuluyo anangoti gululu ndi mwanayo.  

Atamufunsa za ndalamayo anayankha mwa thamo amvekere adzabweza ngongoleyo akadzafuna zomwe sizinasangalatse mwanayo.  

Pamenepa mwanayo anayamba kumuvutitsa mkuluyo kuti amupatse ndalama yakeyo koma mkuluyo m’malo mongopereka ndalamyo anamuponyera chibakera  mwanayo.   

Apatu mwanayo anazinda chibakeracho zomwe zinachititsa kuti mkuluyo agwe yekha ndi chibakeracho. Nthawi yomweyo mwanayo anathamanga kukamukhalira mkuluyo pa msana nkuyamba kumuumbuza.

Anthu omwe amaonelera ndeuyo, anafa ndi phwete maka poganizira momwe mkuluyo anagwera ndi chibakera chake chomwe. Izitu zimachitika, ana ena omwe amachokera ku sukulu akuchemelera nzawoyo ngati muja achitira pa masewero a nkhonya.  

Ataona kuti zavuta mkuluyo anangomuluma mwanayo ndipo nthawi yomweyo anadzukao pamsanapo,  ndeuyo nkuthera pomwepo.

Pakadali pano mkuluyo walumbira kuti sapereka ngongoleyo ati kamba koti ndalamayo yalowa m’malo mwa  chipongwe chomwe mwanayo wachita  pomuvivinyiza m’dothi, anthu akuona.     

22
July

NSANJE IVUTA KU CHIKWAWA

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 1086 times

Zomwe akuchita mkulu wina kwa Mgabu mboma la Chikwawa zikudabwitsa anthu pomwe akumachitira nsanje mkazi yemwe anasiyana naye ukwati. Nkhaniyi ikuti mkuluyo poyamba anakatenga mkazi ku Thyolo nkumakakhala naye kwawo monga mtengwa. Mayiyo akuti ndi wotakataka ndipo atapita ku Chikwawako anapitiliza geni yake yogulitsa kaunjika. Koma vuto nloti mwamunayo amaonjola ndalama za mayiyo akangozisiya poyera, ndipo izi zakhala zikumuwawa mayiyo maka chifukwa choti akamubera ndalamazo amakapatsa akazi ena. Potopa ndi khalidweli mayiyo anamuuza mwamunayo kuti akufuna akamutule kwawo koma mwamunayo amangonyalanyaza. Tsiku lina mwamunayo anafika ndi mkazi wina pakhomopo nkumuuza mkaziyo kuti achoke pakhomopo adzipita kwawo komwe akufunako. Mayiyo atamva izi, anangoti laponda la mphawi diwa, nthawi yomweyo kupakira katundu wake nkuona msana wa njira. Tsono mayiyo atasiyanitsa momwe geni ake imayendera mbomalo ndi kwawo ku Thyolo, anaganiza zochita lendi m’dera lomwelo.   Tsono chomwe chikumachitika panopa nchakuti, mwamunayo walemba aganyu woti azimulonda mayiyo moti anawauza kuti akandzangomuona mayiyo ndi mwamuna wina adzamudziwitse msanga. Koma anthu atamva nkhaniyi, adabwa nazo kwambili ati kaamba koti mwamunayo ndiye anamuthamangitsa mayiyo pakhomopo. Pakadali pano anthu ena alangiza mayiyo kuti ngati sakumufunadi mwamuna wakeyo ndi bwino adzingopita kwawo ku Thyolo poopa kuti mwamuna wakeyo angamuchite chipongwe.

22
July

Gulu la mayi ena mu mzinda wa Blantyre likuganiza zokhaulitsa nzawo wina yemwe ali nchizolowezi chomangoyenda mosalabadira kuti ali ndi ana. Nkhaniyi ikuti mayiyo ali ndi ana atatu koma onsewo bamboo wake wake. Mayiyo yemwe amachita geni yogulitsa masamba ndi tomato mu msika wina, akuti amati akachoka m’mawa, amafika pakhomopo usiku, ndipo nthawi zambili amasiya anawo opanda chakudya. Kwa nthawi yaitali, anthu oyandikana naye nyumba akhala akuwapatsa chakudya anawo pokumva chisoni kuti ndi ang’ono ang’ono woti sangathe kudzisamalira okha.   Tsiku lina mayi wina pa lainipo anayiyambitsa nkhaniyi pomadandaulira anzake ena pa momwe mayi nzawoyo akulelera ana ake. Apatu amayi ena omwe samadziwa za khalidwe la mayiyo anati mpofunika kumuphunzitsa mayiyo kuti adziwe udindo wake ngati kholo la anawo. Amayiwo agwirizana kuti tsiku lina adzawatenge anawo nkukawabisa pa khomo lina kuti awone zomwe achite mayi nzawoyo. Amayiwo ati akadzawafunsa za ana akewo mpomwe adzamuuze nkhawa zawo kuti mwina asinthe khalidwe lakelo. Pakadali pano gulu la amayiwo lati lakonzeka kumenyera ufulu wa anawo wolandira chisamaliro cha mayi awo.

Page 3 of 155

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter