You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma
01
September

Mkulu wina kwa Mfumu Masula mboma la Lilongwe amudula mlomo atamupezelera ndi mkazi wa mwini m’nyumba.

 Nkhaniyi ikuti mkuluyo ali ndi udindo waukulu m’mudzimo koma m’malo moti adzionetsa chitsanzo chabwino, amatchuka ndi mbili zozembera akazi a eni potengerapo mwayi  kuti ali ndi udindo m’mudzimo.


Tsono chomwe chachitika nchakuti m’deralo muli njonda ina yomwe ili ndi akazi awiri ndipo mwa chikonzero chake, imapereka mashifiti kwa akaziwo.


Patsikulo njondayo itapita kwa mkazi wake wamkulu, wang’onoyo naye anayitanira mkulu waudindoyo kunyumbako.  


Atafika ku nyumbako, anapeza mayiyo ali ku bafa ndipo mosajejema anakalowa mnyumba mpaka kukagona pa bedi ku chipinda.


Anthu ena omwe amaipidwa ndi zomwe zimachitika pakhomopo, anayimbila foni mwini mkaziyo kuti afike msanga adzazionere yekha.  


Mwa machawi mwini mkaziyo anatenga wakabaza ulendo kunyumbako komwe anakapezadi mkuluyo ali neng’a pa bedi ku chipindako.  


Pamenepa mwini mkaziyo anazithethetsa zibakera moti chimodzi chinafikira pa momo nkunyotsoleratu.  


Pakadali pano mkuluyo wakalandira thandizo ku chipatala komabe wasanduka olumala poyerayera pomwe akungobindikira mnyumba chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.

01
September

AKOMOKA NDI KACHASU KU MZIMBA

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 1003 times

Mnyamata wina m’dera la Mfumu Mabilabo mboma la Mzimba wabwelera lokumbakumba, atakomoka ndi kachasu.   

Nkhaniyi ikuti mnyamatayo ndi mbiya ng’ambe moti sizimatheka kukhala osamwa tsiku liri lonse.


Nthawi zambii mnyamatayo asanapite kokaledzera, amayamba waphika nsima nkudya koma pa tsikulo anangochoka m’mimba mulibe kanthu.

Atapapila kabangayo analedzera mopyola muyezo ndiye ndi kusadyako analenguka nawo mowawo mpaka anagwa pansi nkukomoka.  

Anthu ena atamuona anaphikitsa phala kwa mayi wina nkumukanula kukamwa kumumwetsa ndipo apo anaoneka ngati wapezako mphamvu.

Komabe anthuwo ataona kuti sizikuthandiza kwenikweni anamutengera ku chipatala komwe anakatsitsimuka.

Pakadali pano achibale a mnyamatayo amulangiza kuti asiye kumwa mowa mwauchidakwa pomwe anati akapitiliza khalidwe lakelo, tsiku lina adzakomoka koma sadzadzukanso.  


Zikuoneka kuti panopa mnyamatayo wadekha chifuwa kuyambira tsikulo sakupitanso kopapila mowawo pomwe akumauza anthu kuti  amalota anthu ena akumukokera m’dzenje.

19
August

M’dera la Mfumu Wimbe mboma la Kasungu, mkulu wina yemwe anasiya mkazi wake kuno kumudzi kupita ku joni kukazisaka, wakhumudwa kwambili atamva kuti mkazi wakeyo ali ndi pathupi.  


Nkhaniyi ikuti mkuluyo anapita ku joniko zaka zingapo zapitazi ndipo akuti amamutumizira mkaziyo ndalama zokwana mwezi uli onse.

M’malo moyamika thandizo la mwamuna wakeyo, mayiyo amadya ndalamazo ndi mphongo zina osalabadiranso zoti ndalamazo ndi thukuta la munthu wina.  


Achibale komanso anthu ena omufunira zabwino mayiyo, anamudzudzula kuti asinthe khalidwe lakelo chifukwa tsiku lina adzalilira ku utsi, mwamuna wake akadzatulukira za zibwenzi zakezo.   

Pasanadutse nthawi atalandira malangizowo, mayiyo wapezeka ali ndi pathupi pomwe amuna onse omwe amayenda nawo akumusasa.  Mwamuna wake ku joni atamva nkhaniyi, wangolamula kuti asadzamupeze pakhomopo moti poopa kuyaluka wangosamuka mwakachete-chete  ku chithando-ko kupita kumudzi kwawo.  

Kumeneko anthu atamuona nkumva nkhani yake, akungomuseka kuti wachita zopusa malinga nkuti amayi ambili kumudziko amamusilira kuti mwamuna wakeyo amamutumizira ndalama zankhani- nkhani zomwenso amatha kuwatumizira makolo ake kumudzi. Pakadali pano mayiyo akukhalabe kumudzi kwawoko koma mosowa mtendere chifukwa nkhani yakeyo yawanda mdera lonselo, ndiye anthu akamuona akungomulozerana.

19
August

NJOKA YOKAWA IGWIDWA KU KASUNGU

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 1238 times

Mkulu wina kwa Wimbe mboma la Kasungu wazunguzia mutu munthu wina yemwe sakudziwika atagwira njoka yake yokawa.


Nkhaniyi ikuti mkuluyo ndi nkhalakale pa bizinesi koma zimamveka kuti ali ndi njoka yokawa.  


Mwa zina anzake a bizinesi pa sitolozo akagulitsa katundu, ndalama sizimaoneka bwino ndipo atafufuza bwino anadziwa kuti mkuluyo akumakawa ndalama za anzake.


Ena mwa abizinesiwo akhala akumufunsa nkhaniyi komanso kumudandaulira kuti ngati nkhaniyi ili yoona asinthe khalidwelo, koma mkuluyo amakanitsitsa kwa ntu wa galu kuti sakudziwapo kanthu pa nkhani yokawayo.  


Tsono masiku apitawa anzakewo atatopa nkugwira ntchito ya bule, anamupita pansi kumupitilira kwa sing’anga wina kukatenga mankhwala woti njoka yakeyo ikapita kokawako, ikakodwe komweko.  

Dzana laliwisili, mkuluyo anatuma njoka yakeyo kupita ku golosake ya Chikhwaya china  ndipo inakakodwa komweko.  Mkuluyo anaswera usiku onse osagona kudikira njoka yakeyo koma ku njira kunali zii ndipo apa anangodziwiratu kuti yalakwa.  Kutacha m’mawa mkuluyo anakhala ngati wapenga chifukwa amangofunsa aliyense za njoka yakeyo koma samatchula kuti njoka amangoti katundu wake wasowa.  Mkuluyo anayenda pafupifupi dera lonselo koma palibe anamuyankha zomveka.

Mkuluyo panopa akusowa mtengo wogwira moti akungochondelera aliyense kuti ngati akumusungira katundu wakeyo angokambirana kuti alipire ndalama zingati kuti amupatse katundu wakeyo.  

Pakadali pano anthu ambili m’deralo ati nkutheka kuti alipo yemwe akusunga katundu wa mkuluyo koma akungofuna kumukhaulitsa kuti asiye mchitidwe wake oipawo.

Page 2 of 155

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter