You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma
21
May

5/21/2021

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 1247 times

Mnyamata wina mdera la mfumu Kaphuka mboma la Dedza wakumana nazo, anthu a mderalo atamuphunzitsa kukhala chifukwa cha zomwe anachita. Mkuluyo nthawi zambiri amakonda kuvutitsa komanso kuchita zosimbwa pakati pa abale ake ndi makolo zomwe zakhala zikukwiitsa anthu ozungulira ndi akubanja. Tsiku lina anayambana ndi mchemwali wake pa nkhani yoti ati amafuna chipangizo cha foni zomwe mchemwali wakeyo anakanitsitsa mpakana kusamvana kunabuka pakati pawo. Nkhaniyi inakwiitsa makolo ndipo sanaimve koma kumema anthu ena azachitetezo cha mderalo kuti akhaulitse mkuluyo. Anthuwo sanachedwe koma kukwidzinga kamunayo ngati tonde opita ku butchare nkukamangilira ku ntsinje usiku kwinaku atamupaka matope. Mkuluyo anadzimvera chisoni koma anayesa kupempha chikhululuko koma sizinaphule kanthu kufikira nthawi yonse yachilango itafika kumapeto.

21
May

5/21/2021

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 1113 times

Read 954 times

Chidakwa china mdera la mfumu Khonsolo mboma la Mzimba chayamba chadukiza kupezeka pa malo ena omwera mowa chifukwa cha zomwe zinamuchitikira. Nkhaniyi ikuti mkuluyo akayamba kukondwa chifukwa chodakwa amakhala ngati alipo yekha odziwa kudzipepesa mderalo chifukwa ngakhale zidakwa zinzake zimagoma naye. Mwazina amavina mdukeduke moti patsikulo anavina mpakana buluku lake kuphwathuka. Koma zidakwa zina zachizimayi kunali kufa mphwete uku ena akumukwakwazira kumbali . Panthawiyo mkuluyo samadziwa kuti buluku laphwathuka ndipo atazindikira analiyatsa liwiro kuthawa mpakana pano palibe akumvetsabe za momwe anachokera pa malopo. Moti ambiri ati mwamunayo akubisala ku Nyanja kuthandiza asodi kupha msomba ndipo zikuoneka kuti atengapo nthawi kuti abwerele mderalo pochita manyazi ndi nkhaniyi. China chomwe sakubwerela mchakuti ambiri akusunga zithunzi za mkuluyo za nkhaniyi zomwe ati ngakhale alongo ake azunguzika nazo mitu. Ena ati mkuluyo nzofuna chifukwa akhala akumulangiza koma wangokhala osimbwa komanso amadzitamandila kuti ngopeza.

21
May

5/21/2021

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 985 times

Anthu akwa gulupu Kavithiwa mdera la mfumu Chikowi mboma la Zomba akulozerana mkulu wina chifukwa chochita zinthu zombwambwana. Mng’ono wake wa mkuluyo anapezeka ndi mlandu ogwilira masiku apitawa ndipo pakadali pano ali mchiotolokosi chaza chitetezo. Mkuluyo powona kuti ndi yekhayo m’bale wake anayamba kumangolalatila aliyense kuti anthu mudzimo ngoipa ndipo dzana-dzana laliwisiri anatukwana m’modzi wa azahitetezo. Koma anangowona atachita izi chifukwa gulu lonse linapezera mwai olangira mkuluyo chifukwa ati mkarekare amafunafuna mkuluyo. Anthu akukhalira kumulozerana mkuluyo ndipo amuchenjeza kuti asamalire ndi khalidwe lake losimbwa chifukwa pakhale-khale akapitiliza amusamutsa. Njondayo pano ili njenjenje chifukwa tsiku lililonse akuophyezedwa ndi enanso ngakhale osawadziwa. Anthu mderalo ati sangaikire kumbuyo mkuluyo chifukwa m’bale wakeyo analaura mudzi pomwe anagwilira mai wina wachikulire. Mbiri ya mwamunayo yaipa mderalo ndipo naye akukhalira kudziyankhulira kuti kaya anadziyambiranji.

Page 7 of 155

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter