You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma
22
May

21-05-21

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 1223 times

 

Adzukulu okumba manda kwa Gulupu Mkwayila mboma la Neno achenjeza akuluakulu a m’mudzimo kuti adzasiya kukumba manda akapitiliza khalidwe lawo lomangophangira chakudya.   Nkhaniyi ikuti m’mudzimo munali mwambo olima kumanda ndipo monga mwa mwambo anthu anaphika zakudya kuti anthu adye akamaliza kugwira ntchitoyo. Tsono chomwe chinachitika nchakuti anthu anaphika nsima ya ufa oyera, gramil komanso mgaiwa ndipo akuluakuluwo amangosankha nsima yoyera ndi gramil komanso ndiwo za nkhuli zomwe zinakwiyitsa amayi omwe anakonza chakudyacho. Pamenepa panabuka kusamvana, amayiwo atadzudzula akuluakuluwo pa zomwe anachitazo. Ndipo adzukulu atamva nkhaniyi, anenetsa kuti khalidweli likapitilira, akuluakuluwo azikakumba okha manda m’mudzimo mukachitika maliro. Pakadali pano akuluakulu omwe akukhudzidwa ndi nkhaniyi akuyenda ali wera wera chifukwa cha manyazi.

22
May

21-05-21

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 770 times

Mayi wina kwa Mfumu Mdunga mboma la Kasungu watenga mbili atakalowerera mwamuna wina ati kamba koti amachedwa kumukwatira. Nkhaniyi ikuti mayiyo anali pa banja koma linathapo chifukwa cha khalidwe lake lolongolola komanso kulalata mosamezera malovu. Amuna ambili akhala akumufunsira koma akangomva mbili yake, samapitilizanso maganizo awo ofuna kumanga banja ndi maiyo. Masiku apitawa mwamuna ochokera m’mudzi wina m’deralo, anamufunsira mayiyo ndipo chibwenzi chinayambika mpaka kuyamba kugwirizana za banja. Koma anthu omwe akumudziwa bwino mayiyo anamuchenjeza mwamunayo kuti akalimbe, chifukwa mayiyo ndi olongolola, sadziwa zokambirana nkhani mwa mtendere. Mwamunayo atamva izi, anabwerera m’mbuyo ndipo anadula phazi pakhomo pa mayiyo. Tsono Mayiyo ataona kuti mwamunayo sakufikanso pamudzipo, anangonyamuka ulendo omulondola kwawo komwe anakapeza mwamunayo ali kumunda kokolola chimanga. Apatu anamulondola kumunda komweko nkukamuuza kuti sapitanso kwawo, wabwera kudzalowa banja. Mwamunayo anayesera kumusasa mayiyo koma zinakanika moti tikunena pano, mayiyo adakali kwa mwamunayo ndipo anthu ambiri kumeneko akungopukusa mitu kusowa chonena.

22
May

21-05-21

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 747 times

Mai wina wachimasomaso m’dera la Mfumu Chilooko mboma la Ntchisi, waona polekela atamukuntha kolapitsa chifukwa chokhala pa ubwenzi ndi mwamuna wa nzake. Nkhaniyi ikuti mayiyo amagwira ntchito limodzi ndi mwamuna wake ndipo ali pantchitopo anayamba kuzemberana ndi mwamuna wina wapabanja zomwe zinachititsa kuti asiyane banjalo. Mkazi wa mkuluyo atamva nkhaniyi amangowawenderera koma akuti amalephera kuwagwira. Pamenepa mayiyo analephera kuugwira mtima ndipo tsiku lina anapita ku ntchito kwa mayiyo, atamangira nsalu nchiuno koma mkati atavalamo buluku. Atafika uko anafunsa za mayiyo ndipo atamuona anamuthamangira nkuyamba kumuthidzimula kwinaku akumulalatira kuti apeze wake mwamuna. Mwamwai anthu ena analeretsa nkhondoyo koma mai wachimasomasoyo akunenetsa kuti atengana ndi mwamunayo kamba koti wamuvulaza ndipo wati masiku akudzawa apita kwawo ku Kasungu kukatsanzika kuti akukalowa banja. Chokhumudwitsa nchakuti mwamunayo akuvomereza zimenezi ndipo akunenetsa kuti amusiya ukwati mkazi wakeyo ati kamba koti wamuchititsa manyazi.

22
May

21-05-21

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 826 times

Mwamuna wina kwa Mbela mboma la Balaka amudzudzula chifukwa chomenya mkazi wake osalakwa pomuganizira kuti akuzemberana ndi mphongo ina.   Nkhaniyi ikuti mwamunayo ndi wa nsanje yoopsya moti saafuna kumuona mkazi wakeyo akuyankhulana ndi munthu wa mwamuna. Tsono chomwe chinachitika pa tsikulo nchakuti mkazi wa mkuluyo amagona pa khonde pa nyumba yake pamene mwamuna wake anali m’nyumba kuonera mpira. Mosakhalitsa mu njira yapafupi ndipakhomopo pamadutsa mnyamata wina koma pa nthawiyo nkuti akulankhulana ndi munthu wina pa foni yake ya m’manja. Mwamunayo atamva mau achimuna panjapo anaganiza kuti akuyankhulana ndi mkazi wake ndipo nthawi yomweyo anadzambatuka m’nyumbamo kusiya kuonera mpirawo, nkufikira kutsamwa mkazi wakeyo pakhosi, koma chonsecho mkaziyo anali mtulo. Pamenepa mkaziyo anadzidzimuka mokuwa ndi mantha poganizira kuti ndi wachiwembu. Izi zinachititsa kuti anthu ena apafupi athamangire ku nyumbako kuti akawone chomwe chikuchitika. Mwamunayo ataona anthuwo anadziwa kuti walakwitsa kwambili ndipo anangokokera mkazi wakeyo m’nyumba nkuthamangitsa anthuwo pakhomopo. Pamenepa anayamba kumupepesa mkazi wakeyo ndipo tsiku lotsatira anakamugulira zitenje za Java ziwiri ati ncholinga choti asaganize zopita kwawo. Komabe ngakhale izi zili chomwechi, mayiyo wakadandaula nkhaniyi kwa ankhoswe pamene mwamunayo akumayenda mogwetsa nkhope yake pansi chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.

Page 6 of 155

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter