You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma
21
May

5/21/2021

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 501 times

Chidakwa china mdera la mfumu Khonsolo mboma la Mzimba chayamba chadukiza kupezeka pa malo ena omwera mowa chifukwa cha zomwe zinamuchitikira. Nkhaniyi ikuti mkuluyo akayamba kukondwa chifukwa chodakwa amakhala ngati alipo yekha odziwa kudzipepesa mderalo chifukwa ngakhale zidakwa zinzake zimagoma naye. Mwazina amavina mdukeduke moti patsikulo anavina mpakana buluku lake kuphwathuka. Koma zidakwa zina zachizimayi kunali kufa mphwete uku ena akumukwakwazira kumbali . Panthawiyo mkuluyo samadziwa kuti buluku laphwathuka ndipo atazindikira analiyatsa liwiro kuthawa mpakana pano palibe akumvetsabe za momwe anachokera pa malopo. Moti ambiri ati mwamunayo akubisala ku Nyanja kuthandiza asodi kupha msomba ndipo zikuoneka kuti atengapo nthawi kuti abwerele mderalo pochita manyazi ndi nkhaniyi. China chomwe sakubwerela mchakuti ambiri akusunga zithunzi za mkuluyo za nkhaniyi zomwe ati ngakhale alongo ake azunguzika nazo mitu. Ena ati mkuluyo nzofuna chifukwa akhala akumulangiza koma wangokhala osimbwa komanso amadzitamandila kuti ngopeza.

21
May

5/21/2021

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 502 times

Anthu akwa gulupu Kavithiwa mdera la mfumu Chikowi mboma la Zomba akulozerana mkulu wina chifukwa chochita zinthu zombwambwana. Mng’ono wake wa mkuluyo anapezeka ndi mlandu ogwilira masiku apitawa ndipo pakadali pano ali mchiotolokosi chaza chitetezo. Mkuluyo powona kuti ndi yekhayo m’bale wake anayamba kumangolalatila aliyense kuti anthu mudzimo ngoipa ndipo dzana-dzana laliwisiri anatukwana m’modzi wa azahitetezo. Koma anangowona atachita izi chifukwa gulu lonse linapezera mwai olangira mkuluyo chifukwa ati mkarekare amafunafuna mkuluyo. Anthu akukhalira kumulozerana mkuluyo ndipo amuchenjeza kuti asamalire ndi khalidwe lake losimbwa chifukwa pakhale-khale akapitiliza amusamutsa. Njondayo pano ili njenjenje chifukwa tsiku lililonse akuophyezedwa ndi enanso ngakhale osawadziwa. Anthu mderalo ati sangaikire kumbuyo mkuluyo chifukwa m’bale wakeyo analaura mudzi pomwe anagwilira mai wina wachikulire. Mbiri ya mwamunayo yaipa mderalo ndipo naye akukhalira kudziyankhulira kuti kaya anadziyambiranji.

21
May

5/21/2021

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 312 times

Mkulu wina mdera la mfumu Chimaliro mboma la Thyolo wati zangovuta koma banja amalifuna pomwe wasamuka pachikamwini chifukwa cha khalidwe la anthu apa banjapo makamaka ana. Nkhaniyi ikuti mkuluyo anafika pamudzipo zaka zingapo zapitazo ndipo malingana ndi watitumizira nkhaniyi mkuluyo ngodzilimbikira pa ntchito zakumunda. Pachifukwa-chi ataona kuti mpofuna kupitiliza kukhala odzidalira anagula njinga yake yamoto kuti adzichititsa hayala. Koma masiku apitawa anadabwa mwana wake wamwamuna akumuuza momuophyeza kuti amupatse njingayo kuti ikhale yake. Mkuluyo sanavute koma kumulangiza kuti kulibwino apatse ena kuti pamudzipo adzipeza kangachepe. Mwanayo apa analusa mkuyamba kulalatila atate wake powauza kuti iwo ngobwera ndipo akapitiliza ndiza nkutuzo asamuke. Nkhaniyi inakwiitsa kwambiri mkuluyo ndipo usiku anthu ali mtulo anakwakwaza njinga yake nkukailizira kwina uku zinthu zake monga magombeza, majekete komanso ma solar atamangilira. M’mawa kutacha anthu ndi pomwe anazindikira kuti mkamwini wadula waya. Mkazi wa mkuluyo usiku analephera kunyengerela mwamuna wake koma kuti anakanitsitsa ponena kuti ati adzafera za eni. Anthu mderalo adzudzula apabanjapo kuti akhala akulekerela khalidwe la mwanayo zomwe ati zachititsa kuti mkamwini yemwe amathandiza asamuke kuti maiyo atsale padzuwa.

21
May

5/21/2021

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 188 times

Mai wina mdera la mfumu Wimbe mboma la Kasungu wazunguzika mutu chifukwa chotaya mwai wa banja. Ntchembereyo yakhala pa banja losililika kwa nthawi mpakana mphatso ya ana. Koma ngakhale zili chomwechi maiyo anawilikiza chibwana chifukwa wakhala akuyenda mwamuna wake njomba komanso mwano. Mwamunayo wakhala akupilira koma zinafika pomukora mpakana kuthetsa banja ndi maiyo. Naye pokwiya anatuta ana ake onse ponena kuti sangamusiire mkuluyo koma choseketsa patangodutsa masiku ochepa ana onse anabwerela kwa atate awo. Izi zapereka chithunzi kuti anawo akudziwa za khalidwe la Mai awo komanso kuti atate awo ndi mlerakhungwa. Maiyo akumulozerana chifukwa cha nkhaniyi ndipo ati akumauza anzake kuti kaya chinamuona mchani chifukwa wataya mwai wa banja. Nkhani ya ntchembereyo yawanda mdera lonselo la Wimbe ndipo wasanduka chitonzo pakati pa amai anzake omwe nawo akuti akaika zoti mai nzaoyo nkudzapezanso mwai wa banja. Ena ongofuna kukolezera nkhani akawafunsa ana kuti mchifukwa ninji akukhala kwa atate awo . iwo akumayankha osajejema kuti atate awo ngokoma mtima. Komabe ena ati nkutheka kuti mwamunayo naye ali mpoipira pomwe anthu ongozionera kutali sakuzidziwa.

Page 5 of 152

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter