You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma
22
July

Mwambo wa maliro unasokonekera m’dera la Mfumu Kwataine mboma la Ntcheu chifukwa cha njuchi zomwe zinabalalitsa anthu ku manda. Nkhaniyi ikuti m’mudzimo munachitka maliro a munthu wina odziwika bwino ndipo monga mwa mwambo anthu anasonkhana pa nyumba ya siwa. Pa tsiku loika malirowo, adzukulu analawira kokumba manda ndipo atamaliza ntchitoyo anatumiza uthenga kumudzi. Mwambo wakukhomo unayenda bwino lomwe mpaka anthu kunyamula zovutazo ulendo wakumanda. Koma mwambo uli mkati kumandako, njuchi zomwe sizinaoneke komwe zachokera, zinayamba kubalalitsa anthuwo ndipo akuti ambili mwa iwo anavulala pothawa komanso ena kulumidwa ndi njuchizo. Yemwe watumiza nkhaniyi wati panatenga nthawi yaitali njuchizo zikuulukabe kumandako ndipo apa mikoko yogona itagundana mitu, inangoganiza zokaika malirowo pakhomo pa mkuluyo. Pamenepa amuna ena olimba mtima anavala zodziteteza mnthupi kuti asalumidwe ndi njuchizo, nkukatenga bokosi la malirowo kubwelera nalo kumudzi. Kunyumbako, mwambo woika m‘mada malemuyo unayenda bwino lomwe popanda chovuta zomwe zachititsa kuti anthu ena aganizire malemuyo kuti anali wokhwima.

22
July

AKUMBUKIRA BANJA LAKE LAKALE

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 765 times

Mai wina kwa gulupu Chipoyola mdera la mfumu Khonsolo mboma la Mzimba waimitsa mitu mikoko yogona chifukwa cha khalidwe lake losintha amuna ngati Malaya.  Nkhaniyi ikuyi mayiyo anali pa banja lolozeka koma masiku apitawa anamuthawa mwamunayo nkukalowelera chikhwaya china m’dera lomwelo.  Mwamuna wakeyo atatsala, naye anapeza mkazi wina ndipo banjalo limakhala bwino lomwe. Patapita nthawi, banja la mayiyo linasokonekera kwa mwamuna anamulowelerayo ndipo apa anakumbukira mwamuna wake wakaleyo.   Pamenepa anauyamba ulendo wakwa mwamuna wake oyambayo koma anaona ngati kutulo atapeza mkazi nzake kunyumbako.  Mayiyo akuti ataona nzakeyo anachita ngati wapenga chifukwa anayamba kuphwanya zinthu pakhomopo ndipo kenaka ndeu inayambika pakati pa amayi awiriwo.  Pa ndeuyo mwini khomolo amachepera mphamvu ndipo apa sanachitire mwina koma kunyanyala banjalo.  Atakasinkhasinkha kwawo, ananyamuka ulendo kwa mwamuna wakeyo komwe anagofikira kuchita nkhondo ndi mkazi nzakeyo.  Chodabwitsa nchoti mwamunayo anayamba kuyikira kumbuyo mkazi wake oyamba anamuthawayo ndipo izi zinadabwitsa anthu ambili.  Pakadali pano mayiyo wabweleranso kwawo koma nzokaikitsa ngati mkazi anamuthawa mwamunayo akhazikike ku banjako.

10
June

AMUGWIRA AKUBA MITENGO

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 2036 times

Njonda ina mdera la mfumu Mlumbe mboma la Zomba ikapitiliza ndi khalidwe lake losazichepetsa aisamutsa mderalo chifukwa cha zomwe yachita. Nkhaniyi ikuti mderalo kuli banja lina lomwe liri ndi nkhalango yawo yapa khomo zomwe ambiri akhala akusilira chifukwa imawathandiza nzambiri. Koma njondayo pa tsiku lina lopemphera itazindikira kuti pamudzipo pali ziii kusonyeza kuti onse akhamukira kopemphera ndipo inayamba kudula mitengo. Koma mphuno salota mwini wake anangokhala duuu osamujejemetsa ndipo ali mkati anangomva pakhosi…. Koma inu mkulu analupmpha ngati kanthete koma zinali zambuyo mwa alendo pomwe anamuuza kuti inu auje ndakuonana ingobwerelani. Njondayo yomwe njaulemu wake inayankha pansi-pansi amvekere tingokambirana zomwe sizinamveke mpakana anamukokera ku bwalo. Komabe pazifukwa zina akufuna kuusamutsira mlanduwo ku bwali lina chifukwa cha khalidwe losadzichepetsa la mkulu-yo. Pomwe mukumvera, mkuluyo ngati sazitenga bwino amusamutsa mderalo potengera kuti iye amene mdindo kumatsogolera umbava. Nkhaniyi yamuipitsira mbiri ananjomba chifukwa ambiri akhumudwa naye potengera kuti nkhalangoyo imathandiza banjalo pazinthu zosiyana-siyana monga nkhuni, mphweya wabwino ngakhalenso kupeza milimo. Mkuluyo akukhalira kupupira madzera mphuno chifukwa zikumuvuta kudziwa kuti mlandu wake utha bwanji.

10
June

AMUGWIRA AKUBA MITENGO

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 1681 times

Page 4 of 155

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter