You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma
10
June

AMUGWIRA AKUBA MITENGO

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 368 times

Njonda ina mdera la mfumu Mlumbe mboma la Zomba ikapitiliza ndi khalidwe lake losazichepetsa aisamutsa mderalo chifukwa cha zomwe yachita. Nkhaniyi ikuti mderalo kuli banja lina lomwe liri ndi nkhalango yawo yapa khomo zomwe ambiri akhala akusilira chifukwa imawathandiza nzambiri. Koma njondayo pa tsiku lina lopemphera itazindikira kuti pamudzipo pali ziii kusonyeza kuti onse akhamukira kopemphera ndipo inayamba kudula mitengo. Koma mphuno salota mwini wake anangokhala duuu osamujejemetsa ndipo ali mkati anangomva pakhosi…. Koma inu mkulu analupmpha ngati kanthete koma zinali zambuyo mwa alendo pomwe anamuuza kuti inu auje ndakuonana ingobwerelani. Njondayo yomwe njaulemu wake inayankha pansi-pansi amvekere tingokambirana zomwe sizinamveke mpakana anamukokera ku bwalo. Komabe pazifukwa zina akufuna kuusamutsira mlanduwo ku bwali lina chifukwa cha khalidwe losadzichepetsa la mkulu-yo. Pomwe mukumvera, mkuluyo ngati sazitenga bwino amusamutsa mderalo potengera kuti iye amene mdindo kumatsogolera umbava. Nkhaniyi yamuipitsira mbiri ananjomba chifukwa ambiri akhumudwa naye potengera kuti nkhalangoyo imathandiza banjalo pazinthu zosiyana-siyana monga nkhuni, mphweya wabwino ngakhalenso kupeza milimo. Mkuluyo akukhalira kupupira madzera mphuno chifukwa zikumuvuta kudziwa kuti mlandu wake utha bwanji.

10
June

AMUGWIRA AKUBA MITENGO

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 390 times

22
May

18/05/19

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 556 times

Mtsikana wina kwa M’biza m’boma la Zomba amuthidzimula moleketsa kaamba kaukazitape. Nkhaniyi yati mtsikanayi yemwe ali n’chizolowezi choyambanitsa anthu anapita kwa mayi wina mmudzi mwawomo n’kukamuuza kuti waona mwamuna wa mayiyo akupatsa ndalama mtsikana wina osakwatiwa wammudzi momomwe. Poti amamudziwa bwino zakhalidwe lake,mwini mwamuna uja sanatekeseke koma kumvetsera mwachidwi chabodza poti mwamuna wokambidwayo n’kuti atapita mu mzinda wina wakutali kwambiri kukagwira ntchito.Atamaliza kufotokoza nkhani yopekayo mtsikana uja anadabwa kuti mwini mwamunayo sakufunsa komwe angapeze anthu onamiziridwawa koma m’malo mwake anazungulira kuseri n’kukaitana aneba ake.Aneba aja atafika, mtsikana wamlomo wopotokayo anayambanso kuyala nkhani ija ndipo izi zinakwiitsa kwambiri mwini mwamuna uja yemwe sanachedwe koma kumdululuza kwinaku mateche akuvumba. Pamenepa, naye neba uja anathyola chindodo n’kumuthyapula nacho zomwe akuti zinachititsa mtsikana wosokoneza uja kuwataya mawu ngati khanda lofuna kuyamwa,kwinaku akupepesa kuti amangofuna kusereula.Padakali pano mtsikanayo akuyenda zyoli zyoli ngati mwanapiye onyowa.

22
May

18/05/19

Written by
Published in Nkhani Zam'maboma
Read 468 times

Page 1 of 151

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter