You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma31/08/18

31/08/18

Written by  Newsroom

Mikoko yogona komanso anthu wothandiza pa ntchito zachitetezo pa mudzi wa Mambo kwa Jenala m’boma la Phalombe akufuna-funa amuna ena anai omwe avulala mlimi wina wa nzimbe.

31
August

Watitumizira nkhaniyi wati mlimiyo ali ndi dimba la nzimbe lokula pafupi-fupi mahekita awiri. Anthu ena a manja mbwee!!! Akhala akuwendelera ndikumakaba nzimbezo. Mwini dimbalo naye wakhala   akutandala kumeneko kuyambira m’bandakucha kuti athane ndi anthu     woipawo. Mbandakucha wa tsiku lina mbava zinai zomwe   zinali ndi zida zoopsya kuphatikizapo zikwanje ndi nthungo zinalawilira kufuna kuti zikabe nzimbe m’dimba la mlimiyo. M’modzi mwa mbavazo italowa m’dimbamo sinachedwe koma inayamba kusenga nzimbezo pamene anzake amasadzula nkumamanga mitolo. Pa nthawiyo mwini dimbalo n’kuti akuwendelera wakubayo. Koma akanadziwa mwini dimbalo sakanayerekeza kuwendelera akubawo koma akanangokuwa kuitana anthu kuti amuthandize kugwira akubawo. Koma mlimiyo atayandikira wakubayo anafuna kuti amugwire koma wakubayo analumpha ndikugwaza mlimiyo ndi chikwanje pa dzanja. Kotero kuti mlimiyo anagwa pansi magazi akuthoboka monga akuchokera   pa mpope. Pa nthawi yomwe mlimiyo anali gada pansi nkuti akufuula kuitana anthu kuti amuthandize kugwira anthu akubawo. Koma mwa tsoka anthuwo anafika pa dimbapo akubawo atatha mtunda ndi mitolo ya nzimbe yomweyo. Pakadalipano mlimiyo akubuula mchipatala china momwe amugoneka m’bomalo.

 

Amai ena anai apa mudzi wa Likoloma kwa Kaphuka m’boma la Dedza   akulilira ku utsi sing’anga wina wa mankhwala a zitsamba atawagwilira komanso kuwabera mafoni awo a m’manja. Watitumizira nkhaniyi wati mwa amaiwo awiri amagulitsa mandasi komanso ali pa banja pamene ena awiriwo ndi mbeta ndipo sachita geni iriyonse. Amai anaiwo anakapezelerana kwa sing’angayo komwe aliyense wa iwo amakafunsa mtera. Amai awiri omwe amagulitsa mandasi amafuna mankhwala a zitsamba kuti bizinesi yawo iziyenda bwino komanso kuteteza ndalama zawo kwa achitaka. Pamene ena awiriwo omwe ndi mbeta amafuna mankhwala woti apeze amuna womanga nawo banja. Pamane sing’angayo amaitanitsa m’modzi-m’modzi nkumalowa naye nkachisimba kake pomwe amabwatika amaiwo kuti mankhwala ake agwire bwino ntchito nkofunika kuti akhale nawo malo amodzi zomwe amaiwo amavomereza osakana pofuna mankhwala. Ndipo pomaliza sing’angayo anauza amai anaiwo kuti asiye mafoni awo a m’manja ndipo adzawatenga tsiku lotsatira kuti akafotokozere sing’angayo paza umboni wawo. Pofotokozera m’nazake naye, m’modzi mwa amaiwo wanenetsa kuti pamene sing’angayo amamufotokozera nkhaniyi yoti akhale malo amodzi amangovomera monga   mbuzi yomangidwa pa chingwe, iye anapitiriza kuti akukhulupilira zonsezi zimachitika chifukwa sing’angayo anawachitira mtera kuti asakane. Pamene amapita kwa sing’angayo tsiku lotsatira anapeza sing’angayo atasamuka ndipo komwe walowera sikukudziwika. Pakadalipano amaiwo akulilira ku utsi kamba ka nkhani yochititsa manyaziyi.               

 

Eni mbumba pa mudzi wa Jeremiya kwa Mwase m’boma la Kasungu akuyang’anizana ndi diso la   nkhwezule   ndi mkamwini wina pa mudzipo. Watitumizira nkhaniyi wati mkamwiniyo ngakhale akukhala ku chikamwini koma ndi wa nsanje ya moto. Tsiku lina mkamwiniyo akuchokera koupopa mowa anapeza mkazi wake pakhomopo palibe. Ndipo atafunsa anthu woyandikana nawo nyumba nawo anati sakudziwa komwe walowera mkazi wake. Apo mkammwiniyo anayamba kufuna-funa mkazi wake mpaka ku chimbudzi koma sanampeze. Posakhalitsa mkaziyo anatulukira pakhomopo matsatsa a nkhuni ali ku manja. Koma mwamunayo atamfunsa mkazi wake sanakhulupilire zomwe anayankhazo kotero kuti anapulumutsa chibakera chomwe mkaziyo anachizinda ndipo chinafikira m’mutu mwa mwana yemwe mkaziyo anamureka kumbuyo. Khandalo linagwa kuchokera ku msana wa mai ake mpaka pansi ndu!!   kukomoka kunali komweko. Anthu ena achifundo ndiwo anatengezana khandalo ulendo waku chipatala china m’bomalo komwe likulandira thandizo la mankhwala. Ndipo eni mbumba anenetsa kuti ngati khandalo silichira mkamwiniyo aona chomwe   chidameta nkhanga mpala.    

 

Amuna awiri apa mudzi wa Lusinje kwa Tsikulamowa m’boma la Ntcheu   awamangilira ku mtengo kamba ka ngongole ya maveta a kachasu asanu. Watitumizira nkhaniyi wati amuna awiriwo omwe ndi mbiyang’ambe anatengana kukapapira mowa ku banja lina pa mudzipo. Mai yemwe amagulitsa kachasuyo sanawakaikire amunawo chifukwa chakuti ndi   makasitomala a nthawi zonse. Ndipo pamene amaitanitsa mavelemoti mpaka kufika asanu ndi pamene mmwini mowayo anaitanitsa   ndalama zake. Koma amuna awiriwo analephera kulipira ngongoleyo kotero kuti akawafunsa amayankha mbwelera zokha-zokha. Chifukwa cha zimenezi mwini mowayo anauza anyamata a dzitho omwe anagwira zidakwa ziwirizo ndikuzimangilira ku mtengo komanso kuzipaka mafuta a nkhumba. Uthenga unakafika kwa achibale a amuna awiriwo kuti awaombole. Tikunena pano achibalewo ali wempha-wempha kufuna-funa ngongole ya ndalama zokwana mavelemoti asanu kuti awombole abale awo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter