You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma05/07/18

05/07/18

Written by  Newsroom

Anthu a m’mudzi wina mdera la mfumu Tambala m’boma la Dedza akukhalira kuseka mai wina yemwe anabaya mwamuna wake ndi CHIUZIRA - kapena kunena kuti chitsulo chomwe amabowolera mpini wa khasu chifukwa choledzera.

05
July

Usiku wapa 31 December, maiyo anakapapira bibida kuti asangalale akamalowa chaka chatsopano. Anathipwadwi ndi mowawo ndipo chisangalalochi chitasefukira, anatenga chitsulo chomwe amabowolera mipini ya khasu mkumuuzakuti mwamuna wake kuti amva naye madzi. Mwamunayo anaganiza zoti mkaziyo akuselewula koma anadzidzimuka atamubaya ndi chitsulocho. Mwamuna-yo anagwa kwinaku akukuwa chifukwa cha ululu kotero kuti m’mene anthuy amafika anapeza magaszi akuyenderera. Mwansanga anthu anathamanga naye ku polisi komwe anakatenga kalata yaku chipatala. Patatha masiku angapo anatuluka ku chipatalacho. Anthu anayembekezera kuti mwina mwamunayo alongeza klatundu wake nkluwona msana wa njira. Koma m’malo mwake, anapita ku polisi kukaseketsa nkhaniyi kuti palibe mulandu izo ndi za m’banja. Panopa, anthuwo akukhala mosangalala.

 

Akhristu a mpingo wina m’boma la Zomba asiya kupita ku kachisi pokwiya ndi bodza la mbusa amene anayambitsa mpingo-wu. Asanayambitse mpingowu, ankanamizira kuti ali ndi gulu losamalira ana amasiye kotero kuti wakhala akulandira thandizo kuchokera ku mabungwe ndi kwa anthu akufuna kwabwino lothandizira ana amasiye-wo. Koma iye amangothyolera mthumba. Atadziwa zoti anthu amutulukira, anayambitsa mpingo ndipo unali ndi chikoka malinga nkuti amauza akhristu makamaka ovutika ndi achikulire kuti adzilandira ndalama zoti zidzikawathandiza ku nyumba kwao. Poganiza kuti adzilandira kenakake akapita ku kachisiko, anthu amapiota mwamkokomo. Koma akhristu ena akamufunsa, mbusayo samayankha zolongosoka. akhristuwo atatulukira zoti mbusayo ndi tambwali, m’modzi ndi m’modzi anayamba kudula phazi ku kachisiko kotero kuti m’mene timalandira nkhaniyi, nkuti atangosalako achibale okha a mbusayo.


Bambo wina m’mudzi wina kwa Msakambewa m’boma la Dowa wathetsa banja la mwana wake wa mkazi, bambo-yo atagulitsa nkhuma ya mkamwini-yo. Nkhaniyi ikuti, mwamunayo yemwe amakhala ndi mkjazi wake mdera lina anagula nkhumba nkukasungitsa kwa apongozi ake. Bamboyo anailandira ndi manja awiri ndipo amaisamalira. Koma nkhumbayo itakula bamboyo anaigulitsa. Mphepo yoti apongozi ake agulitsa nkhumba yake inamupeza mkamwiniyo ndipo atapita kukafunsa, anamuuzadi kuti anagulitsa chifukwa anasowa ndalama zoti ziwathandize. Sanamvane chichewa ndipo anachoka chonyanyala. Pasanathe masiku, mkamwiniyo anadzidzimuka mkazi wake akumuuza kuti akupita kwao ndipo banja latha. Mkaziyo analongeza katundu wake nkumapita kwao. Anthu anakhumudwa ndi zimenezi. Koma chomwe anthuwo akhumudwa nacho kwambiri ndi choti bamboyo amupezerera m’munda wa chimanga akuchita za dama ndi mwana wake wa mkazi amene anamuchotsa ku banja-ko.

 

Njonda ina yaku Blantyre yomwe inakapeza malo m’dera la mfumu Mphuka m’boma la Thyolo yaimikia manja m’mwamba kuti wawalephera malo-wo ndipo akukonza zobwerera ku Blantyre. Nkhaniyi ikuti, kwa zaka zingapo, mkuluyu wakhala akukolola chakudya chochuluka kuposa minda yonse yomwe yayandikana ndi munda wa mkuluyu. Masiku apitawa, aganyu ena amene anakalima m’mundamo anasiya makasu awo m’mundamo pothawa njoka ya Nsato yomwe inalowa m’mundamo. Tsiku lina mkulu wina yemwenso anakalima ganyu anakumanizana nayo ndipo analimbana ndi Nsatoyo mpaka anaipha. Anthu ali bibibi kudzayiopna, anadabwa mwini mundawo akubwera ali wefuwefu thukuta liri kuno, akudandaula kuti anthu ena amuchita chipongwe chachikulu. Atamufunsa sanafotokoze momveka bwino za chipongwe chomwe amati anthu ena amuchita, koma anangouza anthuwo kuti asadandaule njokayo ayikwira yekha m’mundamo akhoza kumapita. Panopa, mkuluyo akuyenda ngati wodwala ndipo akunka nauza anthu kuti akukonza zobwerera ku Blantyre.

 

Anthu a m’mudzi wina ku Shire North m’dera la mfumu Mkaya m’boma la Balaka akulozaloza chala mai wina yemwe akusintha amuna ngati chovala. Maiyo ali pabanja ndi mwamuna yemwe wabwereka naye ana asanu. Koma wawirikika kuchita za dama ndi amuna wosiyanasiyana kuphatikizapo achichepere osagwirizana ndi msinkhu wakle. Miezi yapitayi anagonekera maso mnyamata wina osakwana zaka makumi awiri mpaka anamukopa nkuyamba kuchita naye zadama. Amai ena achikulire, anamuitana nkumulangiza kuti zomwe akuchitazo akudzichotsera ulemu. Koma maiyo anangozikankhira ku nkhongo. Panopa, maiyo watengeka ndi mkulu wina kotero kuti sakugwirika. Panopa, sizikudziwika ngati banjalo likhale mwamuna wa maiyo akazimva nkhani-yi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter