You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma03/07/18

03/07/18

Written by  Newsroom

Anthu a m’mudzi wina ku Dwangwa m’boma la Nkhotakota akhumudwa ndi zomwe yachita njonda ina yapa banja polola mzake kukasangalala ndi chibwenzi chake mnyumba mwake mkazi wake atapita ku msika.

03
July

Mzake wa njondayo anabwera ndi chibwenzi chake koma anasowa koti akasangalale naye. Atamufotokozera za nkhani-yi, bamboyo anauza mzakeyo kuti agwiritse ntchito nyumbayo malinga nkuti mkazi wake wapita ku msika. Anthuwo analowa mnyumbapo. Koma posakhalitsa, mkaziyo anatulukira kuchokera ku msikako koma bamboyo anauza mkaziyo kuti asalowe msanga mnyumbamo muli mzake akucheza ndi chibwenzi chake. Mkazi sanasangalale ndi zimenezi ndipo mkangano unabuka panja pa nyumba-yo. Anthu atafika nkumva chomwe chinabutsa mkanganowu, sanachedwe koma kutsekula mnyumbamo ndipo anaduduluzira kunja mwamuna ndi mkaziyo nkuyamba kuwawoweoza. Anyamata ena a kabanza omwe anafika pamalopo ndi amene anathawitsa anthuwo pa malopo kusiya anthu akuphaphalitsa mafunso mwino nyumbayo pa zomwe anachitazo.


Mkazi wa m’mudzi wina mdera la mfumu Nkaya m’boma la Balaka akunong’onedza bombono chifukwa chophwasula banja ndi manja ake. Nkhaniyi ikuti mkaziyo akapeza ndalama amamuswaya mwamunayo. Izi zakhala zikuchitika kangapo ndipo ndalamazo zikatha mkaziyo amakagwira mwendo kwa mwamunayo yemwe samaumira koma kukululukira mkazi wakeyo. Mwa nthawi zonse atalandira ndalama za mtukula pakhomo , maiyo analalatira mwamuna wake akumati angokhala phwi pakhomo osatakataka. Njondayo, inamanga katundu wake nkumapita kwao. Ndalamazo zitatha anapita kwa mwamuna wakeyo kukagwira mwendo. Koma njondayo inatemetsa nkhwangwa pa mwala kuyti sangayereke kubwererana naye, akayese kwina. Mkaziyo walephera kumunyengerera mwamunayo ndipo panopa, maiu-yo wadziwa kuti madzi achita katondo ndipo akusowa mtengo wogwira ndipo amuna a mderalo sakumulabadiranso.


Anthu a m’mudzi mwa Muluma mdera la mfumu Nkaya m’boma la Balaka anakhamukira ku khomo la mkulu wina kukawona nsato yomwe anaipha usiku m’mudzimo. Yemwe watumiza nkhaniyi wati, usikuwo kunali chinam’balala cha anthu m’mudzi-mo anthu atadziwa zoti mwalowa Nsato. Amuna olimba mtima anayamba kuitsaka njonkayo ndipo atawona komwe inali, amnayesa kulimbana nayo koma inalusa kwambiri. Kenaka, anayiwona ikulowa mkhola la nkhuku la mkulu wina. Anthuwo anayesa klulimbana nayo koma mpaka anakaitana mkulu wina yemwe ali ndi mufti. Atafika, anayamba kugenda mkhola-mo kuti ituluke ndipo izi zinachitikadi. Itangotuluka pafupifupi theka, wa mfutiyo anayiwombera ndipo ndipo inatenga mphindi zingapop ikuthatha mpaka inafa. Mwini kholayo atawerenga nkhuku zake, anapeza zoti Nsatoyo yadya nkhuku zinai. Kutacha, anthu anakhamukira ku khomoko kukawona chirombocho ndipo atayiyeza kutalika kwake anapeza zoti inali yotalika mamita anai.

 

Mai wina wapabanja komanso waulemu wake yemwe akukhala kuchitengwa m’mudzi wina mdera la mfumu Likoswe m’boma la Chiradzulu wapezeka akuchita za dama ndi mnyamata wamng’ono ku manda ena m’deralo. Mkulu wina yemwe ankayendera munda wake omwe wachita malire ndi mandawo anamva kuyankhula pa tchire la mandawo. Atasuzumira, anawona mwamuna ndi mkazi ali pa chikondi. Mkuluyo anawednderera ndipo atafika pafupi, anatsokomola. Mwamuna ndi mkaziyo anadzuka pamene anagonapo nkuyamba kuthawa kusiya zovala zao. Mwatsoka, komwe analunjika kunali ku msewu ndipo anangoti gulululu ndi anthu omwe amadutsa mu msewuwo. Anthu awiriwo sanaime koma kulowa mchimanga ndipo sanawonekenso. M’mene timalandira nkhaniyi, nkuti mayiyo akubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi.


Mikoko yogona mdeera la mfumu Mtwalo m’boma la Mzimba yati ikudabwa ndi zomwe akuchita mnyamata wina pomayenda ndi mafupa a nyama ya ng’ombe mchikwama mwake. Yemwe watitumizira nkhaniyi wati anthu akudabwa ndi anyamata ena awiri omwe akugwira ntchito mderalo koma kwao ndi kwa mfumu Changata m’boma la Thyolo. Chomwe chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke nyanga ndi choti tsiku lina bwana wapa kampani-yo anapeleka nyama kwa aliyense wapa kampanipo ngati mphatso powayamikira kuti akudzipereka pantchito. Koma m’modzi mwa anyamatawo akudabwitsa amzake kuti ikafika nthawi ya m’memo, amawiritsa mafupa a nyama ya ngombe yomwe analandira nkusanula msuzi nkumadyuera msimayo. Anthu ena akuganiza kuti mafupawo akumawagwiritsa ntchito m’masenga ndipo anzake onse pa kampanipo akumusala kamba koti akumuganizira kuti ndi amene akuchita za masenga pakampanipo pomwe akuti anthu azidwala-dwala. Panopa, anthu ena awopseza kuti athana ndi mnyamatayo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter