You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma30/03/18

30/03/18

Written by  Newsroom

Chipwirikiti chinabuka pakati pa amai ena a gulu la banki nkhonde ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre.

30
March

Nkhaniyi ikuti mamembalawo amasungitsa ndalama zawo m’mabukhu awiri, omwe pamapeto pake amayenera kugawana zomwe amasungitsazo kuphatikizapo chiongoladzanja. Tsono chomwe chinachitika patsikuli nchakuti gululo linayamba kugawana ndalama za mbukhu laling’ono la Kalinda koma ena sanakhutire ndi chiongoladzanja chake. Pamenepa ena mwa amayiwo anapempha kuti asanayambe kuwerengera ndalama za mbukhu lalikululo, ayambe awerengeranso bukhu laling’onolo pokaikira kuti pachitika ukapsyali pa ndalama zawozo. Izi zinadzetsa kusamvana pakati pawo mpaka kuyamba kutosana zala. Mkanganowo unakula mpaka amayiwo kuyamba kumenyana ndipo analephera kugawana ndalamazo. Pakadali pano sizikudziwika ngati anagawana ndalamazo koma amayi omwe anayambitsa mkanganowo akuyenda mwa manyazi chifukwa cha nkhaniyi.


Mwamuna wina wa m’mudzi mwa Kalonga kwa Mfumu Mponda mboma la Mangochi amulamula kuti apereke chindapusa cha 250 thousand kwacha chifukwa chofalitsa pa makina a internet kanema olaula wa mai wina. Chomwe chinachitika nchoti mwamunayo anauza mai wina kuti amubweleke phone ya mmanja. Koma mmalo mogwilitsa ntchito yomwe anabwelekela phone-yo, anayamba kuona zithunzi mpaka anapeza kanema olaula wa mai-yo ndipo iye anatumiza zithunzi-zo mu phone mwake. Kenaka mwamunayo akuti anakakamiza mai-yo kuti amupatse 200 thousand kwacha pomuoyseza kuti akapanda kupereka ndalama-yo afalitsa kanema-yo. Mai-yo akuti anakana kupereka ndalama-yo ndipo m’malo mwake anakatula nkhani-yi ku polisi. Mlandu utalowa m’khothi ku Zomba, Mkuluyo anavomera ndipo khothilo lalamula kuti apereke chindapusa cha 250 thousand kwacha apo bii akakhala ku ndende chaka chathunthu. Pakadali pano mkuluyo wapereka chidapusa-cho ndipo mwa ndalama-yo khothi lapereka 200 thousand kwacha yomwe amafuna kwa mai-yo.


Kwa Mponda komweko, imfa ya mtsikana wina yaziziritsa anthu nkhongono. Nkhaniyi ikuti mtsikanayo anapita ku mjigo kukatunga madzi komwe anakapezako atsikana ena atatu. Panthawiyi nkuti mitambo ikusonyeza kuti kugwa mvula komabe poti mjigowo uli pafupi anapitabe kumadziko. Mwadzidzidzi mphenzi inamuomba mtsikanayo ndipo atathamangira naye ku chipatala anakawauza kuti wamwalira kale. Anthuwo atakafika kumudzi ndi zachisonizo, mayi wina anagwa majini nkumauza anthu kuti apite pa mjigopo pali chithumwa ndi bango zakuda. Pokhulupilira kuti mwina izi zachitika m’matsenga, anthuwo anathamangiradi ku mjigoko koma sanapeze kanthu. Pakadali pano mudziwo udakali ndi mantha makamaka chifukwa choti ati thupi la malemuyo limatuluka thukuta.


Mkamwini wina m’dera la Mfumu Mwase mboma la Kasungu wachimina atamusema ndi chikwanje ku nkhope. Mkamwiniyo akuti ndi khalidwe lake lotsekulira akazi a eni m’nyumba. Mwachizolowezi, dzana mkuluyo anapita pa nyumba ina poganiza kuti mwamuna wa mkaziyo kulibe. Atalowa m’nyumbamo, akuti anafikira kuthimitsa babu ngati ndi m’nyumba mwake. Koma poti mphuno salota, mwamuna wa mayiyo anangotenga chikwanje nkusenga nacho mkuluyo ku nkhope. Mkuluyo anatuluka chothawa m’nyumbamo magazi ali chuchuchu. Pakadali pano anthu akungomuseka mkuluyo moti akumayenda njira zamadulira chifukwa cha manyazi.


Mai wina anachoka mwa manyazi pa maliro a mkazi nzake ku Limbe mboma la Salima. Nkhaniyi ikuti mwamuna wa amayiwo anali pa mitala. Mwatsoka mkazi wamkulu anayamba kudwala mosadziwika bwino ndipo matenda atakula anamwalira. Mkazi wam’ngonoyo atamva za imfayi anapita ku maliroko kuti akamuthunzitse mtima mwamuna wake. Ku nyumba ya siwayo mayiyo akuti anakakuta nawo mtembowo ngati namfedwa wamkulu koma izi sizinasangalatse abale a malemuyo. Posakhalitsa achibalewo anayamba kunyoza mkazi wamng’onoyo ndipo kenaka anamuunjilira kuti ayambe kumukuntha. Mwa mwayi amai ena a dzitho anakwanitsa kuthawitsa mayi nzawoyo mpaka sanabwelerenso pa maliropo. Achibalewo ati akukhulupilira kuti mkazi wamng’onoyo akudziwapo kanthu paza imfayo.


Mikoko yogona ya m’mudzi wina kwa Ngokwe mboma la Machinga yati iyitanira mkanyumba komata ana ena omwe akhala akulilira mtengo omwe anthu ena agwetsa m’mudzimo. Nkhaniyi ikuti mwezi wathau amuna ena anagwetsa mtengo wa bluegum pa nyumba ina ncholinga choti apale matabwa. Koma atagwetsa mtengowo, ana ena anayamba kulira ngati kwagwa maliro podzudzula amuna omwe anagwetsa mtengowo. Patapita masiku, amunawo anayamba kuti azicheka matabwa koma akucheka thabwa loyamba, anasiyira pa njira mtengowo utayamba kuchucha magazi. Patha mwezi wathunthu tsopano mtengowo uli chigonere ndipo panopa akuti wauma. Tsono naye mayi wina malinga nkusowa kwa nkhuni, anapitanso pamalopo kuti akachotse makungwa. Koma mayiyo anachoka chothawa ataona kuti mtengowo ukuchuchabe magazi. Apatu mayiyo anakatula nkhaniyi kwa akuluakulu a m’mudzimo moti panopa akukonza zoitanitsa anawo ku bwalo, kuti akafotokoze bwino za mtengowo.Zomwe wachita mkulu wina mboma la Chikwawa zaziziritsa anthu nkhongono. Mkuluyo yemwe akuti ndiwa zaka makumi awiri wagwilila mwana wa mkazi wa zaka zisanu. Yemwe watitumizira nkhaniyi wati mkuluyo anatengela mwana-yo ku tchile lina komwe anakamugwilila. Nkhaniyi yaululika pamene bambo a mwana-yo amafuna funa mwana-yo ndipo anthu ena anawadziwitsa kuti aona mkuluyo atamutenga. Kenaka akuti anangoti naye gululu akutuluka pa tchilepo koma mwanayo akulira. Amai ena ataunika mwana-yo anamuona ndi zizindikilo zoti wagwililidwa ndipo atapita naye ku chipatala anakatsimikizadi zimenezi. Apa anthu a m’mudzi-mo anagwira mkuluyo kupita naye ku polisi. Pakadali pano mkuluyo amutsekera mchitokosi cha apolisi podikira kukaonekela ku khothi posachedwapa pa mlandu ogwilila.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter