You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma29/03/18

29/03/18

Written by  Newsroom

Mnyamata wina ku Likuni m’boma la Lilongwe manja ali ku nkhongo mtsikana wina atamukwangwanula ndalama zake.

28
March

Chomwe chachitika mchoti mnyamatayo amagwira ntchito ku kampani ina yoweta nkhuku mdera lina m’bomalo. Kamba koti mnyamatayo samawugwira mtima akaona siketi pa khomo pomwe amachita Renti anawandikana ndi mtsikana wina oyendayenda . Anthu awiriwa anagwa mchikondi mpaka mwamunayo kumamusiyila makiyi a mnyumba mtsikanayo kuti amusamalire mnyumba mwake ngati kumukolopela ndi zina. Mwachizolowezi mtsikana atamusiyila makiyi , iye anafutukula m’bukhu lina ndikutenga ndalama zokwana 50-Thousand mkuseka mnyumbamo ndikusungitsa makiyiwo mnyumba inanso yowandikana. Mnyamatayo atafika mkufunsa komwe kunali mtsikanayo anthu anamuuza kuti wangosiya makiyi koma komwe walowera sikukuziwika. Mnyamatayo atatsegula mnyumba anapeza kuti ndalama zonse zapita. Apa mnyamatayo analiera ngati wawonekeredwa maliro ndipo atayetse kumuyimbila mtsikanayo fgoni yake suyumagwira. Pakadali pano mnyamatayo akungokhalira kuyendayenda mu mzinda wa Lilongwe ati kuyesa kuti mwina angakomane ndi mtsikanayo , koma anthu ena akuganiza kuti mtsikanayo wabwerela kwawo ku Karonga.

 


Mwambo wa maliro unasokonekera ku mponela m’boma la Dowa m’nyamata wina atamumangilira pa mtengo kamba kochita za matsenga pamalirowo. Nkhaniyi ikuti mnyamata wina amadwala mpaka kuthipwa mpaka kumwalira. Koma pa nthawi yomwe achibale amasazikana ndi m’bale wawoyo powona khope , mnyamata wina anazambatuka mwadzidzidzi ndikuponya chithumwa m’bokosi lomwe anagona malemuyo. Anthu onse anangoti kukamwa pululu ndipo m’modzi mwa achibale ndi amene anaduduluza mnyamatayo kumutulutsa mnyumba ya siwayo. Pamenepa mnyamatayo anathamangira ku manda ndikukaponyanso chinthumwacho zomwe zinadabwitsa anzukulu omwe adamunjata ndikumumangilira pa bwalo la nyakwawa ina m’mudzimo mpaka mwambo onse kutha. Pakadali pano nyakwawawo yalamula mnyamatayo kuti alipile chindaputsa cha mbudzi ziwiri kamba kosokoneza mwambowo zomwe anati ndi makhaluidwe achilendo m’mudzimo.

 


Ku Ntcheu amzukulu anakwilira zenje la manda kamba kokwiya ndi zomwe anachita anamalira pobweresa msima ya bonya ku manda. Chomwe chachitika mchoti mkulu wina yemwe ndi mlimi anadwala ndipo anamwalira. Mwambo onse amayendetse ndi ampingo ndipo itafika nthawi anthu anapereka chakudya cha ndiwo zakhwilu kwa ampingowo ndipo anakapereka msima ya ndiwo za matemba kwa zukulu omwe amagwira ntchito kumandako. M’modzi mwa anzukuluwo anatsina khutu anzake kuti ampingo awapasa msima ya ndiwo nyama. Pamenepa anzukuluwo anakwiya ndikunenetsa kuti sapitiliza ntchitoyo ndipo m’malo mwake anangokwilila zenje la mandalo mkutenga zida zonse mkuthawa kumandako. Anthu ena ndi amene anatenga makasu ndikukafukulanso zenjelo ndipo izi zinachititsa kuti malirowo akayike motchedwa. Pakadali pano nyakwawa ya m’mudzimo yalamula gulu lonse la anzukuluwo kuti akawonekere ku bwalo la nyakwawayo ndipo sizikuziwika kuti ngati gululo lipitilire kugwira ntchito yakumandako.

 


Mkamwini wina ku Nkaya m’boma la Balaka wathawa ndipo sakuoneka atamenya mpongozi wake mpaka kukomoka kamba kokanganila mbuzi. Chomwe cha chitika mchoti mwamuna wina anamanga banja ndi mai wina ndipo wakhala ali pa banjalo kwa zaka zisanu. Zikumveka kuti mwamunayo amakonda kupapila bibida. Tsiku lina mkuluyu anafika ndi anthu ena amalonda ndikulowa mkhola la mpongozi wake ndikugwira mbuzi kuti agulitse . Koma m’mene zimachitika izi mkuti mpongozi wakeyo akuchokera ku munda ndipo atamufunsa kuti afotokoze chifukwa chomwe amagulitsira mbuziyo , mkamwiniyo anagwira mpongozi wakeyo ndikumumenya modetsa nkhawa mpaka kukomoka . Mkamwiniyo ataona kuti madzi achita katondo anangothawa mpaka pano sakuwoneka komwe alowera.l Pakadali pano anthu okwiya atchetcha chimanga chake m’munda onse cha mkamwiniyo.lMnyamata wina kwa Chikowi m’boma la Zomba amubera njinga yakabaza ku chibwezi. Chomwe chachitika mchoti mnyamatayo anagwa mchikondi ndi mkazi wina yemwe mwamuna wake ali ku Joni. Anthu awiriwa akhala akuzemberana kwa nthawi yaitali. Tsiku lina mnyamatayo atafika pa khomo pa maiyo anabisa njinga yake ku Bafa ndikulowa mnyumbamo. Koma m’mene amachiti izi mkuti mnyamata wina akumuona ndipo anazembe ndikusolola njingayo mkuthawa. Mnyamata wakabazayo atafika m’bafamo sanapeze njingayo ndipo analira mpaka ku nyumba kwake. Atafika ku nyumba kwake ananamiza mkazi wake kuti anakoma ndi anyamata achipongwe omwe anamubera njingayo. Pakadali pano mnyamatayo akupempha aliyense yemwe anatenga njingayo kuti amubwezere ndipo adzapereka kangachepe.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter