You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma02/01/18

02/01/18

Written by  Newsroom

Anthu a mdera la Mlauli ku NENO akukhala mwa mantha chifukwa cha mzukwa wina mderalo.

01
January

Nkhaniyi ikuti munthu wina wakhala akudwala mderalo ndipo matenda atakala anamwamira. Mwambo wa zovuta unayenda bwino lomwe koma chodabwitsa anthu mderalo ati akukhalira kukomana ndi mzukwa omwe akukhulupilira kuti ndi malemuyo. Mwa zina mzukwawo ukungoyenda pa msika wa mderalo chakumadzulo zomwe ati zikusokoneza malonda a mderalo. Anthu ena komanso mikoko yogona adzudzula akubanja kwa malemuwo kuti sanafune kumva zofuna za malemuyo pa nthawi yoika m’manda thupi lake. Koma ngakhale ena akutero anthu ena ati zoona pa nkhaniyi ndi zakuti izi zikuchitika chifukwa malemuyo anali katakwe pa zitsamba. Mikoko yogona komanso anthu ena ati achitapo kanthu kuti mderalo mukhale bata.

 

Achinyamata ena anai ku Maleule kwa Kapeni m’boma la Blantyre anawamangilira pa mtengo ku manda kamba kosokoneza pa maliro. Nkhaniyi ikuti mwamuna wina amadwala ndipo matenda anafika povuta kwambili mpaka anamwalila. Koma zovetsa chisoni ndi zoti achinyamata anai apa khomopo anakapapila bibida wa mkalabongo ndikuyamba kuyimba nyimbo zosemphana ndi pa maliropo. Anthu anachita manyazi pamene a mpingo anayamba kulalikira pomwe achinyamatawo amakuwa kuti go dipa mpaka wakufayo amve. Izi zinakwiyitsa anthu pa siwapo mpaka adzukulu anagwira achinyamatawo ndikukawamangilira pa mtengo kumanda. Kenaka mwambo onse utatha anawatengera ku bwalo la anyakwawa ya m’mudzimo. Apa nyakwawayo inalamula anyamata anaiwo kuti alipile mbudzi imodzi aliyense. Anthu ambiri akhumudwa ndi khalidwe la achinyamatowo zomwe ati aka sikoyamba kuti asokoneze mwambo wa maliro ponena kuti anachita zomwezo ku ndirande mu mzinda wa Blantyre. Pakadali pano, nyakwawa ya m’mudzimo yachenjeza makolo anyamatawo kuti awakhaulitsa ngati angabwerezenso khalidwelo ndipo adzawona chomwe chidameta nkhanga mpala.

 

Agulu am’mudzi wina kwa Mpama mboma la Chiradzulu awadzudzula kwambili chifukwa cha mtima wao wadyela. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi wati masiku apitawo mkulu wina wakhala akudwala kwambili. Chifukwa chakudwala mkuluyo amalephela kupita ku mzikiti koswala ndipo mkuluyo atamwalila agulupu kumeneko anati satsekula kumanda pokha pokha anamfedwa atapereka chindapusa cha 10-thousand Kwacha komanso nkhuku ziwili. Pamenepa anamfedwa anapereka ndalama ndi nkhukuzo zomwe anthu ambili akwiya nazo mpaka afika polemba m’miyala zakhalidwe loipa la dyela la agulupu ao kumeneko. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi anthu kumeneko akulingalila zokanena nkhaniyi kwa fumu ya ndodo ya mdelalo.

 

Mikoko yogona kwa Wanama mdela la mfumu Mkanda mboma la Mulanje yaima mitu mkulu wina atagwiulila mbuzi komanso mwana wa zaka zinai. Malinga ndi amene watitumizila nkhaniyi wati mkuluyo anapezelela mbuzi ikudya nandolo mdela lina kumeneko ndipo anaimbwandila mpaka kuigwilila. Kenaka anapeza mwana wa zaka zinai pamalo ena ndipo anamugwililanso kotelo kuti mwanayo ali kuchipayala malinga nkuti wamuvulaza kwambili kumalo obisika. Malinga ndi amene atumiza nkhaniyi panopa mbuziyo yafa ndipo achitetezo m’mudzi alimbikitsa ntchito yofunafuna mkulu yemwe wachita zimenezi. Pakadali pano, anthu amdelalo ati ndi okhumudwa kwambili ndi zomwe mkuluyo wachita ponena kuti akagwidwa akuyenela kulandila chilango chokhwima.

 

Banja la mkulu wampingo wina ku Chitale kwa Senzani mboma la Ntcheu latha mkazi ataola katundu yense mwamuna wake atamugwila pathengo lina akuchita zachisembwere ndi mayi oyendayenda. Watitumizila nkhaniyi wati mdelalo muli mtsikana wina woyendayenda ndipo akumachita kulankhula mwathamo kuti chaka chake mchino akupha makwacha chifukwa cha amuna apa banja kale. Chatsitsa dzaye mchakuti tsiku lina mkulu wina wampingo anatsanzika mkazi wake kuti akupita koona odwala koma chonsecho amakakumana ndi mtsikana wachibwenzi. Anthu omwe anawaona anakatsina khutu mkazi wake komanso anthu ena achibale mpaka anapeza mkulu-yo alibuno bwamuswe ndi mkaziyo. Pa chifukwachi mkuluyo akuti anathawa pamalopo buluku lili m’manja. Panopa, mkazi wamkuluyo waola katundu wake yense wapita kwao ku Chitale mboma lomwelo la Ntcheu. Pakadali pano, nyakwawa ya m’mudzimo yauza mtsikana yemwe akusokoneza mabanja-yo kuti asamuke m’mudzimo pasadathe masiku anayi koma zamveka kuti mkaziyo akukana podziwa kuti m’mdelalo muli malonda kwambili. Panopa, mkulu wampingoyo ayamba amuimitsa kumpingo komwe akutumikila.

 

Mwamuna wina kwa Mazengera m’boma la Lilongwe akugona ku chipatala atawononga ndalama zonse zomwe anagulitsa mtedza ndikumwera bibida. Chomwe chachitika mchoti Mwamuna wina anagwilizana ndi mkazi wake kuti agulitse mtedza malinga nkuti pakhomo pao ndi pa mwana alilenji. Koma zikumveka kuti bamboyo samaupeza mtima akamva chinganga cha mowa ndipo amati akapita mwina pamatha masiku awiri kuti abwerele pa khomo. Atagulitsa matumba khumi amtedza mkuluyo anakamwela mkalabongo ndalama zonse ndipo anatandala ku mowako mpaka msiku awiri. Kenaka ataona kuti madzi achita katondo anapita ku chipatala ndikunamizila kuti akudwala kwambiri ndipo anayimbira mkazi wake foni kuti amugoneka mchipatala. Koma mkuluyu anasiya njinga yake ku mowako ndipo anzake anapita nayo ku nyumba kwakekomwe anauza mkazi wake kuti amuna ake anaiwala njingayo ku mowako kamba koti akhala akumwa mowa masiku awiri. Mkazi wake atafika ku chipatalako anapeza mkuluyu atagona pa bwalo kwala kwinaku akulila mosisima kufotokozela mkazi wake kuti akuba amukwangwanula ndalama zonse. Mkaziyo anakwiya mpaka kumenya mwamuna wakeyo ndikumududuluzila ku nyumba. Mkaziyo anangowola zovala zake ndipo wapita kwawo kutathauza kuti banja latha. Pakadali pano anthu akumuseka mkuluyu kamba kopasula banja lake ndi manja ake zomwe zachititsa kuti aziyenda wela wela ngati napiye ogwela mvuwo.

 

Mwambo wa maliro kwa Mtwalo m’boma la Mzimba unasokonezeka njuchi zitaluma anafedwa ku manda mpaka wina kukomoka. Chomwe chachitika mchoti mwamuna wina amadwala mpaka kumwalira. Mkuluyu asanmwalire ananenetsa kuti mwana wake adzatsogolere pa ulendo waku manda ndi nkhuku yoyera. Koma mkuluyo atamwalira achibalewo sanatsatire malangizowa ndipo atafika kumandako njuchi zambiri zinatuluka pa dzenje la manda ndipo chimphwirikiti chinabuka mpaka kusiya bokosi asanalikwilire. Anthu ena anakumbukira zomwe ananena malemuyo ndipo mikoko yogona inalamula kuti akagwire nkhuku yoyera ku siwako ndipo atafika anaiponya mdzenjemo. Apa njuchizo zinaziya kuvutitsako ndipo zonse zinalowa m’dzenjemo. Kamba kokumudwa ndi zimenezi ampingo anakana kupitiliza kuyendetsa mwambowo ndipo nyakwawa inangolamula kuti anthu angokwilira bokosilo popanda ampingo kuyimbila nyimbo. Pamene izi zimachitika mkuti achibale ena ali kwala njuchizo zitawaluma modetsa nkhawa. Pakadali pano anthu ambiri akuganiza kuti mkuluyu anali okhwima ndipo ku mpingoko kunali kungoiwerenga chabe.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter