You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma30/12/17

30/12/17

Written by  Newsroom

Paja pali mau oti magwiragwira amapha manja.

30
December

Nkhaniyi yapherezera mdera la Mzukuzuku ku Mzimba pamene mnyamata wina wayamba kulankhula zosamveka atakaba mtondo wapa banja lina. Mnyamatayo amachita bizinezi zosiyana-siyana mderalo ndipo pa chifukwachi Sing’anga wina anamutsimikizila kuti akapeze mtondo wa anthu ena mcholinga choti akamukonzere mankhwala kuti bizinesi zake zipite patsogolo. Masiku apitawa mnyamatayo anazembera mtondo wa banja lina usiku koma akanadziwa sakanatero chifukwa atangonyamuka kumene anayamba kulankhula zosamveka mpakana kuvula zovala zake. Anthu mderalo kuphatikizapo akubanja m’malo momvera chisoni mnyamatayo akukhalira kumuloza zala kuti ati nzofuna chifukwa mwa zina akhala akumulangiza. Mikoko yogona ati akokera ku bwalo la milandu Sing’angayo pamene anthu opemphera ati mpofunika kuti mnyamatayo akomane ndi atumiki Ambuye mcholinga choti alandile mzimu wa Mulungu.

 

Anthu aku Ligowe mdera la Mfumu Mlauli m’boma la Neno adakudabwa ndizomwe akuchita mwamuna wina polola mkazi wake kutasa ndi chibwenzi iye akuona. Nkhaniyi ikuti mwamunayo amakhala ndi mkaziyo bwinobwino osadziwa kuti akumuyenda njomba. Kenako, anthu ena anayamba kumutsina khutu mwamunayo za mayendedwe a mkazi wakeyo koma chodabwitsa nchakuti samazilabadira. Apa mkaziyo akuti anafika poitanila chibwenzicho ku nyumbako ndi kumagona nacho kuchipinda. Nthawi zonse chibwenzicho chikafika, mwini mkaziyo akuti amakhala pa balaza ati popeleka mpata kuti anthu awiriwo acheze momasuka. Nkhaniyi akuti inafika poipa mkaziyo atayamba kuyankhula mwathamo kuti ali ndi pathupi pa njonda ina osati mwamuna wakeyo. Mikoko yogona komanso abale a mwini nyumbayo akamulangiza kuti amusiye mkaziyo, amayankha m’maso muli gwaa kuti sakuona chovuta china chili chonse. Pakadali pano, anthu ambiri mderalo akudzudzula mkaziyo kuti ndi oyipa ndipo kuti adampusitsa mwamuna wakeyo ndi mankhwala a chikondi kuti asamawilingule.


Mkulu wina wa mdera a la Malili ku Lilongwe anatuluka thukuta losamba pa maso pa mkazi wake. Nkhaniyi ikuti mwamunayo yemwe saphetira akaona njole anapalana ubwenzi wa ntseli ndi mai wina osakwatiwa. Mphuno salota tsiku lina mwamunayo anapita kunyumba kwa chibwenzi chakecho mwadzidzi jumbo ya zinthu iri manja koma anaona ngati kutulo atakapeza mphongo ina kuchipinda kwa mkaziyo atakolekerana miyendo. Apa mwamunayo sanaimve koma kuyamba kulongozana ndi mzakeyo koma akanadziwa sakanatero chifukwa mkaziyo mogwirizana ndi mphongoyo anayamba kuzazila mwamunayo uku akumuthamangitsa ngati galu. Apa mwamunayo anachoka pakhomopo atanyowa ngakhale anafunsa mkaziyo kuti mchifukwa ninji akumuchita chipongwe? Njira yonse mwamunayo amadzilankhulira yekha ngati wamisala mpakana kukafika kunyumba. Zinthu zinapitilirabe kuipa chifukwa m’malo momulandila kunyumba kwake, mkazi wa mwamunayo anayamba kumuzazila ndikumukankha mwamunayo ati pokwia kuti chikhalireni sanabweretsepo buledi pa khomopo choncho anali odabwa ndi buledi yemwe anali mjumbomo. Mwamunayo anatuluka thukuta losamba mpakana kukamwa yasa. Anthu oyandikana nawo omwe anamva kulalata kwa mkaziyo anayamba kuchemerela mkaziyo ati ponena kuti amukhaulitse mwamunayo.

 

Njonda ina ku Chingale ku Zomba yomwe imayendetsa njinga yamoto yakabaza inalira ngati mbuzi ataithidzimula mpakana thaphya. Nkhaniyi ikuti mai wina wapa banja mderalo wakhala akusokoneza mabanja a weni kuphatikizapo kukhala pa ubwenzi wa ntseri ndi njondayo. Masiku apitawa maiyo anapangana ndi mwamuna winanso wapabanja kuti akakumane kochezera pamene anthu mderalo anali ndi mwambo otentha simba. Apa maiyo anakakumana ndi njonda inayo ku ntchochi yomwe yazungulira dambwelo ndipo zinathekadi. Koma pa nthawiyo nkuti mwamuna wa maiyo akumufunafuna anthu ena atamutsina khutu kuti mkazi wake ali pa tchire ndi mwamunayo. Mwatsoka mwamuna wa maiyo anasemphana ndi mkazi wakeyo ndipo chifukwa chophwetekedwa mtima anaganiza zopita kunyumba. Mwamunayo kunyumbako m’malo mwake anapeza njonda ya njingayo nayonso ikudzafunafuna maiyo. Apa ndeu ya fumbi inabuka mpakana njondayo inathidzimulidwa mpakana kukokedwa mpakana kulira ngati mbuzi. Atadzuka analiyatsa liwiro losayang’ana mbuyo komabe anakwanitsa kukaliza njinga yakeyo yomwe anaibisa chapatali ndi pakhomopo. Mwamuna wa maiyo anayesa kuthangitsa wakabazayo kuti sizinaphule kanthu. Pakadali pano mphongo zonse ziwiri zomwe zimayenda ndi maiyo sizikupezekanso mderalo chifukwa mwamuna wa maiyo wachenjeza kuti akapeza aliyense wa iwo aona chomwe chidameta nkhanga mpala. Komabe anthu sakumvetsa chifukwa banjalo likupitilirabe.

 

Mnyamata wina ku Migowi m’boma la Phalombe waseketsa anthu a mderalo ataumilira kukhala ku chipatala ngakhale anayamba kupeza bwino pa vuto lomwe anali nalo. Mnyamatayo akhala akumulangiza kuti asiye khalidwe lake la nchuuno koma m’malo mwake wakhala akuponyera ku nkhongo malangizowo. Chifukwa chotopa ndi khalidwe la mnyamatayo mkazi wake tsiku lina anamugwira mpakana kumupanilira mphechepeche ndikuyamba kumuomba ngati ng’oma. Apa mnyamatayo zinamukoka manja mpakana kulephera kukuwa ndipo mkaziyo anapitiliza kusambitsa makofi mphongoyo mpakana kulefuka uku akulira ngati khanda. Anthu ena omwe anabwera kudzaleletsa ndeuyo anatengera mkuluyo ku chipatala ndipo patadutsa tsiku lino anayamba kupeza bwino. Koma chodabwitsa komanso choseketsa mwamunayo anakanitsitsa kutuluka mchipatalamo ati pochita manyazi ndi nkhaniyi. Pamene ena ati mwina anachita izi pochita manyazi ndi mamembala a mpingo wake chifukwa mwa zina amadzitamandila kuti ndi katakwe pa nkhani yazibagera. Ngakhale mwamunayo tsopano amutulutsa mchipatalamo akudandaula kwambiri kuti ali mu ululu owophya ndipo wanenetsa kuti wachimina.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter