You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma28/12/17

28/12/17

Written by  Newsroom

Kambelembele wina  aona zakuda pa sitolo zapa Santhe kwa mfumu yaikulu Kalolo m’boma la Lilongwe.

28
December

Nkhaniyo ikuti mderalo muli anyamatawo awiri omwe ndi alimi a fodya ndipo amapha makwacha pa ulimiwo koma alibe chiphaso chogulitsira fodya-yo ku Auction. Choncho iwo nthawi yogulitsa fodya itayamba anapempha bambo wina mderalo yemwe ali ndi chiphatso chovomelezeka ku msika wa fodya-wo kuti agulitse fodya wao pogwiritsa ntchito chiphatso chake.  Ndipo ngati zonse ziyende bwino azamulipira akagulitsa fodyayo. Ndipo atamvana anyamatawo anatumiza fodya wawoyo kudzera pa chiphatso cha mkuluyo. Koma chomwe chatsitsa dzaye kuti njovu ithoke mnyanga ndi choti ataguluitsa fodyayo mkuluyo anathawa ndi ndalama zonse zomwe anapeza pa malondawo kuphatikiza za anyamata awiri aja. Anyamatawo  anayamba kusaka-saka mkuluyo ndipo dzana Lolemba adamupeza pa sitolo zapa Santhe. Anyamatawo anafunsa mkuluyo za ndalamazo koma mkuluyo sanayankhe zomveka.  Atalephera kumvana Chichewa anthuwo anapindirana mabuluku ndipo ndewu yafumbi inabuka pakati pao mpaka kambelembeleyo kulavula mano atatu. Pakadali pano, mikoko yogona ikadali mkanyumba komata kuti awone chomwe angachite kuti athetse nkhaniyi.

 

Nkhosa yosokela isokoneza anthu pa mapemphero pa depoti ya bus m’boma la Salima. Yemwe watumiza nkhaniyi wati masiku apitawo pa depoti ya bus-po padafika munthu wa Mulungu yemwe anagawa mau a Mulungu molapisa. Aliyense anali pamalopo anaona ufumu wakumwamba ukutsika ndipo angelo a Mulungu akukhuza wina aliyense  kuphatikizapo zidakhwa zomwe zimapapira  mtonjani pafupi ndi  malowo. Apo anthu ena okhuzidwa ndi ulalikiwo anaponya limodzi limodzi kuthokoza mlalikiyo mpaka jumbo inakhuta. Koma chomwe chadabwitsa anthu omwe anali tcheru kumvera ulalikiwo ndi choti mmodzi mwa anthu olezera anayamba kugubuduka kwinaku akuziguguda pachifuwa komanso kulira chifukwa chokhuzidwa ndi uthenga womwe munthu wa Mulunguyo amagawa pamalopo.  Wolederayo atafika pafupi ndi mlalikiyo anasomphola jumbo yomwe munali ndalamazo nkuyamba kuthawa. Apo anthuwo anagwa phwete! Popeza nkhosa yotaika yalephera kupeza chipulumutso kaamba kokonda ndi phukutsi la ndalama.

 

Amai awiri akunthana kodetsa nkhawa lero kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo. Nkhaniyi ikuti lero mderalo mudali mwambo wolumbiritsa nyakwawa ina. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mmodzi mwa amaiwo wakhala akudandaula kuti mzakeyo yemwe amagwira naye ntchito limodzi ku kamapani ina mderalo ali pa ubwenzi wa mseli ndi mwanuna wake. Koma mwini mwamunayo atafunsa mwamuna wakeyo komanso mzakeyo za nkhaiyo onse anakana nkhaniyo. Koma dzana Lolemba mkaziyo wapeza uthenga wachikondi pa lamya ya mmanja ya mwamuna wakeyo omwe analembera mkaziyo. Apo mkaziyo anachotsa sim card mu lamya ya mwanuna wakeyo, mwamunayo osadziwa ndipo anaika sim card-yo mlamya yake. Atatero anayamba kulemba ma uthenga achikondi kwa mkazi mzakeyo yemwe anayamba kuyankha mauthenga achikondiwo mpaka mkazi wakubayo kuyamika chisamaliro chomwe amalandira kuchokera kwa mwamunayo chonsecho osadziwa kuti uthenga ukupita kwa mwini mwamunayo. Izi zinaswetsa mutu mwini mwamunayo yemwe anali patchuthi kuntchitoko. Mwasoka lero anangoti gululu ku mwambo wolumbilitsa nyakwawa mderalo. Apo mwini mwamunayo sanachitire mwina koma kuyamba kusambitsa mkazi mzakeyo ndi zibakera mpaka kukhadzula  mphuno yakumamzere  ya mzakeyo. Anthu ena achifundo anatengera mai-yo kuchipatala komwe amusoka mphunoyo ndipo sanathe kuonera mwambowo chifukwa cha manyazi komanso ululu wapa balapo.    

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter