You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma21/12/17

21/12/17

Written by  Newsroom

Omvera paja pali mau oti magwiragwira amapha manja. Nkhaniyi yapherezera mdera la Mzukuzuku ku Mzimba pamene mnyamata wina wayamba kulankhula zosamveka atakaba mtondo wapa banja lina.

21
December

Mnyamatayo amachita bizinezi zosiyana-siyana mderalo ndipo pa chifukwachi Sing’anga wina anamutsimikizila kuti akapeze mtondo wa anthu ena mcholinga choti akamukonzere mankhwala kuti bizinesi zake zipite patsogolo. Masiku apitawa mnyamatayo anazembera mtondo wa banja lina usiku koma akanadziwa sakanatero chifukwa atangonyamuka kumene anayamba kulankhula zosamveka mpakana kuvula zovala zake. Anthu mderalo kuphatikizapo achibale m’malo momvera chisoni mnyamatayo akukhalira kumuloza zala kuti ati nzofuna chifukwa mwa zina akhala akumulangiza. Mikoko yogona ati akokera ku bwalo la milandu Sing’angayo pamene anthu opemphera ati mpofunika kuti mnyamatayo akomane ndi atumiki Ambuye mcholinga choti alandile mzimu wa Mulungu.


Mkulu wina wa mdera la Malili ku Lilongwe anatuluka thukuta losamba pa maso pa mkazi wake. Nkhaniyi ikuti mwamunayo yemwe saphetira akaona njole anapalana ubwenzi wa ntseli ndi mai wina osakwatiwa. Mphuno salota tsiku lina mwamunayo anapita kunyumba kwa chibwenzi chakecho mwadzidzi jumbo ya zinthu iri manja koma anaona ngati kutulo atakapeza mphongo ina kuchipinda kwa mkaziyo atakolekerana miyendo. Apa mwamunayo sanaimve koma kuyamba kulongozana ndi mzakeyo koma akanadziwa sakanatero chifukwa mkaziyo mogwirizana ndi mphongoyo anayamba kuzazila mwamunayo mpaka kumuthamangitsa ngati galu. Apa mwamunayo anachoka pakhomopo atanyowa ngakhale anafunsa mkaziyo kuti mchifukwa ninji akumuchita chipongwe? Njira yonse mwamunayo amadzilankhulira yekha ngati wamisala mpakana kukafika kunyumba. Zinthu zinapitilirabe kuipa chifukwa m’malo momulandila kunyumba kwake, mkazi wa mwamunayo anayamba kumuzazila ndikumukankha mwamunayo ati pokwia kuti chikhalireni sanabweretsepo buledi pa khomopo choncho anali odabwa ndi buledi yemwe anali mjumbomo. Mwamunayo anatuluka thukuta losamba mpakana kukamwa yasa. Anthu oyandikana nawo omwe anamva kulalata kwa mkaziyo anayamba kuchemerela mkaziyo ati ponena kuti amukhaulitse mwamunayo.


Njonda ina ku Chingale ku Zomba yomwe imayendetsa njinga yamoto yakabaza inalira ngati mbuzi ataithidzimula mpakana thaphya. Nkhaniyi ikuti mai wina wapa banja mderalo wakhala akusokoneza mabanja a weni kuphatikizapo kukhala pa ubwenzi wa ntseri ndi njondayo. Masiku apitawa maiyo anapangana ndi mwamuna winanso wapabanja kuti akakumane kochezera pamene anthu mderalo anali ndi mwambo otentha simba. Apa maiyo anakakumana ndi njonda inayo ku ntchochi yomwe yazungulira dambwelo ndipo zinathekadi. Koma pa nthawiyo nkuti mwamuna wa maiyo akumufunafuna anthu ena atamutsina khutu kuti mkazi wake ali pa tchire ndi mwamunayo. Mwatsoka mwamuna wa maiyo anasemphana ndi mkazi wakeyo ndipo chifukwa chophwetekedwa mtima anaganiza zopita kunyumba. Mwamunayo kunyumbako m’malo mwake anapeza njonda ya njingayo nayonso ikudzafunafuna maiyo. Apa ndeu ya fumbi inabuka mpakana njondayo inathidzimulidwa mpakana kukodzedwa uku akulira ngati mbuzi. Atadzuka analiyatsa liwiro losayang’ana mbuyo komabe anakwanitsa kukaliza njinga yakeyo yomwe anaibisa chapatali ndi pakhomopo. Mwamuna wa maiyo anayesa kuthangitsa wakabazayo kuti sizinaphule kanthu. Pakadali pano mphongo zonse ziwiri zomwe zimayenda ndi maiyo sizikupezekanso mderalo chifukwa mwamuna wa maiyo wachenjeza kuti akapeza aliyense wa iwo aona chomwe chidameta nkhanga mpala. Komabe anthu sakumvetsa chifukwa banjalo likupitilirabe.


Tili m’boma lomwelo la Zomba Mwamuna wina mdera la Namalima wamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sakufunanso kukhala pa banja. Nkhaniyi ikuti mwamunayo anamanga oyera ndi mkazi wina wa mderalo koma pazifukwa zina anagwirizana kuti mwamunayo apeze mkazi wina. Koyambilira anthuwo amakhala bwino lomwe koma mkazi wamkuluyo anayamba kukangana ndi mzakeyo pa zifukwa zopanda pake. Akamufunsa mkazi wamkuluyo pa nkhaniyi wakhala akulankhula m’maso muli gwa kuti sakumusowa mkazi mzakeyo zomwe zakhala zikusowetsa mtendere mwamunayo. Pa chifukwachi mwamunayo zakhala zikumukoka manja chifukwa mwa zina akapita kwa mkazi wa mng’onoyo, mkazi wamkuluyo amaima pa chulu usiku onse zomwe zakhala zikusowetsa mtendere mwamunayo ndi mkazi wa ng’onoyo. Apa mwamunayo anakatula nkhaniyi ku bwalo koma m’malo momuthandiza anangomudzudzula kuti nzofuna. Pamene timalandila nkhaniyi mwamunayo ati achita china chili chonse kuti asiyane ndi akazi ake awiri onsewo ndipo wanenetsa kuti sakufunanso kukhala pa banja. Koma anthu ena amuuza kuti akanayamba kumudziwa kaye mkazi wake oyambayo asanamukwatile.

Mnyamata wina ku Migowi m’boma la Phalombe waseketsa anthu a mderalo ataumilira kukhala mchipatala ngakhale anayamba kupeza bwino pa vuto lomwe anali nalo. Mnyamatayo akhala akumulangiza kuti asiye khalidwe lake la nchuuno koma m’malo mwake wakhala akuponyera ku nkhongo malangizowo. Chifukwa chotopa ndi khalidwe la mnyamatayo mkazi wake tsiku lina anamugwira mpakana kumupanilira mphechepeche ndikuyamba kumuomba ngati ng’oma. Apa mnyamatayo zinamukoka manja mpakana kulephera kukuwa ndipo mkaziyo anapitiliza kusambitsa makofi mphongoyo mpakana kulefuka uku akulira ngati khanda. Anthu ena omwe anabwera kudzaleletsa ndeuyo anatengera mkuluyo ku chipatala ndipo patadutsa tsiku anayamba kupeza bwino. Koma chodabwitsa komanso choseketsa mwamunayo anakanitsitsa kutuluka mchipatalamo ati pochita manyazi ndi nkhaniyi. Pamene ena ati mwina anachita izi pochita manyazi ndi mamembala a mpingo wake chifukwa mwa zina amadzitamandila kuti ndi katakwe pa nkhani yazibagera. Ngakhale mwamunayo tsopano amutulutsa mchipatalamo akudandaula kwambiri kuti ali mu ululu owophya ndipo wanenetsa kuti wachimina.

 

Anthu a mdera la Mlauli ku NENO akukhala mwa mantha chifukwa cha mzukwa wina mderalo. Nkhaniyi ikuti munthu wina wakhala akudwala mderalo ndipo matenda atakala anamwamira. Mwambo wa zovuta unayenda bwino lomwe koma chodabwitsa anthu mderalo ati akukhalira kukomana ndi mzukwa omwe akukhulupilira kuti ndi malemuyo. Mwa zina mzukwawo ukungoyenda pa msika wa mderalo chakumadzulo zomwe ati zikusokoneza malonda a mderalo. Anthu ena komanso mikoko yogona adzudzula akubanja kwa malemuwo kuti sanafune kumva zofuna za malemuyo pa nthawi yoika m’manda thupi lake. Koma ngakhale ena akutero anthu ena ati zoona pa nkhaniyi ndi zakuti izi zikuchitika chifukwa malemuyo anali katakwe pa zitsamba. Mikoko yogona komanso anthu ena ati achitapo kanthu kuti mderalo mukhale bata.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter