You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma17/12/18

17/12/18

Written by  Newsroom

Mwamuna wina kwa Ganya m’boma la Ntcheu zamusokonekera mkazi wa chibwezi atamulanda foni.

17
December

Nkhaniyi ikuti mwamunayo ali pa banja ndipo zonse zimayenda bwino. Kenaka anatumiza mkazi wake ku mudzi kuti akatenge chimanga ndikukasonda matenda. Mwamunayo anadyerera maso mkazi wina woyandikana nyumba ndikumunamiza kuti banja lake latha kamba koti mkazi wake amupeza ndi mwamuna wina. Popeza mkaziyo anali woyendayenda anakomedwa mpaka kukalowa mnyumba mwa mumanayo. Mwamunayo anamuuza mkazi wachibweziyo kluti amupasa foni ngati adzilongosola kwambiri ndipo izi zinatheka. Mwadzidzidzi mkazi wake mwamunayo anafika kuzakhazikika pakhomo kuchokera kumudzi komwe anapitako. Pamenepa mkazi woyendayendayo sanawugiwre mtima koma kumuwuza mwamunayo kuti amupase foniyo apo biii awulula kwa mkazi wakeyo. Mwamunayo anapereka foniyo. Koma mkazi mwini mwamunayo anava nkhaniyi ndipo anapita kukalanda foniyo ndipo ndeu ya fumbi inabuka mpaka kung’ambilana zovala. Pakadali pano mkaziyo wapita kwawo ku Thondwe ndipo anthu ambiri akudzudzula mwamunayo kamba kosowa chikondi mpaka kutyengera mkazi wachibwezi mnyumba . Mwamunayo akuyenda zoli-zoli kamnba ka manyazi.


Abambo awili akunthana kodetsa nkhawa kwa Tambala mboma la Dedza chifukwa cholimbilana mkazi. Nkhaniyi ikuti amuna awiliwo anapita m’mudzi umodzi komwe onse anapalana ubwenzi ndi mkazi m’modzi koma osadziwa. Tsiku lina amuna onse awili analunjika kunyumba ya mayiyo ndipo wina kufika anadabwa kumva kuti muli mwamuna nzake. Tsono poona ngati iye ndiye mwini mkazi analowa mnyumbamo momwe munabuka ndeu yovuta kwambili mpaka onse kuunjikana pansi. Nyakwawa yaopsyeza kuti ikokela amuna awiliwo kubwalo omwe akutinso avulazana kwambili. Mkazi yemwe waombanitsa amunayo wati sasiyana ndi amuna onse awiliwo chifukwa onse palibe amene amachepela kaba pobwela ndi zakudya. Naonso amunawo ati samusiya mkaziyo chifukwa amakwanitsa kuwatumikila pa nkhani zakuchipinda. Pakadali pano, amuna awiliwo akuonanabe ndi diso lofiila.


Mikoko yogona kwa Wimbe m’boma la Kasungu yapukusa mitu kamba ka njoka yoopsya yomwe yapezeka mdengu lina la mphwetekere pa msika wina mderalo. Nkhaniyi ikuti anthu ambiri akhala akudandaula ndi zomwe akuchita mkulu wina yemwe akuti amalankhula mwathamo kuti anthu adzakhala ndi ndalama pa msikapo iye akazagonela mkono. Izi zinakwiyitsa anthu ambiri pa msikapo mpaka tsiku lina mnyamata wina wa hardware anamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti apondaponda kuti akapeze masamba azisamba ndi cholinga choti yemwe akuchita za chipongwezo aziwike. Tsiku lina mkuluyu anachoka kupita ku mwambo wa chiliza kwawo ku Dowa ndipo mwadzidzidzi kavuluvulu anayambika pa msikapo mpaka anakasasula chisakasa cha mkuluyu ndikusiya katundu wonse ali pa mbalambanda . Anthu anadzidzimuka ataona njoka yaikulu ikuzungulila mdengu lina momwe munali mphwetekereyo. Apa anthu anakwiya mpaka kumpha njokayo ndikudula mutu . Mwini njokayo atafika pa msikapo analira ngati wawonekeredwa zovuta uku akuitana achimwene ndikuchondelela kuti amubwezere njoka yakeyo . Pakadali pano anthu ambiri muy msikawo asangalala kwambiri mpaka ena anachita mphwando. Zikumveka kuti mkuluyu wapita kwawo ku dowa ndipo anthu akuganiza kuti njokayo inali ya masengo yomwe amagwiritsa ntchito pokawira ndalama za anthu mu msika.


Mwamuna wina kwa Mtwalo m’boma la Mzimba wachimina anthu atatentha njinga yake yamoto ku chibwenzi. Chomwe chachitika mchoti mwamunayo anamanga banja ndi mkazi wina mpaka mulungu anamudalitsa ndi ana awiri. Mkuluyo amagwira ntchito za ulimi wa njuchi ndipo amayendera alimi osiyanasiyana. Zikumveka kuti mai wina yemwe amachita uli wa njuchiwo mderalo anagonekera khosi kwa mkuluyu mpaka anthu awiriwa kugwa mchikondi. Chibwezi chawo chitafumbila mwamunayo amapita kwa mkaziyo ndikumakagona. Kamba koti mkazi-yo mwamuna wake anali ku Joni achibale anaimbila foni mwamuna wake kufotokoza zomwe akuchita mkaziyo. Mwamunayo anatumiza ndalama kwa achibale kuti alembe ganyu anthu kuti amuugwire mkaziyo kuti pakhale umboni wokwanila. Mwachizolowezi mwamuna wachibweziyo anafika pakhomopo ndikukabisa njinga yake ya moto kuseli kwa nyumba ndikukukwilila mipesi ndikukalowa mnyumba mwa mkazi-yo . Koma phuno salota pamene mkuluyu amabiusa njingayo anthu ena amamuona ndipo anangoyatsa moto. Mwamunayo anali kwambiri kamba koti njingayo inali yaku ofesi ndipo anawona ngati akulota . Apa mkuluyo anatuluka mnyumbamo ali mbulanda mkuyamba kuthawa ndipo mpaka pano sakupezeka mderalo. Akulu-kulu a ku ntrchito komwe amagwira ntchito mkuluyu akakoka njingayo ngati umboni ndipo anthu ambiri akumudzudzula mkuluyu kamba kowononga ntchito chifukwa cha zibwezi. Pakadali pano mkazi wa mkuluyu wapita kwawo ku Nkhata-bay ndipo waneneytsa kuti sabwerelana banja ndi mwamunayo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter