You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma13/12/17

13/12/17

Written by  Newsroom

Mwamuna wina ku Migowi m’boma la Phalombe yemwe anali pa ubwenzi wa ntseri ndi mkazi wamwini wachimina.

13
December

Nkhaniyi ikuti mkaziyo mwamuna wake wakhala akugwira ntchito ku Joni zaka zingapo zapitazo ndipo maiyo atatsala anangoti laponda kuyamba kuzemberana ndi njondayo mpakana chibwenzicho kufumbila. Masiku obwerela kuno kumudzi atakwana mwini mkaziyo anaimbila foni mkazi wake kuti akubwera kutchuthi komanso kuti adzaonane ndi banja lake pamodzi ndi abale onse. Apa mkaziyo nkhaniyi anailandila ndi chisoni poganizila ubwenzi wa ntseri omwe ali nawo pakati pake ndi mwamuna wakubayo. Pa chifukwachi sanachedwe koma kukafotokozera mwamuna wachibwenziyo koma akanadziwa sakanatero chifukwa mwamuna wachibwenziyo anagwa pansi mpakana kukomoka atamva za nkhaniyi. Anthu akufuna kwabwino anayamba kukupiza ndikuthira madzi mwamunayo ndipo mwa mwai anatsitsimuka. Koma chomwe chagwetsa nkhongono anthu mderalo mchakuti mwamuna waku Joniyo atamva za nkhaniyi sanapupulume koma kutsimikizila mzakeyo kuti apitilize banja ndi mkazi wakeyo zomwe iye anakana. Pamene timalandila nkhaniyi mkaziyo anauza mwamuna wa chibwenziyo kuti asade nkhawa chifukwa ubwenzi wao upitilira koma amudikire kuti ayambe kudya ndalama zaku Joni. Pakadali pano zadziwika kuti mwini mkaziyo wathetsa banja.

 

Mnyamata wina mdera la Mponela m’boma la Dowa wachimina chifukwa cha nchuuno. Nkhaniyi ikuti mchimwene wa mnyamatayo anapeza banja mderalo kuchokera kwao m’boma la Salima ndipo zonse zimayenda bwino lomwe ku chikamwini komwe amakhala. Mnyamatayo ataona kuti sizimamuyendera anaganiza zotsatila mchimwene wakeyo mcholinga choti akamupezere maganyu mboma la Dowa-lo. M’malo mopitila maganyuwo mnyamatayo anayamba kudyerela maso mlamu wake mpakana ubwenzi wa ntseri unayambika. Anthuwo akhala ali pa ubwenzi kwa chaka ndi theka kufikira masiku apitawa anthu ena atatsina khutu mchimwene wakeyo za nkhaniyi. Apa mchimweneyo posafuna kukangana ndi m’bale wakeyo anakasuma kwa nyakwawa ndipo ku bwalo la milandu anthu awiriwo anangoti zoli ngati nkhuku zachitopa. Nyakwawayo inalamula mnyamatayo kuti ipereke chakudya chonse chomwe anapeza mchakachi kuphatikiza chimanga ndipo kumapeto kwake anamuuza kuti achoke mderalo. Pamene timalandila nkhaniyi mwini mkaziyo akupitilizabe banja ndi mkaziyo zomwe ena ati akadangothetsa banjalo. Pakadali pano mnyamatayo wagwira njakata potengera kuti ngakhale ndalama yobwerelera kumudzi m’boma la Salima alibe ndipo akukhalira kuzungulira zungulira mderalo.

 

Mwamuna wina mdera la Chikho m’boma la Ntchisi akukhala mwa mantha pa zomwe zamuchitikira. Mwamunayo pakati pa usiku anadzidzimuka atamva kugwa kwa chinthu chodabwitsa kuchokera pa kona la nyumba yake. Atayatsa nyali mwamunayo sanamvetse kuona chimbalame chofanana ndi kadzidzi chitangokhala pansi koma chitafungatila dzila. Apa mwamunayo anasowa mtengo ogwira ndipo m’malo mwake anathamangira panja ndikukatenga chimwala chachikulu nkuphinja nacho chimbalamecho koma akupumila mphuno. Kenako ataona kuti chimbalamecho chikuthatha anafuula ndikuitana anthu okhala nawo pafupi kuti adzaone za malodzazo. Posakhalitsa anthu ambiri anathamangira kunyumbako koma ena m’malo mothandiza mzaoyo anayamba kumuloza zala kuti zachitika chifukwa choti mkuluyo ngokhulupilira matsenga. Ngakhale ena anayamba kumuloza zala ena ati zachitika chifukwa cha njiru potengera kuti mwamunayo ndi olimbikira pa ntchito zotukula banja lake. Mwamunayo pakadali pano ati achita chili chonse kuti athane ndi yemwe akumuyenda mapazi.

 

Mwambo wa chinkhoswe unathera panjira kwa gulupu Wira ku Machinga. Mai wina mderalo wakhala asakukwatiwa ndipo m’malo mwake akhala ali pa maubwenzi a ntseli ndi amuna osiyana-siyana mcholinga choti mwina tsiku lina adzachita mwai. Masiku apitawo mkaziyo anapalana ubwenzi ndi njonda ina koma yosakwatilanso ndikutsimikizila maiyo kuti amange naye banja. Pamene anthu awiriwo amagwirizana za nkhaniyi nkuti maiyo ali ndi pathupi pa miyezi ingapo koma samafuna kuulura poopa kuti mwamunayo akhoza kusintha maganizo. Pa chifukwachi anayamba kukonzekera za chinkhoswe mpakana zinathekadi. Koma amai ena omwe samasangalala zochita za mzaoyo ndipo amadziwa za chinsinsicho anapita ku mwambowo ndikukafotokozera mbali zonse ziwiri zokhudza pathupi pa maiyo. Apa mwambowo unasokonezeka ndipo anthu ena anauza mai yemwe amachita chinkhoswecho kuti ali ndi ufulu otsutsa zomwe akunena amzakewo popita ku chipatala. Maiyo zinamukoka manja ndipo anakanitsitsa kwa ntuwagalu zomwe zinachititsa kuti anthu ambiri akhulupilire za nkhaniyi. Pakadali pano anthu ena adzudzula amai omwe achita zaupanduzo pamene ena ati achita bwino kukhaulitsa mai osakhulupilikayo.

 

Mai wina kwa gulupu Mkwaila mdera la Mkanda ku Mulanje anakodzedwa. Zaka zingapo zapitazo mkamwini wina anakwatila mwana wa maiyo koma nthawi zambiri mkazi wake amaonana ndi diso la mkhwezure ndi mai akewo pa zifukwa zosadziwika bwino. Mwa zina maiyo wakhala akuuza mwana waoyo kuti achoke pakhomopo kuti akapeze malo okhala chikhalireni ndi malo a bambo ake. Masiku apitawo mkamwiniyo anayamba ntchito youmba zidina mcholinga choti akonzenso nyumba yomwe amakhala. Apongozi akewo ataona izi zinawaipila ndipo m’malo mwake analanda zida zonse zomwe amagwiritsa ntchito uku akukwakwaza mcholinga choti asapitilize ntchitoyo. Mwana wa maiyo ataona izi sanaimve koma kugwira mai akewo mpakana kuwathidzimula mpakana kukodzedwa komanso kulephera kupita ku nsika kukagulitsa mati-mati. Anthu ambiri anakhamukira kunyumbako ndikuyamba kuleletsa ndeuyo. Pamene timalandila nkhaniyi maiyo wapepesa banjalo. Anthu ambiri komanso mikoko yogona adzudzula kwambiri mwanayo ndi mkamwiniyo pa nkhaniyi pamene ena adzudzula maiyo paza khalidwe lake losasunga anthu .

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter