You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma12/12/17

12/12/17

Written by  Newsroom


Ntchembere zina ku Fatima m’dera la mfumu Mlolo m’boma la Nsanje zinakalipira mai wina wa mwana m’modzi poyankhula zoduka mutu pagulu.

12
December

Nkhaniyi ikuti amaiwo kuphatikizapo amuna amapita ku msonkhano wa bungwe lina m’deralo. Akuyenda anthuwo pambuyo pawo panatulukira mwamuna wina wa kabaza yemwe anakweza mai wina woyembekezera pa njinga yemwe amamuperekeza ku chipatala matenda atamuyamba. Atafika pomwe panali gulu la anthuwo wa kabazayo anapempha anthuwo kuti afumuke ndikumulola kudutsa kamba koti amathamangira ku chipatala ndi mai woyembekezerayo. Pa nthawi yomwe wakabazayo amadutsa pa gululo, mai woyembekezera yemwe anamunyamula pa kaliyala amaoneka kuti matenda anamuyambadi. Wa kabazayo atadutsa mai yemwe ndi ntchembere kamodziyo anayamba kunyogodola mai m’nzake woyembekezerayo yemwenso amaoneka wachitsikana ponena kuti iye samapita mofulumira bwanji ku chipatala? Maiyo anapitirizanso kunena kuti pamene amachita zaozo ife tinaliko ndiye zitikhudze. Kamba ka mauwa anankungwi omwe anali pa malowo anapsya mtima mpaka kulangiza mai yemwe amayankhula zoduka mutuyo kuti nkofunika kuti amukokerenso m’kanyumba komata kuti akalandire mlango. Kamba koti kwa iwo maiyo ndi wosalangidwa. Koma mai wosamverayo anapitiriza kunena kuti mukufuna kubisira ndani, mukadadziwa kuti amunawa masiku ano akumaona zambiri pa makina a internet ngakhalenso foni zawo za m’manja simukadatero? Anapitiriza motero mai wosalangidwayo. Pa nthawiyo, ntchemberezo zinakhala chete popwetekedwa mtima ndi zomwe mai wosamvayo amayankhula. 

 

Mwamuna wina wapa mudzi wa Kawenje kwa Chilooko m’boma la Ntchisi akupukusa mutu wopanda nyanga mbalame itamubera foni m’matsenga. Nkhaniyi ikuti mwamunayo ndi wodzilimbikira kotero kuti pakhomo pake ndipa mwana alirenji. Ngakhale anthu sanakolore zochuluka chaka chino malinga ndi ng’amba komansa kuchuluka kwa mvula m’madera ena zomwe zadza kamba ka kusintha kwa nyengo banjalo liri ndi chakudya chokwana chaka chonse. Anthu ena omwe safunira zabwino banjali atalephera kuchita zawo pamaso anatumiza mbalame m’matsenga yomwe inakaba foni ya m’manja ya 13-thousand Kwacha ya mlimiyo. Mlimiyo atadzambatuka ku tulo anadabwa kupeza kuti foni yake ya m’manja yasowa pomwe anaiika. Atayesera kuiimba foniyo inapezeka kuti ndi yozimitsa. Koma kutacha m’mawa mlimiyo anadabwa kuona nthenga za mbalame zitakanilira pa zenera laku chipinda chake chogona. Apa m’pamene mlimiyo anatsimikiza kuti mbalameyo ndi ya matsenga yomwe munthu wina wosafunira banjalo zabwino waitumiza ndikumubera foni yake ya m’manja. Koma mlimiyo wanenetsa kuti sakhala pansi kufikira naye apeze chithandizo pa nkhaniyi.

 

Banja lina kwa Liwaakhwa mdera la Nkanda m’boma la Mulanje likukhala mwa mantha. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mtsikana wina mderalo anali ndi pakati pa miyezi isanu ndi itatu. Ndipo sabata yatha mtsikanayo anapita ku sikelo pachipatala china mderalo komwe anamwino anamulangiza kuti apite kunyumba ndipo adzikadikira matenda akayamba. Iye anapitadi kwao koma usiku wa tsiku lotsatira iye analota ali ndi khanda mmanja, komanso anthu achilendo akumuthangitsa. Ku tuloko anthuwo ankakuwa kuti amupha mtsikanayo akapanda kutaya khanda lomwe ali nalo mmanja. Mtsikanayo anayetsetsa kuthawa koma anthuwo anapitirizabe kumuthamangitsa koma ali pafupi kumugwira iye anaponya khanda-lo pansi. Atadzidzimuka anadabwa kuona kuti analibe pakati pomwe anali napo pa miyezi isanu ndi itatu. Apo anakuwa kuitana makolo ake omwe anali nchipinda china mnyumbamo omwe anafika kudzaona za malodzazo. Koma banjalo silinamvetse za zachilendozo kotero kuti usiku womwewo anakadziwitsa nyakwawa yapa mudzi pawo za nkhaniyi. Kuchoka kwa pakati m’jira ya matsenga zikutsimikiza zamatsenga zambiri zomwe anthu akukumana nazo mderalo komanso monga kutchulidwa maina pakati pa usiku, kumva athu osaoneka akuyenda padenga komanso kuyaka kwa moto m’mitengo pakati pa usiku koma mitengoyo wosapsya. Pakadali pano, banjalo likadali ndi mantha chifukwa cha za matsengazo.

 

Nyakwawa ina ku Linthipe m’boma la Dedza yalira ngati mwana chifukwa cholilira mkazi. Nkhaniyi ikuti nyakwawa-yo ili ndi khalidwe lolanda akazi a weni ndipo yathetsa mabanja ena kale oposa khumi mderalo.Masiku apitawo mnyamata wina anafunsira mmodzi mwa akazi anai omwe nyakwawayo ili nayo pa banja yemwe ndi wachitsikana. Chibwenzi cha awiriwo chitafumbila mai-yo anayamba kutailira osalabadira za mwamuna wakeyo. Izi zinachititsa kuti nyakwawayo idziwe za nkhaniyo. Ndipo pamene inamva za nkhaniyo masiku apitawo inayamba kulira ngati mwana chifukwa kuti mnyamatayo wafunsira mkazi wa nyakwawayo. Pakadali pano nyakwawayo ikumatsatira mnyamatayo ku madimba komwe akulima kumuchondelera kuti athetse ubwenzi wake ndi mkazi wake wachinai ndipo nyakwawayo yalonjeza kuti imupatsa mnyamatayo malo ngati ubwenzi wa awiriwo ukatha. Koma mnyamatayo wanenetsa kuti iye sakufuna malo koma mkaziyo kamba koti poyamba mkaziyo anali pa ubwenzi ndi m’nyamatayo ndipo nyakwawayo idachita kulanda mkaziyo kwa m’nyamatayo. Mtsikanayo atakhala pa banja ndi nyakwawayo waona kuti kuli bwino abwelere m’buyo kwa bwenzi lake yemwenso ndi wachinyamata m’nzake. Pakadalipano anthu mderalo akuiseka nyakwawayo.

 

Mwamuna wina kwa M’biza ku Zomba wapulumukira mkamwa mwa mbuzi achitetezo atafuna kumumbandila. Chomwe chinachitika nchakuti mwamunayo analolela mkazi wake kumachita geni mdera –lo. Komano mwamunayo anayamba kudabwa ndi mayendedwe a makzi wakeyo kamba nthawi zambiri amafika pakhomo usiku. Akamufunsa mkaziyo amayankha mwathamo kusonyeza kuti mkaziyo amamuyendadi njomba mwamuna wakeyo. Pa chifukwa ichi mwamunayo anapeza mkazi wina kuti azimutsamalira. Pamenepa mkazi wamkuluyo pokhumudwa kuti mwamuna wake wapeza mkazi wina anakamang’ala nkhaniyi kwa achitetezo omwe anakonza kuti akamugwire kuchibwenziko pofuna kumuchititsa manyazi mwamunayo. Koma tsiku lina mwamunayo ali kuchibwenziko anadzindikira kuti panja pa nyumba ya mkazi wachibwenziyo pafika mkazi wake ndi anthu ena kuti amugwire. Apo mwamunayo adalowa m’dalamu lamowa nkubisala. Mkazi wa mkuluyo pamodzi ndi achitetezowo anafuna-funa mnyumba monse koma osamupeza mwamunayo ndipo anthuwo anachoka pakhomopo manja ali ku nkhongo. Pamenepo mwamunayo anapeza mpata nkutuluka mdalamu ndipo anagona komweko osapitanso kwa mkazi wake wamkuluyo. Koma m’bandakucha wa tsiku lotsatira anapita kwa mkazi wake wamkuluyo zovala zake zili thepete komanso fungo gu! chifukwa cha fungo la mowa lomwe analitenga mdalamu anabisala muja. Ndipo atafika kunyumbako anadzazira mkazi wake wamkuluyo kamba ka zomwe mkaziyo anachita pomema nkhondo kuti akamugwire pomwe ku chibwenziko. Atafika kunyumbako anaulula kuti mkaziyo ndi achitetezo sadamugwire popeza anabisala m’dalamu. Ndipo chifukwa chokwiya ndi kupsya mtima mwamunayo walamula mkazi wa mkuluyo kuti amange katundu yense kutanthauza kuti banja ndi mkaziyo latheratu. Pakadali pano, mkaziyo wamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti zivute zitani sangalole kulekana ndi mwamuna wakeyo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter