You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma01/12/17

01/12/17

Written by  Newsroom

Banja lina ndi nyakwawa ina mdera la Malili ku Lilongwe akuyang’anizana ndi diso la mkhwezule.

01
December

Nkhaniyi ikuti zaka ziwiri zapitazo ku banjako kunachitika maliro ndipo masiku apitawa kunali mwambo wa chiliza. Pofuna kuonetsa chikondi pa m’bale waoyo ena mwa apa banjapo omwe amaoneka kuti ndi opeza anagula chiliza chamakono chomwe anakangozika pa mandapo. Tsiku lina analandila malipoti oti chilizacho chaphwanyika ndipo atafufuza zadziwika kuti anthu ena osawadziwa anakhalira chilizacho mwina pa nthawi yoika maliro anthu ena. Apa anafedwa sanaimve koma kuzula chilizacho ndikukachitula pakhonde pa nyakwawa ati pokwiya kuti nyakwawayo ikanatha kulangiza anthuwo pa nthawiyo. Nyakwawayo inaona ngati kutulo koma malodza pa zomwe anachita anthuwo ndipo mbali ziwilizo zinayamba kulalatilana Pamene timalandila nkhaniyi sizikudziwika kuti nkhaniyi yatha bwanji chifukwa mwa zina mikoko yogona kopmanso nyakwawayo akwiya kwambiri ndi nkhaniyi.

 

Mwamuna wina kwa Jali m’boma la Zomba yemwe amadziwika pa nkhani zoyankhulayankhula wachimina. Nkhaniyi ikuti m’deralo munali maliro ndipo nyakwawa ya mderalo inalangiza adzukulu kuti akayambe kukumba manda ndipo zinachitikadi. Mkuluyo yemwe amatchuka kuti mwini mzinda anapita kumandako ndikuyamba kudzudzula adzukuluwo kuti manda ambiri omwe akhala akukumba sakhala okuya. Apa adzukuluwo anmakwiya kwambiri mpakana kumugwira mwamunayo ndikugwentsera mandamo uku akumuuza kuti atuluka pokhapokha amalize kukumba. Mphekesera inapita kunyumba ya siwa ndipo mikoko yogona motumidwa ndi nyakwawa ya mderalo anachonderela adzukuluwo kuti amukhululukire mwamunayo. Atangotuluka mdzenjemo mwamunayo anamuthambitsa makofi koma atayamba kumuthila dothi lamanda ndipo analiyatsa liwiro losayang’ana pambuyo. Pamene timalandila nkhaniyi mwamunayo wanenetsa kuti sadzayambilanso ndi khalidwe lakelo. Koma ngakhale anatero sizinamveke chifukwa mwa amaitanitsa ku bwalo la milandu kuti akayankhe mlande odzetsa chisokonezo. Anthu ena ati akukhulupilira kuti mkuluyo mutiu wake sumayenda bwino pamene ena ati mkuluyo amafuna maudindo a mderalo.

 

Mwamuna wina mdera la Kambwiri ku Salima yemwe amadzitcha yekha kuti ndi mpondamatiki wa mderalo analira momvetsa chisoni. Ngakhale mwamunayo amadzitcha kuti ndi wachuma koma nthawi zambiri amakhala khwakhwakhwa. Anthu akamufunsa kuti amadzivutilanji kudziika mgulu la anthu olemera , mwamunayo wakhala akuyankha m’maso muli gwa kuti chikhupiliro chimalenga zinthu zosaoneka ndi maso. Tsiku lina mwamunayo pofuna kukwanilitsa masomphenya ake anazemberela mbuzi ya mwini ndikuyamba kukaitsatsa malonda ku dera lina lakutali ndi komwe amakhala. Koma akanadziwa sakanatero chifukwa yemwe anakamutsatsayo anazindikira za mwini chifuyocho ndipo apa anayamba kukuwa uku atamugwira mkuluyo. Anthu atasonkhana pa malopo chifukwa cha kukuwako ndipo kunali kumenya kosayang’ana nkhope mpakana mpondamatikiyo analira ngati khanda. Ngakhale mwamunayo analira momvetsa chisoni anthu sanamusiye koma kumuthidzimula kwa chakwanu leka uku ena akumufunsa kuti, amadyabwino mwataninso? Anayesa kuchondelera kuti amusiye koma sizinamveke kufikira ena omwe amamwa nawo mowa wa kabanga anagwada kuchonderala anthuwoi.

 

Gogo wina mdera la Chikweo ku Machinga yemwe amagwira ntchito yokonza njinga zakapalasa analira ngati khanda. Nkhaniyi ikuti gogoyo wakhala akugwira ntchitoyo yomwe imadziwikanso kuti tchapo koma chodabwitsa wakhala akuuza anthu kuti sakufuna kuti abale ndi anansi adzadye chuma chake iyoyo ikadzatsamila nkono. Pa chifukwachi zina mwa ndalama zomwe amapeza pa tchapoyo amakwilira pansi pa malo omweo ati mcholinga choti sakufuna kuti aliyense otsala adzadalire chuma chake. Koma chifukwa choti ntchito ya tchapo simayenda bwino ndipo amapezeka ali khwakhwakhwa gogoyo inaganiza zoti afukule ndalamazo koma anaona ngati kutulo ena atawakwangwanula ndalamazo. Apa gogoyo inalira chokweza ngati momwe imachitila khanda ndipo anthu ambiri kuphatikizapo makasitomala ake anakhamukira pa malopo koma m’malo mothandiza gogoyo anthu ena anayamba kuiseka itafotokozera anthuwo za nkhaniyi. Pamene timalandila nkhaniyi gogoyo yanenetsa kuti sidzabisanso ndalama pokumbila pansi koma m’malo mwake ikapeza ndalama idzigwiritsa ntchito ndalamazo moyenera. Anthu akufuna kwabwino kuphatikizapo nyakwawa ya mderalo athandiza gogoyo ndi zinthu zina.

 

Anthu akwa Yasini ku Chiradzulu ati sakumvetsa pa zomwe wachita mwamuna wina wapa banja mderalo. Nkhaniyi ikuti mwamunayo anakwatila mkazi kuchokera ku dera lina loyandikana nalo ndikukhala naye pa chitengwa. Koma mkazi wa mwamunayo m’malo mosunga banja anayamba kuyenda njomba mwamuna wake . Amzake a mwamunayo komanso abale ake akhala akuuza mwamunayo za mphekeserayo ndipo pachifukwachi anayamba kulondola zochita za mkaziyo koma sizinaphule kanthu. Mwamunayo m’malo mwake amakhalira kulongozana ndi mkazi wakeyo tsiku lirilonse mpakana mkaziyo anafika potopa ndi khalidwe la mwamuna wakeyo. Tsiku lina mkangano unabuka pakati pao koma chifukwa chochepa mphamvu kwa mphongoyo anakunthidwa ndi mkazi wakeyo mpakana thaphya ndikumukhadzula mlomo . Mkuluyo analira ngati momwe amamvekera munthu olengeza zochitikachitika za mdera. Poyambilira anthu ambiri amaona ngati zachibwana koma atamvetsera bwino lomwe anamva kufuula kuchokera kwa mphongoyo. Atayamba kupeza bwino mwamunayo anadabwitsa anthu ponena kuti zimachitika ndipo akukhalira limodzi ngati banja ndi mkazi wakeyo. Anthu mderalo ati sakukaika kuti mwamunayo anamudyetsa khuzumule.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter