You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma30/11/17

30/11/17

Written by  Newsroom

Mai wina ku Blantyre akuyenda mogwetsa nkhope yake pansi chifukwa cha manyazi.

30
November

Nkhaniyi yati mayiyo ndi mdindo ku mpingo tsono pokhala masiku ano ogwilitsa ntchito luso la makina amakono kumpingoko adakhazikitsa gulu lao pa whatsup. Ngati atsogoleli kumpingowo amakhala akugawana zinthu zosiyanasiyana pofuna kukweza mpingo. Koma mayiyo wa udindoyo zikumveka kuti ati anali ndi chibwenzi cha mseli ndi m’modzi mwa akulu ampingo. Tsono mayiyo anaganiza zotumiza chithunzi chomwe anadzijambula ali chibadwile ndipo m’malo mopita kwa atsogoleli chifukwa akuti anangolemba kuti atsogo landilani, chinakafika kugulu lonse lapa Whatsup kumpingo. Mayiyo atadziwa kuti zatere zinamukoka manja kwambili mpaka kufuna kutuluka gululo koma zinakanika. Panopa, zamveka kuti mayiyo wadula phanzi ku mpingoko chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi yomwe ili mkamwamkamwa kumpingowo pakati pa akulu.


Mtsikana wina kwa Malambo m’boma la Ntchitsi wayimisa mitu mikoko yogona atathesa banja lake lochita kumangitsa kutchalichi pasanathe mwezi. Nkhaniyi ikuti mtsikanayu anamangitsa ukwati woyera mwezi wathawu. Koma chodabwitsa ndi choti patsiku laukwatilo, mtsikanayo ati amaoneka kuti sizikumukhuza. Ndipo akuchimuna anadabwa ndi khalidwe lakelo. Kenako anatengera pambali mwamuna wa mtsikanayo ndikumufunsa chomwe chimachititsa kuti mkaziyo azioneka wosasangalala. Koma mwamunayo anayankha kuti nayenso akudabwa nazo. Ndipo mwambo waukwati utatha, mwamuna anadabwa kuona kuti mkaziyo amaphatikiza mabuluku atatu pogona. Ndipo atamufunsa, mkaziyo anayankhga kuti sakumufuna mwamunayo. Apa nyamatayo sanachedwe koma kukatula nkhaniyi kwa ankhoswe. Komabe mkaziyo anayanklha pamaso pa ankhoswe kuti sakumufuna. Ndipo anati abweza ndalama za chiongo zomwe anapereka. Malinga ndi yemwe watitumizira nkhaniyi, mwamunayo ati angokhalira mnyumba chifukwa cha manyazi ndi zomwe zachitikazo.

 

 

Mikoko yogona kwa TA, Nazombe mboma la Phalombe yaima mitu agulupu ena mdelalo atagulitsa mitengo yakumanda. Nkhani-yi ikuti agulupu akhala akuletsa anthu kudula mitengo kumanda ati ponena kuti anthu akuononga chilengedwe ndipo zinathekadi. Koma mosakhalitsa anthu anadabwa kuona kuti mitengo ikutha kumanda pa chifukwa-chi anthu am’mudzi anagwilizana kuti aonetsetse yemwe akuona mitengo mdelalo. Koma tsiku lina adzukulu nao akuti amafuna kugulitsa mitengoyo koma agulupu anakaniza patatha masiku zinadziwika kuti mitengo yagulitsidwa ndipo atafufuza zinadziwika kuti agulupuwo ndi omwe akhala akuba mitengo kumanda. Pamenepa, adzukulu anapita kunyumba kwa agulupuwo omwe ndi wachinyamata kwambili koma anakapeza kuti wathawa pakhomopo malinga nkuti anali atamva kale za nkhaniyi. Pakadali pano adzukulu anenetsa kuti athana ndi agulupuwo omwe akuti akusambula kumanda. Ena ati manyado akuwakulila agulupuwo malinga nkuti ndi achinyamata.Mkazi wina wadabwitsa anthu pamudzi wa Ngwelelo mboma la Zomba atakafuna mkazi wina kuti ati mwamuna wake akhale pa mitala. Nkhaniyi ikuti mkazi wina wakhala pa banja ndi mwamuna wina kwa Ngweleloko koma vuto linali loti samabereka mkaziyo ndipo pa chifukwa-chi chikondi chao chimafooka. Tsiku lina mkaziyo anauza mwamuna wake kuti apita mboma la Nsanje komwe akapeze mkazi wina woti amukwatile pofuna kuti apeze mphatso ya mwana. Mwamunayo anavomera mpaka mkaziyo kukatengadi mkazi nzakeyo. Mwa zina anagwilizana momwe azikhalila ngati akazi awili mwamuna m’modzi mpaka mwamunayo anakwanitsa kumagulila akaziwo zovala zofanana. Koma masiku akumapita chikondi chinayamba kukula pa mkazi waku Nsanje uja zomwe zinakwiitsa mkazi wamkulu uja. Panopa, mkazi wamkuluyo akulingalila zothamangitsa mkaziyo ati bola azipita kwao mboma la Nsanje poopa kuti amulandilatu banja. Koma anthu akumuseka ati podziwa waziputa dala kukadzitengela mavuto.


Mwamuna wina kwa Kambionjo mboma la Ntcheu kufupi ndi kwa Sela waimitsa mitu ya mikoko yogona zitamveka kuti akumachitila azimai zamatsenga. Watumiza nkhaniyi wati mkuluyo anafunsila mtsikana wina mpaka kumupatsa 1-Hundred Thousand Kwacha yoti azikadyela kwao ndi makolo ake. Mkuluyo akuti anauza mtsikanayo kuti amukwatila koma kufika kwa mai ake anamuuzitsa kuti ofunika ndalamayo aisamalitse. Kufika m’mawa kukayang’ana pomwe anabisa ndalama paja anakapezapo 100 Kwacha yokha komanso mtsikanayo akuoneka kuti amuchita chipongwe kumalo obisika m’matsenga. Anthu omwe amva za nkhaniyi ati sikoyamba mkuluyo kuchita zotere ndikuti ndi khalidwe lake lokonda kuchita zamatsenga. Mkuluyo akuti amachita zimenezi pofuna kukhwimila ulimi wake wa kachewere. Panopa, mkuluyo akuyenda zamadulila chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi yomwe ili mkamwamkamwa mdelalo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter