You are here:CategoriesNkhani Zam'mabomaUKWATI WALEPHELEKA ZITADZIWIKA KUTI MKWATI ALI KALE PA BANJA

UKWATI WALEPHELEKA ZITADZIWIKA KUTI MKWATI ALI KALE PA BANJA Featured

Written by  Zam'maboma

Mwambo wodalitsa ukwati walepheleka pa tchalichi china ku Chigumula mu mzinda wa Blantyre zitadziwika kuti mkwati ali kale pa banja ndi mkazi wina.


Nkhaniyi ikuti mwamunayo amakhala ndi banja lake kwa Kuntaja ku Blantyre komweko. Tsono masiku angapo apitawa njondayo inatsanzika mkazi wake kuti ikupita ku mudzi ku Mwanza kukaona mai ake adwala.


Koma pa nthawiyo nkuti maiyo atatsinidwa kale khutu kuti mwamuna wakeyo akukadalitsa ukwati ndi mkazi wina ku Chigumula kotero kuti anagwirizana ndi abale ena kuti amuleke mkuluyo apite ndikuti adzakavundule madzi tsiku la ukwatilo.

Tsikulo litafika, mkazi uja anatengana ndi mwana wake, abale komanso amzake ulendo waku Chigumula. Atafika ku tchalichiko anakhala nawo mgulu la anthu omwe anafika kukaonelera mwambowo.


Pa nthawiyo mwamuna uja atakhala kutsogolo ndi mkazi watsopanoyo kudikila kuti abusa ayambe ntchito yao yodalitsa ukwati monga zikhalira.  

Posakhalitsa mkazi wake uja anangodzambatuka pamene anakhala nalunjika kutsogolo akuuza abusa kuti asadalitse ukwatiwo kaamba koti mwamunayo ndi wake ndipo kuti ali naye ana angapo.


Apatu njonda ija inangoti zolii kulakalaka pansi patatseguka kuti alowepo. Mai uja atapeleka umboni wake, abusa ndi akulu a mpingo anatsimikiza kuti mkuluyo ali kale pa banja ndipo anauza anthu kuti sadalitsa ukwatiwo kotero kuti anthu onse omwe anali mkachisimo anayamba kubalalika, ena akumvera chisoni akwatiwo pamene ena amati zachitika bwino kuti atambwali ena aphunzirepo.


Pakadali pano mkuluyo akuti sanafikebe ku nyumba kwake kwa Kuntaja.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter