You are here:CategoriesNkhani Zam'mabomaAVUMBULUTSIDWA PATHENGO AKUCHITA ZADAMA

AVUMBULUTSIDWA PATHENGO AKUCHITA ZADAMA Featured

Written by  Zam'maboma

Mayi wina ku Nguludi Turn-off, amuvumbulutsa pathengo, akuchita zadama ndi mlonda wina.

 Nkhaniyi ikuti mayiyo tsiku ndi tsiku, amatsanzika mwamuna wake chakumbandakucha kuti akupita ku madzi ndipo pozindikira vuto lamadzi m’deralo, mwamunayo samawiringula koma kulolera kuti akatunge madziwo.   

Izitu zakhala zikuchitika kwa nthawi yaitali koma mwamunayo samadziwa kuti nthawi zina mkazi wakeyo amakhala akukakumana ndi chibwenzi chake chomwe chimalondera thanki ya madzi m’phiri lina kumeneko.

Ndiye poti chozemba chidakumana nchokwawa, patsikulo anatsanzikanso chimodzimodzi kuti akulawira kukatunga madzi koma chonsecho akukakumana ndi mlondayo.  
 

Tsono amayi ena anayi omwe analawira ku msika kwa Kanje anamuona mayiyo akuchita zadama ndi mkuluyo pa thengo.

Apatu sanalimbane nazo, koma kungotola miyala nkuyamba kuwagenda. Pamenepa awiriwo anavumbuluka ali mbulanda nkuthawa pamalopo, mwamunayo buluku liri m’manja.

Amayiwo atabwerako ku msikako anayamba kufalitsa nkhaniyi mpaka mwini mkaziyo inamupeza.  Pakadali pano banja la mayiyo lasokonekera pamene mlondayo akuyenda champeni, anyamata omwe ndi achibale a mwini mkaziyo,  atamuchenjeza kuti amukuntha  akakomana naye.About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter