You are here:CategoriesNkhani Zam'mabomaNSANJE IVUTA KU CHIKWAWA

NSANJE IVUTA KU CHIKWAWA Featured

Written by  Zam'maboma

Zomwe akuchita mkulu wina kwa Mgabu mboma la Chikwawa zikudabwitsa anthu pomwe akumachitira nsanje mkazi yemwe anasiyana naye ukwati. Nkhaniyi ikuti mkuluyo poyamba anakatenga mkazi ku Thyolo nkumakakhala naye kwawo monga mtengwa. Mayiyo akuti ndi wotakataka ndipo atapita ku Chikwawako anapitiliza geni yake yogulitsa kaunjika. Koma vuto nloti mwamunayo amaonjola ndalama za mayiyo akangozisiya poyera, ndipo izi zakhala zikumuwawa mayiyo maka chifukwa choti akamubera ndalamazo amakapatsa akazi ena. Potopa ndi khalidweli mayiyo anamuuza mwamunayo kuti akufuna akamutule kwawo koma mwamunayo amangonyalanyaza. Tsiku lina mwamunayo anafika ndi mkazi wina pakhomopo nkumuuza mkaziyo kuti achoke pakhomopo adzipita kwawo komwe akufunako. Mayiyo atamva izi, anangoti laponda la mphawi diwa, nthawi yomweyo kupakira katundu wake nkuona msana wa njira. Tsono mayiyo atasiyanitsa momwe geni ake imayendera mbomalo ndi kwawo ku Thyolo, anaganiza zochita lendi m’dera lomwelo.   Tsono chomwe chikumachitika panopa nchakuti, mwamunayo walemba aganyu woti azimulonda mayiyo moti anawauza kuti akandzangomuona mayiyo ndi mwamuna wina adzamudziwitse msanga. Koma anthu atamva nkhaniyi, adabwa nazo kwambili ati kaamba koti mwamunayo ndiye anamuthamangitsa mayiyo pakhomopo. Pakadali pano anthu ena alangiza mayiyo kuti ngati sakumufunadi mwamuna wakeyo ndi bwino adzingopita kwawo ku Thyolo poopa kuti mwamuna wakeyo angamuchite chipongwe.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter