Katswiri wa nkhonya ochokera m’dziko la South Africa, Ruann Visser, wati iye akong’ontha ndi kugwetsa Mussa Ajibu, amene ndi katswiri wa zigogodo wa m’dziko muno, mu ndime yoyamba mwa zisanu ndi zitatu zimene akuyenera kumenyana.
Visser, yemwe ndi wamtali mododometsa, anayankhula izi atangofika m’dziko muno pa bwalo la ndege la Kamuzu mumzinda wa Lilongwe pamodzi ndi katswiri wina Francy Ntetu wa m’dziko la Democratic Republic of Congo (DRC).
Ntetu, amene amayimilira dziko la Canada, awonetsana chamuna ndi namandwa pa nkhonya m’dziko muno, Alick Mwenda.
“Ndine ochezeka ndi kakhala kunja kwa ring koma ndi kalowa mu ring ndimasintha mawanga,” anachenjeza Ntetu.
Youth Boxing Promotion ndi imene yakonza masewerowa amene achitike Lamulungu ku Lilongwe ku Area 36.