Yemwe anali wachiwiri kwa prezidenti wachipani cha Democratic Progressive Party (DPP), a Uladi Mussa, wati agwira ntchito limodzi ndi atsogoleli achipani cha MCP pofuna kuonetsetsa kuti chipanichi chipitilire kukhala champhamvu.
A Mussa amayankhula ku Dedza pabwalo la Phillip Holseman kumene mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera amachititsa msonkhano wa chitukuko.
Mwa zina a Mussa ati ma area omwe adawakhazikitsa okwana 188 tsopano awasandutsa kukhala a chipani cha MCP.
Iwo adalowa m’chipani cha MCP masiku apitawa kuchoka kuchipani cha DPP ati poona mfundo zabwino zomwe mtsogoleri wa dziko lino akutsatila potsogolela dziko lino.