Mwambo wa maliro a Hope Chisanu wayamba tsopano kumudzi kwa Nyaka, mdera la Mfumu Kalumbu ku Lilongwe.
Polankhula pa mwambowo, Msuweni wa Hope Chisanu wathokoza abale komanso ena akufuna kwabwino amene anathandiza kuti thupi la Hope lifike kuno ku Malawi ngakhale pena amataya mtima kuti mwina sizitheka.
Iwo ati imfa ya Hope yathandiza kulumikizitsa abale ake akuno ku Malawi ndi m’maiko osiyanasiyana komanso kuno ku Malawi.
Iwo apempha abale onse kuti athandize ana awiri a Hope Chisanu kuti amalize maphunziro a ukachenjede.
A Chisanu adagwirako ntchito ku MBC ndi Capital Radio ngati owulutsa mawu pa wayilesi.
Olemba: Isaac Jali