Mneneri Shepherd Bushiri ndi mkazi wake Mary lero ali kubwalo lamilandu la Resident Magistrate ku Lilongwe.
Bwalo lamilanduli likumva pempho la boma la South Africa kuti a Bushiri akayankhire milandu yawo m’dzikolo.
Oimira a Bushiri ndi akazi awo pamlanduwu lero akuyenera kupitilira kufunsa mboni yaboma yochokera m’dziko la South Africa, a Sibongire Mnzinyathi, omwenso ndi ozenga milandu ku Gauteng m’dzikolo, pa zomwe akudziwa pamlanduwu.