Khoti lina m’boma la Phalombe lalamula a Paul Mwina a zaka 35 zakubadwa kuti akagwire jele kwa zaka 14 chifukwa adagwililira mwana omupeza wazaka 12 pofuna kulemera.
Ofalitsankhani pa Polisi ya m’bomali, a Jimmy Kapanja, ati bamboyu adapita kwa sing’anga wina pofuna kukhwima kuti alemere ndipo atabwera ndilufotokozera mkazi wake zoyenera kuchita, sadazengereze koma kulolera malodzawo.
Komabe mwanayo adakatsina khutu m’bale wake, yemwe adakatula nkhaniyi ku Polisi.
A Mwina ndi a m’mudzi mwa Volupo, mfumu yayikulu Nkhulambe m’boma la Phalombe lomwelo.