Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Mafumu ku Mzimba apepesa Dr Chakwera

Inkosi ya Makosi Mbelwa V yatsogolera mafumu m’boma la Mzimba kukapepesa President Dr Lazarus Chakwera pa imfa ya amene anali wachiwiri wawo Dr Saulos Chilima pa ngozi ya ndege ndi anthu ena asanu ndi atatu.

Inkosiyi yati mafumuwa ndi okhudzika popeza ngoziyi idachitikira m’dera lawo, mu nkharango ya Chikangawa m’bomalo, ndipo anati ndi kofunika kuwalimbikitsa Dr Chakwera pa nthawiyi kuti apitilire kutsogolera dziko lino ndi kugwira ntchito yawo moyenera.

Adathokonzanso mtsogoleri wa dziko linoyu poonetsetsa kuti akadaulo akafukufuku apeze mayankho pa chomwe chidachititsa ngoziyi.

Inkosi ya Makosi M’belwa V yapemphanso a Malawi kuti alore ngoziyi kulunzanitsa dziko lino ndipo ati avomeleze zotsatira zomwe zingatuluke pa kafukufukuyu kuti zikhale chitonthozo kwa onse.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Government plans to allocate 200,000 hectares for irrigation farming

Beatrice Mwape

Kalindo back in court for the firearm acquisition case

MBC Online

Kalindo granted bail

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.