Bungwe la Minority Shareholders Association of Listed Companies (Misalico) lati boma liwonetsetse kuti kampani za migodi zidziyika umwini wake wina pa msika wa Malawi Stock Exchange (MSE) kuti a Malawi adzigula nawo magawo.
Mlembi wa bungweli, a Frank Harawa, amafotokoza izi pamene msonkhano wa zamigodi watha lero mu mzinda wa Lilongwe.
Bungwe la Misalico ndi la anthu amene ali ndi masheya pa msika wa Malawi Stock Exchange.
Mukanema ali m’munsiyu, a Harawa akufotokoza zambiri.