You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma25/10/17

25/10/17

Written by  Newsroom

Athawa mamuna wa chibwenzi kamba ka ndalama

Tili mboma la Lilongwe m’mudzi mwa Kamwana, Mtsikana wina akuyenda mozemba poopa mwamuna wa chibwenzi yemwe anamudyera ndalama. 

25
October

Nkhaniyi ikuti mtsikanayo ndi khalidwe ake lomadyera amuna pomwe amawanamiza kuti amukwatira. Masiku apitawa anachita chibwenzi ndi mnyamata wina wa m’mudzi momwemo ndipo anagwirizana zomanga banja.  Mwa zina myamatayo wakhala akugulira mkaziyo zinthu zosiyanasiyana komanso kumupatsa ndalama. Chibwenzicho chinafika pa mpondachimera moti mnyamatayo anakhulupiliradi kuti wapeza nthiti yake.  Pofuna kuwonetsa chikondi komanso kutsimikiza, mnyamatayo anagula chitenje nkukamupatsa mkaziyo pamodzi ndi 19 thousand kwacha.  Tsono chomwe chakhumudwitsa mwamunayo panopa nchakuti mkaziyo anayamba kuthawathawa moti akamuuza kuti akupita kwawoko iye amachokapo kupita kwa mbale wake wina mpaka osawonana ndi bwenzi lakelo.  Izi akuti zakhala zikuchitika kangapo konse ndipo atatopa ndi khalidweli wangomuuza kuti amubwezere ndalama zake apo biii awona polekera.  Koma ngakhale izi zili chomwechi, mtsikanayo akuyankhula mwa thamo kuti sangakwatirane ndi mnyamatayo ati kamba koti amangofuna kumudyera komanso akunama kuti wamumvera mbili zoipa.  Pakadali pano anthu ambili m’mudzimo alangiza mtsikanayo kuti abweze ndalamazo ngati sakumufuna mwamunayo chifukwa choti sakudziwa zomwe  mwamunayo mu mtima mwake.

 

Anjatidwa kamba kogwilira nzukulu wawo

Mkulu wina wa zaka 72 wa m’mudzi mwa Nantunga kwa T/A Chikweo mboma la  Machinga  amulamula kuti kakhale ku ndende ndi kugwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka khumi nzinayi chifukwa chogwilira mdzukulu wake wa zaka zinayi.  Malinga ndi mboni pa nkhaniyi, mkuluyo akuti wakhala akugwilira mwanayo kawiri konse ndipo nkhaniyi inaululika pamene agogo ake akazi a mwanayo anamudabwa mayendedwe ake.  Mwanayo akuti amavutika poyenda ndipo atamufunsa mpomwe anaulula kuti agogo ake amunawo ndiwo anamugwilira.  Pofuna kutsimikiza nkhaniyi, mwanayo anamutengera ku chipatala chapa  Chikweo Health Centre komwe madotolo anatsimikizadi kuti mwanayo anamugwilira. Atamva chigamulocho, mkuluyo anapempha akhothi kuti amuchepetsere chilangocho ati kamba koti ndi munthu wachikulire.  Koma magistrate wa khothi lomwe limazenga mlanduwo  anakana pempholo ponena kuti zomwe anachita mkuluyo ndi nkhanza zazikulu zosayenera kuchita munthu wachikulire  malinga nkuti iye ndi amene  akanakhala patsogolo kusamalira ndi kuteteza moyo wa mwanayo. Pakadali pano nkhaniyi yakhumudwitsa anthu ambili m’deralo moti ena akuganiza kuti mkuluyo ndi wokhwima.

 

Anyamata ena awonetsedwa nyenyezi

Anyamata ena atatu  ogwira ntchito pa kampani ina kwa Ngomani ku Lilongwe awaonetsa nyenyezi usana atawaphaphalitsa makofi chifukwa chozemba kupereka ngongole .  Yemwe watitumizira nkhaniyi wati anyamatawo nthawi zambili amagula nsima ndi mbatata yootcha pa nthawi ya nkhomaliro ndipo anali makasitomala a mayi wina pamalopo.  Ataona kuti chikasitomala chamera mizu, mayiyo anayamba kuwakongoza ndipo poyamba anyamatawo amakhulupilika kubweza ngonglezo.  Koma kenaka atakongola nsima ndi mbatata yoootcha anayamba kuzemba zemba mpaka mayiyo kufika pothodwa.  Ataona kuti sakumupatsabe ndalama zake, anapita kukamang’ala ku polisi ndipo apolisi anayitanitsa anyamatawo.  Kumeneko anyamatawo anawaphaphalitsa makofi atayamba kukana mlanduwo.  Kenaka akuti anavomera mlanduwo koma anati ndalama za mwezi wathau awononga kale.  Pachifukwacho anyamatawo alonjeza kuti abweza ngongoleyo kumapeto kwa mwezi uno ndipo awachenjeza kuti ngati sabweza awoa chomwe chidameta nkhanga mpala.  Pakadali pano mayiyo ndi anyamatawo akuonana ndi diso la nkhwezule chifukwa cha nkhaniyi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter