You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma23/10/17

23/10/17

Written by  Newsroom

 Mwambo wa chiliza usokonekela

Mwambo wachiliza unasokonekera nyakwawa zitakana kutsekula kumanda kwa gulupu Chonjowa mdera la Chilooko m’boma la Ntchisi.

23
October

Nkhaniyi ikuti kumeneko kunali gogo wina wa zaka 87, ndipo atazunzika ndi matendawo kwanthawi gogoyo adamwalira. Patadutsa chaka chimodzi chimwalilire achibale amalemuyo anakonza mwambo womanga chiliza pofuna kulemeka malemu gogoyo. Zonse zomanga chilizacho zinayenda bwino mpaka masiku apitawo pomwe adafuna kuti anthu akaone chilizacho. Monga zikhalira pamudzipo panafika anthu ambiri-mbiri kuphatikizapo nyakwawa kuzachitira umboni za mwambowo. Apo eni mbumba anapereka chakudya monga nsima, mpunga ndi zakudya zina zosiyana-siyana kwa anthu omwe anafika pamudzipo. Koma kamba ka kuchuluka kwa anthu omwe anafika pamudzipo achibalewo sanakwanitse kudyetsa aliyense. Mwa zina mmalo mopereka ndiwo zankhuli kwa nyakwawa zomwe pachikondwelerocho, anthuwo anapereka nsomba. Koma anthuwo anadabwa kuti nyakwawazo zinakana chakudyacho mpaka kuopsyeza kuti sidzikatsekula kumanda pokhapokha atazipatsa ndiwo za nkhuli. Koma chifukwa choti ambumba anali atamaliza chakudya chomwe anakonzera anthu pamwambopo, mwambowo unaima mpaka kwa maola asanu. Pakadali pano anthu ena ati atengera nkhani kwa mfumu ya ndodo kuti ilangize nyakwa zadyerazo.

 

Mayi wina akhala mobisala kamba ka zizimba
Mayi wina ku Chingale mboma la Zomba akukhala mobisala m’dera lina atadziwa kuti anthu akumufunafuna chifukwa chosunga zizimba za mwana wke yemwe akuti ndi mbava yoopsya. Yemwe watitumizira nkhaniyi wati maiyo anabereka mwana m’modzi wa mwamuna koma akuti ndi mbava yoopsya. Kwa zaka zambili mwana wakeyo wakhala akusowetsa mtendere anthu m’deralo powabera zinthu zosiyanasiyana kuphatikizapo kuthyola makola koma akuti anthu samamva kuti kwabwera mbava malinga ndi zithumwa zomwe amamusungira mayi akewo.. Masiku apitawa mnyamatayo anapita kukathyola khola la mbuzi la mkulu wina wokhwima ndipo mwini wakeyo anamva msanga nkuyamba kumuthamangitsa. Apatu mnyamatayo ananjonjola ngati nkhwali komabe mwini wakeyo mothandizana ndi anthu ena m’mudzimo anamugwira. Pamenepa anatenga chikwanje nkumukhapakhapa ku msana ndi mapazi ndipo kenaka anamududuluza kupita naye kawo. Tsono chifukwa cha zizimba mayi akewo anadziwiratu kuti mwana wakeyo amugwira ndipo pamene anthu amafika kunyumbako anakapeza mayiyo atathawa kale. Pakadali pano mnyamatayo akudwala mwakayakaya pamene mayi akewo athawa m’mudzimo ndipo komwe alowera sikukudziwika.

Akakamila ku chikamwini
Mkulu wina kwa T/A Juma mboma la Mulanje waimitsa mitu mikoko yogona atakakamila kuchikamwini pamene anamukaniza kuti agumule nyumba yomwe amagona ndi malermu mkazi wake. Nkhaniyi ikuti mkuluyo anakwatira m’mudzi mwa Namowa ndipo amakhala ku chikamwini ndi mkazi wakeyo. Mwatsoka mkaziyo anamwalira ndipo patatha miyezi isanu ndi itatu akuchikazi anamusudzula mkuluyo pofuna kumumasula kuti adzipita kwawo. Koma mkuluyo anakhumudwitsa anthu pamudzipo atapempha kuti agumule nyumba yomwe anamanga pamudzipo ncholinga choti atenge njerwazo akamangire nyumba kwawo. Akuchikaziwo anakana pempholo ndipo anamutsimikizira kuti kuteroko nkulaula mudzi. Posamvetsa zimenezi, mwamunayo wakakamila pamudzipo ndipo wati sachoka pokhapokha akuchikaziwo amumvere pempho lakelo. Pakadali pano mkuluyo akukhala pamudzipo mwakufuna kwake kamba koti anthu pamudzipo sakulabadira za pemphp lakelo.

Akwangwanulidwa K63,000
Mwamuna wina wa m’mudzi mwa Zamani kwa T/A Mazengera mboma la Lilongwe amuyeretsa m’maso atamukwangwanula K63,000 chifukwa chofuna kulemera. Nkhaniyi ikuti mwamunayo ali ndi golosale ndipo tsiku lina anamva za munthu wina yemwe amati ndi sing’anga. Mwa zina munthuyo amauza anthu kuti amachulukitsa ndalama komanso ali ndi njoka zokawa ndalama. Mwamunayo atamva izi anafunitsitsa kukomana ndi munthuyo ndipo izi zinathekadi. Pa mkumanowo sing’anga wolengayo anatsimikizira mkuluyo kuti atha kumuchulukitsira ndalama kapena kumupatsa njoka yokawa ndalama ndipo anamupatsa mwayi woti asankhe njira yomwe akufuna. Pochita mantha ndi njokayo, mkuluyo anasankha njira yochulukitsa ndalamayo ndipo anamupatsa sing’angayo 63 thousand zomwe anati akasakaniza ndi zitsamba zake zikwana 120 thousand kwacha. Atamupatsa ndalamazo, Sing’angayo anapempha mkuluyo kuti apitile limodzi kumanda kuti mizimu ikavomereze ndipo ndalamazo anaziyika mu nsupa. Atapita kumudzi sing’angayo anauza mkuluyo kuti apitenso yekha ku mandako ndipo nsupayo anamusiyira nkumaganiza kuti ndalamazo zili momwemo. Koma mkuluyo anangoona ku njira kuli zii ndipo atayang’ana mbotolomo anapeza kuti munalibe ndalamazo. Apatu mkuluyo anayamba kulira ngati kwagwa Maliro koma anthu ena atamva nkhaniyi anayamba kumuseka komabe anamulangiza kuti angolimba mtima chifukwa choti munthuyo ndi wakuba ndipo sangapezekenso m’mudzimo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter