You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma20/10/17

20/10/17

Written by  Newsroom

Mwamuna wina asamuka kamba ka utambwali
Mwamuna wina mdera la Kachere ku Dedza wasamuka mderalo chifukwa cha utambwali.

20
October

 

Nkhaniyi ikuti mwamunayo ndi otchuka mderalo pochititsa lendi minda yake ndipo kwa zaka zambiri zakhala zikumuyendera. Chaka chino mwamunayo anachititsa lendi munda wina kwa mphongo ina koma chifukwa choti mphongoyo imachedwa kulima anaganiza zotsasa mundawo kwa munthu winanso ati mcholinga choti apezeretu zipangizo za ulimi. Posafuna kuchedwa mwamunayo anayamba kulima patangodutsa masiku awiri, koma tsiku lina ali mkati kulima mwamuna oyamba uja anafika pa malopo ndikukalipila mzakeyo. Winayo sanafune kukangana ndi mzakeyo ndipo m’malo mwake anauza mzakeyo kuti abisale mundamo ndikuimbila foni mwini mundayo kuti adzatenge ndalama yotsala. Mwini mundayo analunjika kumundako koma ali mkati kukambilana yemwe anabisalayo anangoti balamanthu. Apa mwini mundayo anathamanga ngati alibe mafupa mpakana kugwera ku phompho. Pamene timalandila nkhaniyi mwini mundayo wasamukiratu mderalo koma mikoko yogona komanso nyakwawa ya mderalo amema anthu kuti apitilize kufunafuna tambwaliyo.

 

Atha kwawo kuopa sing'anga

Anthu ena amakomo angapo ku Mitundu ku Lilongwe asowa mnyumba zao pothawa Sing’anga wina wadzitsamba ochokera ku Mozambique. Nkhaniyi ikuti mderalo nyakwawa mogwirizana ndi mikoko yogona anaitanitsa Sing’anga kuti adzasilike deralo malinga ndi nkhani zaufiti zomwe ati zakula mderalo. Koma Sing’angayo atafika tsiku lotsatila chinthu china choneka ngati ndege yaufiti chomwe chinakutidwa ndi mphinjili, mikanda komanso nthenga za mbalame chinagwa . Tsiku lotsatila anthu anaona ngati kutulo anthu angapo ochokera m’mabanja ena anasowa mderalo zomwe zikupereka chithunzithunzi kuti akukhudzidwa ndi nkhaniyi.

 

Anamizila kudwala kuthawa ukwati

Anthu omwe anapita ku ukwati wa banja lina akhumudwa kwambili mkwati atanamizila kudwala chonsecho samafuna kumangitsa ukwati. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi akuti masiku apitawa ku Blantyre kumayenela kuchitika ukwati. Mkazi anapereka ndalama iliyonse yofunikila ali kunja komwe anali malinga nkuti awiliwo adapezana pa tsamba la Facebook pa intaneti ndipo anali asadaonane. Mkazi akuti anatumniza ndalama zokwanila kulipila zofunikila pa ukwati-wo kuphatikizapo holo. Mkazi kubwela kuno kumudzi malinga ndi amene watumiza nkhaniyi zikuonetsa kuti m’nyamata anaona mkaziyo kuti ndi wamkulu kwambili. A komiti atafunsa zamalo ngati adalipila mwamuna amavomera m’maso muli gwa! koma chonsecho anali asadalipile mkomwe. Tsiku kuyandikila usiku mwamuna ananamizila kuti wadwala mpaka kudzigwetsa ngati wakomoka. Kuchipatala anawauza kuti sakudwala ndiponso sadakomoke, koma chodabwitsa mchakuti atakafunsa kumalo komwe amati analipila kale ndalama za nkhani nkhani zinadziwika kuti sadalipire. Tsiku la ukwati m’mawa ananamizilanso kukomoka mpaka mchimwene wake kuyesela kumuchondelela koma sizidaphule kanthu. Panopa, sizikudziwika kuti zinatha bwanji chifukwa nkuti mkazi atavala kale velo ya ukwatiwo. Koma anthu ena ati nkutheka kuti mwamunayo anali wadyela ndikuti amafuna kungodya ndalama za mkaziyo.

 

Amangililidwa pa mtengo ku manda

Kwa Muluma mdela la Shire North Ku Mkaya mboma la Balaka mkulu wina amumangilila pa mtengo kumanda. Nkhaniyi ikuti mkulu wina mdelalo salabadila zoti m’mudzi mwachitika malilo kotelo kuti amapitililabe kupita kumunda komanso ku ntchito zina zapa khomo. Choncho masiku lelo mdelalo kuli malilo a nyakwawa ina ndipo anthu onse anakhamukila kusiwako. Koma anthu atafufuza za mkulu uja akuti anapezeka kuti ali ku dimba komwe amalima phwetekele ndi ndiwo zamasamba. Pa chifukwa-chi adzukulu ndi anthu ena omwe anali kumanda anapita kudimba kwa mkuluyo komwe amukwidzinga ndi dzingwe pa mtengo. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi ati akufuna kuti mkuluyo amukhaulitse kuti adziwe kulemekeza mwambo wa malilo akagwa m’mudzi. Anthu ena anati nkofunika amusiye podikila kuti tsiku lina zikadzamugwela adzasowe mtengo ogwila. Mkuluyo akuti analila kwambili polingalila za ululu omwe akuumva.

 

Anjatidwa poganizilidwa kuti agwilira mwana wawo
Apolisi ku Ntaja mboma la Machinga agwila mkulu wina wa zaka 36 Kabichi Botomu pomuganizila kuti wagwilila mwana wake omupeza wa chaka chimodzi ndi miyezi 9. Malinga ndi mneneli wa apolisi ku Machinga Davie Suluma, Botumu adakwatila mai yemwe ali ndi ana kale ndipo momwe amamukwatila anamupezansi ndi mapasa awili. Tsiku lina mkazi wake analawilila kotunga madzi ndipo anatenga khanda limodzi linalo anasiila amuna ake. Koma pobwela anadzapeza kuti mwanayo wavulala kwambili kumalo obisika pachifukwa mayiyo anakanena nkhaniyi ku polisi mwamunayo atalephela kufotokoza chomwe chinachitika. Kupita kuchipatala zinatsimikizika kuti Botomu anagwililadi khandalo. Kabichi Botumu yemwe kwa Kalonga mdela la Mfumu Chowe mboma la Mangochi wayamba kale kuonekela kubwalo la milandu pa nkhani-yi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter