You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma18/10/17

18/10/17

Written by  Newsroom

Asambisidwa makofi kamba kau katakwe

Mwamuna wina kwa Ngokwe mboma la Machinga anaona zakuda anthu atamusambitsa ndi makofi chifukwa chozembetsa katundu.

18
October

Nkhaniyi ikuti bungwe lina laza chifundo limagawa zinthu zosiyana-siyana kuphatikizapo mafuta ophikira kwa anthu ovutika mderalo ndipo pa tsikulo anthu ambiri anasonkhana kudzalandila thandizolo kuphatikizapo anthu achikulile. M’modzi mwa anthu achikulilewo analandila chigubu cha 5 litres cha mafuta ophikira ndipo anachisiya pansi mcholinga choti adikirire kulandilanso zinthu zina. Pa chifukwachi mwamunayo yemwe anakhala moyandikana ndi gogoyo anakhwekhwereza chigubucho mcholinga chofuna kuzembetsa koma osadziwa kuti anthu ena amamuona. Posakhalitsa anthu omwe amaona izi zikuchitika anadzidzimutsa mwamunayo ndi makofi omuonetsa nyenyezi zomwe zinadabwitsa gulu la wanthu lomwe limalandila thandizolo. Apa chipwilikiti chinabuka chifukwa mwa zina anthu pa malopo kunali kukuntha kolapitsa mpakana mwamunayo analira ngati mwana. Pamene izi zimachitika anthu ena anakhuthulira mwamunayo thope mpakana anachoka pa malopo ali nyontcholi. Pakadali pano nyakwawa ya m’mudzimo yati ikokera ku bwalo mwamunayo kuti akayankhe mlandu wakuba ngakhale mwamunayo wasowa mderalo.

 

Landilodi alira kuutsi

Mwini nyumba zina za rendi kwa Mazengera mboma la Lilongwe akulilira ku utsi. Mwamunayo ali ndi nyumba zambiri za rendi mderalo ndipo zaka ziwiri zapitazi wakhala akumanganso nyumba zina koma chifukwa cha nkhani yaza chuma nyumba yake ina akulephera kuimaliza mpakana pano. Koma chodabwitsa mkuluyo chifukwa choti akusaka kwambiri ndalama wakhala akuchitisa rent nyumba yosathayo kwa anthu ochita za dama. Mwamuna wina mderalo wakhala ali pa ubwenzi wa mseri ndi mkazi wamwini ndipo akhala akuchita rendi chinyumbacho ndikumachitilamo zachisembwere. Anthu mderalo akhala akufotokozera mwamunayo za nkhaniyi ndipo iye anangoti adzagwira yekha. Tsiku lina mwachizolowezi mwamunayo anatengana ndi mkaziyo ndikukabindikira mchinyumbacho koma mphuno salota mwini mkaziyo nayenso anakabisala ndi ziphona pachinyumbacho. Apa ataona anthuwo akulowa mchinyumbacho sanafune kuwatutumutsa ndipo macheza ali mkati mwamunayo pamodzi ndi amzakewo anagumula chinyumbacho mpakana kusalaza, koma mwatsoka samadziwa kuti anthuwo anali akutulukira pa bowo lina. Pakadali pano mwini nyumbayo akukhalira kulilira nyumba yake chifukwa ku bwalo nkhaniyi inamuipila ndipo amulangiza kuti akapitiliza ndi nkhaniyi amukokela ku chitolokosi. Anthu ambiri mderalo akukhalira kumuseka mwini nyumbayo ndipo akuyenda njira zodula ngati mwana piye ogwera mvuwo ndipo banja la mayiyo laweyeseka.

 

Mai wina ayenda monyowa kamba ka manyazi

Mai wina kwa Kamchere mdera la Mkanda ku Mchinji akuyenda monyowa chifukwa cha manyazi. Maiyo wakhala pa banja ndi mwamuna wina wa bizinesi mderalo koma kwa nthawi yayitali maiyo wakhala ali pa ubwenzi wa nseri ndi mlamu wake. Amzake a mpondamatikiyi akamuuza za nkhaniyi wakhala akulankhula kuti mchimwe wakeyo adzaona polekera. Tsiku lina mpondamatikiyo anapita kogula zinthu zamu shopu yake ndipo pofika pakhomo anaona ngati malodza mkazi wake yemwe iye amamuchitila chilichonse atakolekana miyendo ndi mchimwene wake. Apa mchimwene wa nchuunoyo pamodzi ndi maiyo anasowa mtengo wogwira ndipo anangoti kakasi kusowa cholankhula uku akupuma wefuwefu chifukwa cha mantha. Koma chodabwitsa mpondamatikiyo sanafune kuchita ziwawa ndipo m’malo mwake anajambula anthuwo ndi foni yake ya m’manja kuti ukakhale umbobi kubwalo. Kumapeto kwake anauza mchimwene wakeyo kuti asade nkhawa koma akwatile mlamu wakeyo ndipo anapitiliza kuuza mkazi wakeyo kuti banja latha uku akumuponyera katundu wake yense panja. Pamene timalandila nkhaniyi mchimwene wa mpondamatikiyo wauza mlamu wakeyo kuti sangamukwatile chifukwa ali ndi mkazi. Pakadali pano mkaziyo akunong’oneza bombono chifukwa cha chibwana .

 

Chipwilikiti pa bwalo la nyakwawa

Chipwilikiti chinabuka ku bwalo la nyakwawa mdera la Chilikumwendo mboma la Dedza. Nkhaniyi ikuti mwamuna wina yemwe wakhala pa banja kwa nthawi yayitali wakhalanso ali pa ubwenzi wa nseri ndi atsikana osiyana-siyana koma mkazi wake samadziwa. M’modzi mwa atsikanawo ataona kuti njondayo sikumusamalira ngati kale analembera kalata mkazi wa njondayo yomunyoza ndikunyogodola mcholinga choti akayambana amukwatire iyeyo. Maiyo posafuna kulongolora anakatula nkhaniyi ku bwalo ndipo nyakwawa ya mudzimo inayitanitsa mtsikanayo, njondayo ndi mwini mwamunayo koma mtsikanayo anaonetsa kusagonja pa nkhaniyi ponena kuti sangaimve chifukwa choti kwa iye mwamuna ndi wake. Abale a mwini mwamunayo pokwiya ndi nkhaniyo anapempha nyakwawayo kuti athane ndi mtsikanayo zomwe zinapangitsa kuti njondayo ikhale kumbuyo kwa mtsikanayo. Pa chifukwachi ndeu ya fumbi inabuka pakati pa mbali ziwirizi ndipo mapeto ake nyakwawayo inadzudzula mtsikanayo ndipo inalamula kuti alipire chindapusa cha nkhuku zisanu. Pamene timalandila nkhaniyi nkuti mtsikanayo akunenetsa kuti sasiila pomwepa ndi nkhaniyi. Ngakhale anthu ambiri akukhalira kulozerana mtsikanayo koma iye sizikumukhudza pomwe akulankhula mwathamo kuti chaka chake ndi chino.

 

 

Atandala kutchire
Mwamuna wina kwa Kalumo mboma la Ntchisi akukhalira kubisala ku ntchire mphekesera itamupeza kuti akumufunafuna mcholinga choti amukokere ku bwalo. Mwamunayo wakhala akusiya akazi ambiri mderalo ndipo pa chifukwachi achibale akhala akumulangiza koma njondayo yakhala ikuponyera ku nkhongo malangizowo. Masiku apitawa mchemwali wa njondayo anaitanitsa mchimwene wakeyo kunyumba kwake mcholinga choti amulangize paza khalidwe lake la nchuuno. Mwa zina mchemwali wakeyo anadzudzula njondayo kuti akuwachititsa manyazi posintha akazi komanso pobwerelana ndi hure wina mderalo. Izi sizinasangalatse mwamunayo ndipo pa chifukwachi anagwira mchemwali wakeyo ndikuyamba kumumenya kodetsa nkhawa koma chifukwa cha mfuu anthu ambiri anakhamukira kunyumbako. Pofuna kuteteza maiyo anthuwo anagwira mwamunayo ndikuyamba kumukuntha koonetsa nyenyezi. Mwamunayo chifukwa cha ululu anatsimikizila gululo kuti wachilapa koma sizinamveke. Mwa tsoka mwamunayo anawapulumuka ndipo pakadali pano sakudziwika komwe walowera. Mikoko yogona komanso nyakwawa ya mderalo ati apitilira ndi ntchito yofunafuna mwamunayo mpaka atakaponda kubwalo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter