You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma07/10/17

07/10/17

Written by  Newsroom

Mwamuna wina adabwitsa anthu pa maliro
Mwamuna wina pa mudzi wina kwa Kachere m’boma la Dedza wadabwitsa anthu pa maliro a mwana wake.

07
October

Nkhaniyi ikuti mwana wa mwamuna m’banjalo anadwala mosadziwika bwino mpaka kutsikira kuli chete matendawo atathipwa koma masiku ochepa. Imfayo inadzetsa chikaiko pakati pa anthu ambiri pa mudzipo kuphatikizapo aku banja. Koma ngakhale nkhaniyi inali chomwecho mwamuna wa m’banjamo zimaoneka kuti sizimamukhudza kweni-kweni zomwe anthu ena amati akudziwapo kanthu. Pa tsiku loika malirowo mwamunayo anapempha amai omwe anafungatira chitanda mu siwa komanso aku mpingo kuti amulore kutsanzikana ndi malemu mwana wake. Anthu ambiri anagwira pakamwa m’nyumba ya siwapo kuphatikizapo mikoko yogona kuona mwamunayo mwa zina akutemera mphini mtembowo komanso kusiya ndalama mbokosi la maliro. Amai omwe anafungatira chitandacho komanso ampingo anayamba kuchita mantha ndi zomwe amachita mkuluyo koma iye sizimamukhudza. Mwambo wa maliro unayamba wasokonezeka kwa ola limodzi mikoko yogona mogwirizana ndi nyakwawa yapa mudzipo atafotokozera namfedwayo kuti asapitilize ndi zomwe amachitazo. Mwambo wonse utatha mwamunayo anamuitanitsa ku bwalo la nyakwawa komwe anakanitsitsa kupepesa. Nkhaniyi yapherezera malinga ndi zomwe anthu akhala akunena kuti mwamunayo ndi nthakati wotheratu.

Amuna ena amangililidwa pa mtengo

Amuna ena atatu pa mudzi wa Chinse kwa Malili m’boma la Lilongwe omwe amalembera ndalama zachipepeso pa Maliro omwe anagwa pa mudzipo anawamangilira ku mtengo mpaka mwambo wonse kutha. Nkhaniyi ikuti zovuta zitachitika pa mudzipo monga mwa nthawi zonse amuna atatuwo ndiwo amalondoloza ndikulembera ndalama komanso zinthu zina zomwe anthu amapepeso nazo banja lofedwa pa tsikulo. Koma amuna atatuwo pa zifukwa zodziwa wokha anabisa ndalama zina zomwe mkulu wina anapereka zopepesera anamfedwa. Amuna atatuwo akuti anagwiritsa ntchito zina mwa ndalamazo pokagulira kabanga yemwe anadakwa. Zonsezi zinadziwika pa siwa pamene amalengeza za chipepeso zomwe anthu apereka ku banja lofedwa. Mkulu wina yemwe anapereka ndalama yochuluka ndithu pa zocvutazo sanamutchule ndipo pamodzi ndi mikoko yogona atawapanikiza anyamata atatuwo zinadziwika kuti anathyolera mthumba ndalama zachipepeso zokwana 15-thousand Kwacha. Kamba ka izi anyakwawa komanso mikoko yogona inalamula anyamatawo kuti abweze ndalama zachipepesozo, zomwe anabwezadi kupatula 2-thousand Kwacha yomwe anagulira bibida. Ndipo analamula anyamata adzitho kuti awamangilire ku mtengo kufikira mwambo wonse waku manda kutha. Pakadalipano anyamata atatuwo akubindikira m’nyumba kamba ka manyazi ndi nkhaniyi, malinganso nkuti nkhope mikono ndi miyendo ndi zotupa kamba ka zingwe zomwe anawanjata nazo ku mtengo.

 

Malonda asokonekela kamba ka khoswe

Malonda anasokonezeka pa msika wina ku Madise m’boma la Dowa khoswe wolemera makilogramu asanu ataba ndalama zokwana 5-million Kwacha. Watitumizira nkhaniyi wati amalonda ambiri pa msikapo akhala akuduka kamba koti katundu wawo amatha koma osapeza phindu leni-leni. Kamba ka izi ambiri mwa amalondawo akhala akusamuka ndikumakagulitsira malonda awo misika ina. Koma ambiri mwa anthu omwe amapitirizabe kugulitsa malonda awo pa msikawo anali anthu omwe amadzithemba kuti athana nazo malinga ndi chitaka chomwe chakhala chikuchitika kumeneko. Masiku apitawa anthu pa msikapo anadabwa kuona chikhoswe chachikulu chomwe wamalonda wina anachigwira ku malo ake aza malonda. Wamalondayo anachenjeza onse pa msikapo kuti yemwe akumuseweretsa aona chomwe chidameta nkhanga mpala. Ndipo anachenjeza kuti yemwe akudziwa kuti khosweyo ndi wake abwere poyera. Koma palibe munthu ndi m’modzi yense yemwe anatulukira poyera. Apo wamalondayo anakachita mtera wake kotero kuti khosweyo anasanza ndalama zapepela zokwana 5-million Kwacha ndipo pomaliza pake anamupha. Pakadalipano mkulu wina m’deralo yemwe akumuganizira kuti ndi mwini khosweyo akudwala mwa kaya-kaya.

Gule wamkulu asokoneza mapemphero

Gule wamkulu anasokoneza mwambo wa mapemphero omwe amachitika ku mpingo wina m’boma la m’boma la Kasungu. Mamembala a mpingowo anakonza mapemphero apa dera ncholinga choti apeze ndalama zoyendetsera ntchito za mpingowo. Koma mapempherowo ali mkati mamembala pa mpingowo anadabwa kuti pa mpingowo panatulukira balamanthu! msambi wa gule wamkulu motsogozedwa ndi eni dambwe omwe anayamba kuuza mamembalawo kuti awathandize kusonkhetsa ndalama kudzera n’kuvina. Apa anthu ambiri pa mpingopo anagwira pakamwa kudabwa ndi nkhaniyi pamene akuluakulu a mpingowo anatsimikizira akulu a dambwe pamodzi ndi guleyo kuti ntchito zawo ndi zosagwirizana ndi mpingowo. Ngakhale akulu-akulu a dambwewo anachondelera a mpingowo kuti awalole kuchita mwambo wa guleyo n’cholinga choti nawo apeze ndalama kuti agwiritse ntchito. Pa chifukwachi mamembala a mpingowo anagwira njakata kamba koti guleyo pamodzi ndi akulu a dambwewo anakanitsitsa kuchoka ku malowo. Kamba ka izi mpungwepungwe unabuka pakati pa mbali ziwirizo zomwenso zinachititsa kuti mapempherewo athere panjira. Anthu ambiri m’deralo akuganiza kuti anthu ena amu mpingowo omwe sagwirizana ndi atsogoleri ake ndi omwe anamema guleyo kuti asokoneze mapempherowo.


Adabwisa anthu pa maliro a mwana wake
Mwamuna wina mdera la Kachere m’boma la Dedza anadabwitsa anthu pa maliro a mwaka wake. Nkhaniyi ikuti mwana wa mwamunayo anadwala mosadziwika bwino ndipo matenda atakula anamwalira. Imfayi inadzetsa chikaiko pakati pa anthu ambiri mderalo kuphatikizapo aku banja. Koma ngakhale nkhani inali chomwecho mwamunayo sizimamukhudza zomwe zinapereka chikaiko kuti mwamunayo amadziwapo kanthu. Pa tsiku loika maliro mwamunayo anapempha amai omwe anafungatila chitanda komanso aku mpingo kuti amulore kuti atsanzikane ndi malemu mwana wake. Anthu ambiri anagwira pakamwa pa siwapo kuphatikizapo mikoko yogona chifukwa mwa zina mwamunayo anayamba kutema mphini mtembo komanso kusiya ndalama mbokosi. Amai omwe anafungatila chitanda komanso ampingo anayamba kuchita mantha ndi zomwe amachita nmkuluyo koma sizimamukhudza. Mwambo wa maliro unasokonezeka kwa ola la thunthu kufikira mikoko yogona mogwirizana ndi nyakwawa ya mderalo anauza nafedwayo kuti asapitilize ndi zomwe amachitazo. Mwambo onse utatha mwamunayo anamuitanitsa ku bwalo la nyakwawa koma chodabwitsa anakanitsitsa kupepesa chifukwa ati iye palibe yemwe angamuuze chochita ndi thupi la mwana wake. Nkhaniyi yapherezera ndi zomwe anthu akhala akumva kuti mwamunayo ndi nthakati.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter