You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma04/10/17

04/10/17

Written by  Newsroom

Anyanyalilidwa mwana ku ntchito

Mwamuna wina yemwe amagwira ntchito ku bungwe lina kwa Chimwaye kwa Kwataine m’boma la Ntcheu anazingwa mkazi wake atamunyanyalira mwana wa miyezi itatu ku ntchito.

04
October

Nkhaniyi ikuti mwamunayo anapeza mbeta pa mudzi wina m’deralo ndipo awiriwo anakwatirana mpaka kukhala ndi mphatso ya mwana. Pakadalipano mwanayo ali ndi miyezi itatu. Koma modabwitsa mwamunayo mkaziyo tsiku lina anafika ku ntchito kwa mwamunayo ndikumutulira mwanayo ponena kuti bwanji sakumugulira nsapato iye pamodzi ndi mwanayo. Atamunyanyalira mwanayo mkaziyo anachoka ku malowo osayang’ana m’buyo. Mwanayo anayamba kulira mosatonthozeka mai ake atamusiya ku malowo. Ngakhale mwamunayo anayesera kuti amwetse mwanayo mkaka wa ng’ombe koma mwanayo amangolira mosatonthozeka. Akulu-akulu aku bungwelo analangiza mwamunayo kuti apite ku nyumba kuti akakambirane ndi mkazi wakeyo za nkhaniyi. Koma mwamunayo anadabwa kuti atapita ku nyumba sanakampeze mkaziyo , ndipo atakafufuza kwao anamva kuti wathawitsana ndi mphongo ina m’deralo.

 

Mai wina aimitsa mitu mikoko yogona

Mai wapa mudzi wina kwa Maseya m’boma la Chikwawa waimitsa mitu ya mikoko yogona kamba ka zochita zake. Yemwe watitumizira nkhaniyi wati mderalo muli mai wina yemwe wakhala pa banja kwa nthawi ya-itali, ngakhale wakhala akukhumudwitsa mwamuna wake. Mwa zina, m’mbuyomu banja la mkaziyo linatha kamba koti anampezelera ali pachikondi ndi mphongo ina. Nkhaniyi itafika ku mpingo mkaziyo anagwira mwendo wa mwamuna wake nanenetsa kuti amukhululukire kamba koti ndi satana ndi yemwe anamuchititsa kuti apezeke akuchita zadamazo ndi mwamuna wakubayo. Mwamunayo motsogozedwa ndi mzimu woyera anakhululukira mkaziyo ndikubwelera ku banja. Koma tsiku lina mwamunayo anatsazika mkazi wake ndikuchoka pakhomopo kukafuna maganyu. Mkaziyo anangoti laponda la mphawi anaitanira m’nyumba chibwenzi chake cha nseri chomwe chikukhala pa mudzi woyandikana. Mwamuna wakubayo anayamba kumafika pakhomopo nthawi iliyonse monga afunila. Ngakhale abale a mkaziyo anamulangiza mbale waoyo koma iye sadawamvere ndipo anapitiliza ubwenzi wanseri ndi njonda yakubayo. Abale a mkaziyo atatopa ndi khalidwe la mbale wao anaimbira foni mwini mkaziyo kumufotokozera nkhani yonse. Atamva nkhaniyo mwamunayo anafika pakhomopo mwadzidzi ndikupezelera awiriwo ali pachikondi. Kamba ka izi mwini mkaziyo anayamba kulira ngati waonekedwa zovuta mpaka kuthamanga uku akuzungulira nyumba ndipo pa nthawiyo amachotsa zovala zake nkukhala mbulanda. Pakadali pano mwamunayo sakudziwika komwe walowera , pomwe anthu ena akuti wapenga kamba ka maganizo.

 

Anthu ayipidwa ndi zochita za mkulu wina

Anthu omwe anali pa ulendo wopita ku Muloza m’boma la Mulanje masiku apitawa anaipidwa kwambiri ndi zomwe amachita m’modzi mwa anthu apa ulendowo. Yemwe watitumizira nkhaniyi wati patsikulo, minibasi ina inanyamula anthu paulendo wopita mmadera osiyana-siyana kudzera mu mseu wa Mugabe kapena kuti Midima. Ndipo ulendowo unalai wokoma kamba koti anthu anakambirana nkhani zosiyana-siyana zina zokhudza umoyo wawo. Ena mwa anthu apa ulendowo amayamikila apolisi apa mseu kamba kolimbikitsa minibasi zizinyamula anthu atatu-atatu pampando. Zomwe zinadzetsa chisangalalo chifukwa anthu samapanikizana m’basimo. Koma mnyamata wina yemwe anakwera mpando wakutsogolo anayamba kukangana ndi dalaivalayo ponena kuti iye ndi wolemera kamba koti amanyamula matumba a mchenga. Nayenso dalaivalayo anati wolemera kwambiri ndi iyeyo chifukwa tsiku lili lonse amathamanga kupita kukatenga minibasiyo m’mawa. M’modzi mwa anthu omwe anali m’minibusiyo anafunsa dalaivalyo kuti amalemera makilogalamu angati? Mosakaika dalaivala anayankha kuti amalemera makilogalamu 70. Momwe zimachitika izi nkuti minibasiyo itafika pa mphambano yopita kwa Chinakanaka, ena amati pa Nang’ombe. Ndipo ataona wamalonda wina yemwe anali ndi sikelo yoyezela chimanga anyamatawo anagwilizana zoimitsa minibasiyo nkupita kukakwera sikeloyo. Ndipo mzake wa dalaivalayo amaoneka wokondwa atakwera sikeloyo kamba koti mlingo wake unaposa dalaivalayo. Kuima kwa ulendowo kunakwitsa apaulendo ena omwe anali m’minibasiyo.

 

Mai wina asasa mwamuna wake kamba ka njonda ina
Mai wina kwa Chilinjala ku Penga-penga m’boma la Ntcheu wapilikitsa mwamuna wake kamba ka njonda ina ya golosale. Watitumizira nkhaniyi wati mkaziyo wakhala akudyetsa njomba mwamuna wake pozemberana ndi mwamuna wa golosaleyo. Mkaziyo mwa zina ati amachita izi kamba kokopeka ndi mphatso zomwe amalandira kuchokera kwa mwamuna wa wokalayo. Kamba ka izi mkaziyo anafika popitikitsa mwamuna wakeyo yemwenso ali naye ana. Mkaziyo wanenetsa kuti samusiya mwamuna wa wokalayo ngakhale akhale mkazi wachiwiri. Anthu ambiri pa mudzipo akupukusa mitu yopanda nyanga podandaula ndi zomwe mkaziyo wachita. Koma mikoko yogona yanenetsa kuti nthawi zambiri amavutika ndi ana pa nkhani za mtunduwu.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter