You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma03/101/7

03/101/7

Written by  Newsroom

Bambo wina amuminitsa ku Lilongwe

Bambo wina yemwe wakhala akunyozera kupita ku maliro a nzake amuminitsa ku Area 49 mu mzinda wa Lilongwe.

03
October

Nkhaniyi ikuti kwa nthawi yaitali njondayo yakhala ikukana kukakhazika anzake zikawaonekela. Mikoko yogona mderalo yakhala ikudandaulira njondayo kuti idzituluka koma zonse zimathera kunkhongo. Koma masiku apitawo mwana wake anadwala. Bamboyo ngakhale anayetsera kuthamanga- thamanga matendawo anamera nthenje mpaka mwana kutsikila kuli chete. Ndipo nyakwawa ya delaro inamemama anthu kuzakhazikiza banjalo. Koma anthu omwe analipasiwapo anadabwa kwambiri zitadziwika kuti mkati mwa usikuwo bamboyo anazemba nkukapapila bibida mpaka thapsyaaa maliro a mwana wake ali mnyumba. Apo anthu ena achifundo omwe anali pamowapo adanyamulira njondayo mu wheel- burrow nkupita naye ku siwako. Kufika kwa njondoyo ili chiledzelele kunakwiitsa anthu pasiwapo mpaka anayamba kuchoka mmodzi- mmodzi mkusiya anamfedwa okha. Nawonso a mpingo omwe amayendetsa mwambo wamaliro unasiya kuyendetsa mwamboyo kaba kokwiya ndi zochita za bambo wa womwalirayo. Ndipo ataika maliro nyakwawa ya deralo inalamula bamboyo kuti ayende khomo ndi khomo ndikupepetsa aliyense yemwe anagona pasiwapo. Mkuluyo yemwe pa nthawi ya chigamuloyo amaoneka kuti mowa unali utamukungunuka anali wonyowa ngati nkhuku yogwera mvuwo.

 

Anthu ayima mitu ndi njoka ina

Anthu komanso mikoko yogona yaima mitu ndi njoka ya mtunda wa mamba yomwe aipha pa mudzi wa Kachikwatu kwa m’ndunga m’boma la Kasungu. Watitumizira nkhaniyi wati banja lina pa mudzipo lomwe liri ndi zifuyo linadabwa m’bandakucha wa lero pamene amamva mbuzi zawo m’nkhola zikulira mwachilendo kusonyeza kuti zaona chinthu china chochititsa mantha. Mwamuna wa banjalo anadzambatuka nthungo iri ku manja kuti akaone chomwe chimachitika m’nkhola la mbuzi. Atasuzumiramo anapeza njoka ya mtundu wa mamba itadzukulunga koma mbuzi zitamwazikana. Mwini zifuyoyo anafuula kuitana anthu omwe anafika ndi kugwirizana popha njokayo. Zomwe mikoko yogona adabwa nazo ndi zakuti ataipha njokayo anaiyeza pa sikelo ndipo inalemera makilogram khumi komanso imatalika mamita awiri ndi theka. Mikoko yogona yanenetsa kuti zomwe zachitikazo ndi zodabwitsa sanaonepo njoka yaikulu chomwecho kwa nthawi yaitali.

 

Mai wina ayenda zamadulira kuopa kukunthidwa

Mai wina yemwe ndi mbeta ku Central 2 ku Dwangwa m’boma la Nkhota-kota akuyenda njira zamadulira amai anzake atampanganira kuti amukunthe kamba kosokoneza mabanja a weni. Watitumizira nkhaniyi wati kwa nthawi yaitali amai ambiri kumeneko akhala akudandaula kuti amuna awo amawadyetsa njomba. Tsiku lina anthu kumeneko anadabwa kumva mfuu wa mai wina ndipo anthu atakhamukirako anapeza mwamuna wa banja lina ali ndi mai wina woyenda-yenda yemwenso amai akhala akumukaikira kuti amasokoneza mabanja awo. Ndipo amai angapo anamuumbilira ndikumuumbudza mosamvera chisoni. Anthu ena achisoni ndiwo anamuombola maiyo pomulanditsa m’manja mwa amai wolusawo. Pakadalipano maiyo wathawa m’deralo ndipo komwe walowera sikukudziwika. Koma banja la mwamuna wa mchiunoyo laweyeseka kotero kuti mkazi wa banjalo akuganiza zomanga katundu wake kuti azipita ku mudzi kwao.

 

Mwamuna wina agwidwa njakata mwini mkazi atamulanda nsapato

Mwamuna wina yemwe akugwira ntchito ku kampani ina kwa Mankhanamba ku Naminjiwa m’boma la Phalombe akusowa chonena kwa akulu-akulu aku ntchito mwini mkazi yemwe amazemberana naye atamulanda nsapato za jumbo. Watitumizira nkhaniyi wati mwamunayo yemwe wangofika kumeneko ku malowo ndi wa mchiuno. Ndipo amapitiriza khalidwe lake ku malo atsopanowo. Tsiku lina anatengana chandamale ndi mkazi wina yemwe wakhala akubwatika mwamuna wa mchiunoyo kuti sali pa banja. Ndipo tsiku lina anapangana kuti akacheze pa phiri lina. Machezawo ali mkati munthu wina yemwe anawaona ku malowo anaimbira foni mwini mkaziyo kumudziwitsa za nkhaniyi. Ndipo mwini mkaziyo sanachitire mwina koma kuthamangira ku malowo. Ndipo mkazi wodyetsa njomba mwamuna wakeyo anamuonera patali mwamuna wakeyo ndipo ananamiza bwenzi lake la nserilo kuti akukataya madzi kuthawa kunali komweko. Pamene mwamuna wakubayo amadikilira mwina mkaziyo anatulukira balamanthu ndikumuwakha mwamuna wakubayo mpaka kumulanda jombo zaku ntchito. Pakadalipano mwamuna wa mchiunoyo watupa nkhope ngati chitumbuwa ndipo sakupitanso ku ntchito. Koma zamukoka manja kuti akanenanji paza nsapato zomwe amulandazo.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter