You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma02/10/17

02/10/17

Written by  Newsroom

Anthu akwiya ndi nduna ina ku Chikwawa

Anthu okhala mdera la Ndakwera m’boma la Chikwawa ati ndi okwiya ndi zomwe yachita nduna ya mfumu ina pomwe inapita kukaveka unyakwawa.

02
October

Yemwe watumiza nkhaniyi wati masiku apitawo anthu mderalo anali okonzeka kukhala ndi nyakwawa ya tsopano. Ndipo zokonzekera zonse zimayenda bwino. Athuwo amakonzekera pokonza magule, kuphika chakudya komanso mowa kuti anthuwo adzasangalale limodzi ndi nyakwawa yatsopanoyo. Ndipo kutasala tsiku limodzi kuti aveke nyakwawayo, gulu la anthu omwe anawatuma kudzaveka nyakwayo anakana kugwira ntchitoyo ati kamba nyakwawayo inasankha ti abuthu, kuti awatumikire, kusiyana ndi momwe iwo amaganizira kuti awatumizila anamwali oti adagwa kale mdothi. Apo anthuwo ananyanyala mwambowo ndikubwerera kwao. Izi zinachititsa mikoko yogona kukachonderela anthuwo. Koma zomwe zakwiitsa anthu mderalo ndi zoti olonga ufumuwo anati apita kukalonga ufumuwo pokha-pokha atawapatsa 15 thousand kwacha komanso nkhuku zisanu.Mkulu wina ayenda zamadulira ku Zomba
Mkulu wina akuyenda zamadulira kwa gulupu Namalima mdera lina la mfumu Jenala m’boma la Zomba. Yemwe watumiza nkhaniyi wati masiku apitawo njondayo pamodzi ndi banja lake inabwerera kuchokera mziko lina komwe inakagwira ntchito. Ndipo itafika inadyerera maso mai wina yemwe ndi wamalonda pa sitolio zapa Milepa m’bomalo. Koma poona kuti sakanatha kukomana naye ndikumufunasira mkaziyo, njondayo inadandaulira mwamuna wina yemwe amakonza njinga mderalo kuti amuthandize kufunsila njoleyo ngakhaler kuti inali ya banja kale. Izi zinathekadi mpaka kuyamba kumazembarana ndi mwamuna wammchiunoyo. Mwa zina mwamunayo wakhala akugulira chiphadzuwacho zinthu zosiyana-siyana kuphatikizapo zakumwa zozizilitsa kukhosi komanso makabudula amkati. Koma anthu ena anakatsina khuthu mwini mkaziyo yemwe walonjeza kuti athana ndi njondayo kamba kolowetsa libolonje m’banja lake. Pakadali pano njonda-yo yasowa mderalo ndipo siikudziwika komwe yalowera.

 

Mwambo wa maliro wa gogo wina usokonekela

Mwambo wa maliro wa gogo ina unasokonezeka kwa gulupo Mwangata m’boma lomwelo la Zomba. Yemwe watumiza nkaniyi wati, mderalo munali gogo wina yemwe wakhala akudwala kwa kanthawi ndithu. Ndipo matenda atakula gogoyo anamwalira apa anthu komanso mafumu anafika pasiwapo kudzakhazika anamfedwawo. M’mawa wa tsiku lotsatira eni mbumba anatulutsa makasu ulendo wakumanda. Kumandako kunafika adzukulu ochulukirapo kuti athandize kukonza nyumba yotsiliza yagogoyo. Koma kamba koti banjalo ndi losowa, linaphera kupereka chakudya cha m’mawa kwa azukuluwo ndipo m’malo mwake anapititsa chakudya komanso nkuti isanakwane 12 koloko masana. Apo azukuluwo anavumbitsa mafunso kwa eni mbumba kamba kowapatsa chakudya cha masana mofulumila. Komabe mkulu wina anachonderela azukuluwo kuti amvetse kamba koti eni mbumbawo mngosowa ndipo achita zomwe akanatha kuchita. Koma chisokonezo chinabukanso panthawi yomwe anamedwa anafika kumanda ndi chitanda kamba koti azukuluwo anatseka kumandako ndikulamula kuti maliro saika. Apo anthuwo sanachitire mwina koma kutula chitanda pansi pofuna kupereka danga lokambirana ndi adzukuluwo. Koma mkulu wampingo wina ndiye analowa m’mandamo ndi kukambirana ndi adzukuluwo kuti alore anthuwo aike maliro ndipo zina akakambirane kunyumba. Pakadali pano anthu mdera ati ndi okhumudwa ndi zomwe achita azukuluwo kamba ka mtima wao wadyela.


Mwamuna wina athidzimulidwa modesa nkhawa

Mwamuna wina amuthizimula m’boma la Mchinji mpaka kutsala pang’ono kuyoyoka mano pa mphumi. Nkhaniyi ikuti njondayo inapeza ganyu ku bungwe lina ndipo anaipatsa nyumba yomwe mbali ina kumakhalanso mai wina wapabanja. Mayiyo amagwila ntchito limodzi ndi mkuluyo ndipo ndi woyembekezera. Koma tsiku lina maiyo anadabwa kuona kalata pa mpukutu wa makondomu uli m’bafa yomwe anthuwo amasambiramo. Mkalatamo bamboyo anadandaula kuti maiyo sakumulabadira ngakhale pa pulotipo alipo awiri okha ogwila ntchito kumalo amodzi. Ndipo njondayo inati inagula mipila ya abambo-yo kuti azigiwiritsa ntchito ndi maiyo. Ngakhale mkaziyo wakhala akukana kuchita zachisembwere ndi njondayo, iyo inapitilizabe kukakamiza mkaziyo kuti ayambe kumakhala ngati banja. Koma mkaziyo atatopa ndi zochita za njondayo anatula nkhaniyo kwa mwamuna wake. Choncho mkaziyo anagwirizana ndi mwamuna wake kuti alange mwamuna wamchiunoyo maka kuti mkaziyo akhale ngati wavomera zokhumba za bambo wa mchiunoyo ndipo anagwilizana zokakumana pamalo ena ogona anthu apa ulendo. Ali mchipindacho mkaziyo anatumiza uthenga wapa lamya yam’manja kwa mwamuna wake za nambala ya chipinda chomwe awiriwo analowamo. Posakhalitsa mwini mkaziyo anafika mchipindamo ndikuyamba kuphika mwamuna wamchiunoyo. Pakadali pano, mwamunayo wasiya kupita kunchito kamba ka manyazi ndi nkhaniyi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter