You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma29/09/17

29/09/17

Written by  Newsroom

Akangana ndi mkazi wake kamba ka bulu

Tili mboma la Lilongwe m’mudzi mwa Nyundo kwa T/A Chadza mwamuna wina wakangana kwambili ndi mkazi wake pa nkhani ya bulu. 

29
September

Nkhaniyi ikuti mkuluyo ali ndi mkazi ndi mwana m’modzi ndipo pa ulimi wa chaka chino anakolola theka la ngolo imodzi ya chimanga.  Kenaka  mwamunayo anayamba kuuuza mkazi wakeyo  kuti akufuna kugula bulu. Mkaziyo atafunsa kuti buluyo agula ndi chani, anamuyankha kuti m’mesa tili ndi mwana.  Izi zinachititsa mantha mkaziyo mpaka anathawa pabanjapo.  Mwamunayo ataona izi, anasasula denga la nyumbayo ndipo kenaka anagumula nyumba yonseyo nayenso nkumapita kwawo.  Pakadali pano mwamunayo ali kwawo ndipo mkaziyo ndi mwana wakeyo ali m’manja mwa makolo ake.  Anthu ambili omwe amva nkhaniyi ati akuganizira   kuti mwamunayo amafuna kukhwima popha mwana wakeyo ndipo amuyamika kwambili mkaziyo kamba kopulumutsa mwanayo.

 

Akanika kulanditsa jumbo ya nyama

Mkulu wina waona ngati malodza atalephera kulanditsa jumbo yake ya nyama kwa agalu omwe anamuzinga ku Chilobwe mu mzinda wa Blantyre.  Nkhaniyi ikuti mkuluyo ndi chidakwa koma saiwala kugula ndiwo  akamapita ku nyumba kwake.  Patsikulo mkuluyo anagula nyama ndi zonse zofunikira pa ndiwoyo.  Koma ali mkati mwa njira, anakomana ndi agalu oposa khumi omwe anamuzinga nkuyamba kukoka jumbo ya nyamayo.  Pochita mantha mkuluyo anangosiya jumboyo iye nkuyamba kuthawa mowa wonse balala.  Atakafika ku nyumba anafotokozera mkazi wake ndi ana za nkhaniyi ndipo akuti anakhumudwa kwambili malinga nkuti ku nyumbako kunalibiretu ndiwo.   Pakadali pano mkuluyo wati sadzagulanso ndiwo za nkhuli usiku poopa kukomana ndi zomwe anaonazo.

 

Alandidwa mwamuna ndi mzake waponda apa mpondepo

Zoonadi mtima wa nzako ndi tsidya lina.  Mauwa apherezera kwa mayi wina yemwe walandidwa mwamuna ndi nzake wa ponda apa nane mpondepo ku Lizulu mboma la Ntcheu.  Nkhaniyi ikuti m’deralo muli amayi awiri okondana kwambili koma m’modzi mwa amayiwo ndi mbeta.   Tsono chomwe chimachitika nchoti amayiwo amagula zovala zofanana ndipo samasiyana kulikonse komwe amapita.  Koma masiku apitawa anthu anakhumudwa atamva kuti mwamuna wa m’modzi mwa amayiyo wathawitsana ndi mayi winayo kupita ku Mangochi komwe akukhala ngati banja.  Yemwe watumiza nkhaniyi wati zikumveka kuti mayi winayo anachita chibwenzi ndi mwamuan wa nzakeyo pakanthawi koma chifukwa chokondana kwambili anthu amalephera kumutsina khutu mwini mwamunayo.  Tsono pano chibwenzicho chitafika pa mpondachimera anthu awiriwo anangoganiza zothawitsana nkukamanga banja lawolo kwina.  Pakadali pano mwini mwamunayo manja ali mkhosi kusowa mtengo wogwira malinga nkuti foni ya mwamuna wakeyo ngakhalenso mkazi nzakeyo siikugwira mpaka pano.  Pamenepa mayiyo wachenjeza amayi ena m’deralo kuti azisankha bwino anzawo ocheza nawo poopa kuti nawonso angadzaone ngati zakutulo atalandidwa mwamuna ndi nzawo wapamtima.

 

Akaniza mwana wawo kukwatira

Mkulu wina akudabwitsa anthu kwa Mfumu Mpama mboma la Chiradzulu, atakaniza mwana wake wamkazi kukwatiwa ati ncholinga choti azisunga mudzi.  Nkhaniyi ikuti mkazi wa mkuluyo anamwalira chaka chathachi ndipo adasiya ana atatu akazi okhaokha.  Tsono chomwe chachitika panopa nchoti mwana wamkulu mbanjamo wapeza mwamuna woti amange naye banja koma mkuluyo atamva nkhaniyi zinamuipira kwambili.  M’mau ake mkuluyo akuti anazazira kwambili mwana wakeyo kuti asayerekeze kukwatiwa ndi mwamunayo ngakhale wavomera zokakhala kuchikamwini.  Poona mkwiyo wa atate akewo, mtsikanayo anakatula nkhaniyi kwa atsibweni ake omwe atamufunsa mkuluyyo cholinga chake anati sakufuna kuti mwana wakeyo akwatiwe chifukwa choti ndi amene akusunga ang’ono ake pamudzipo kukhatikizaponso iyeyo.  Koma anthu ambili m’deralo ati zomwe akunena mkuluyo pa nkhaniyi  nzosamveka chifukwa choti mwanayo akakwatiwa azikhala pamudzi pomwepo ndi mwamuna wakeyo.  Pakadali pano mikoko yogona idakakambirana za nkhaniyi kuti awone momwe angamuthandizire mtsikanayo.

 

Chikhwaya china chichenjezedwa

Amuna ena  m’dera la Mfumu Tengani mboma la Nsanje achenjeza chikhwaya china m’deralo kuti chiwona zakuda ngati chipitilire kuyenda ndi akazi a eni.  Nkhaniyi ikuti m’deralo muli mpondamatiki wina yemwe akusokoneza mabanja a eni potengerapo mwayi kuti ali ndi ndalama zambili.  Mpondamatikiyo yemwe akuti ali ndi mabizinesi osiyanasiyana, wakhala akunyengerera amayi ambili apabanja kuti azigona nawo koma chonsecho ali ndi akazi atatu ovomerezeka.   Yemwe watumiza nkhaniyi wati chomwe chavuta panopa nchoti amayi ena otengeka akumakopeka ndi ndalama za mkuluyo kulolera kosokoneza mabanja awo pamene amayi ena akumakaulula nkhaniyi kwa amuna awo.  Pakadali pano amuna ambili omwe nkhaniyi ikuwakhudza agwirizana zomukhaulitsa mkuluyo ngati apitilire ndi khalidwe ake loipalo.

 

Ataya bomwetamweta atathesa chibwenzi

Mtsikana wina wataya bomwetamweta kwa msakambewa mboma la Dowa atathetsa chibwenzi ndi mnyamata wina yemwe amafuna kumanga naye banja nkukalola njonda ina mosadziwa kuti ili ndi mkazi ndi ana. Nkhaniyi ikuti mtsikanayo wakhala ali pachibwenzi ndi mnyamata wina m’deralo ndipo adagwirizana zomanga banja. Chibwenzicho akuti chatha zaka zinayi ndipo posachedwapa mtsikanayo anakomana ndi njonda ina ya galimoto nkumunamiza kuti ndi yosakwatira.  Potengeka ndi ndalama, mtsikanayo anayamba chibwenzi ndi njondayo koma mnyamatayo atamva  nkumufunsa bwenzi lakelo za nkhaniyi, anangomuuza kuti ayendere yake kusonyeza kuti chibwenzicho chatha.  Ngakhale mnyamatayo zinamuwawa polingalira zaka zinayi zomwe wakhala ali pa chibwenzi ndi mtsikanayo, anangovomerezabe kuti zikhalire momwemo.  Ndiye poti choipa chitsata mwini chibwenzicho chitafiika pa mpondachimera mpomwe mtsikanayo amatulukira kuti njondayo ili ndi mkazi ndi ana awiri.  Apatu zinamuwawa kwambili ndipo anathetsanso chibwenzi ndi njondayo nkuyamba kulumikizana ndi mnyamatayo.  Koma zachisoni, mnyamatayo wamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sangayerekeze kubwelerana ndi mtsikana wachimasomasoyo ndipo naye pobweza moto wangomuuza kuti aliyense ayendere yake kusonyeza kuti chibwennzicho chinatha, chinatha basi.

 

Banja lina liweyeseka ku Mulanje

Banja lina laweyezeka kwa gulupi Kachenje mdera la mfumu yaikulu Nkanda m’boma la Mulanje. Yemwe watumiza nkhaniyi wati kumeneko kuli banja lina lomwe kwa nthawi yaitali mwamuna wa banjalo wakhala akuzembera mkazi wake.  Koma mkaziyo akamfusa mwamuna wake za nkhani zokhuza akazi ena iye amakana kuti sangachite kamba ndi  mkulu wa mpingo wina mderalo. Koma tsiku lina mwamunayo  anatengana ndi mlongo wake wa mkazi wake kupita pa mudzi wina kukapapila mowa wa matanthi. Ndipo onse ataledzera ananyamuka ulendo wobwerela kunyumba kwao. Koma pobwerela anthuwo anadzera kunyumba ya chibwenzi cha njondayo. Ndipo atafika pakhomo pa mkaziyo  bamboyo anauza mlongo wa mkazi wakeyo, yemwe ndi mlamu wake kuti abadikira panja pa nyumba yamkaziyo. Apo mkuluyo adalowa mnyumbayo mpaka kukomedwa ndi kugona tulo tofa nato kambanso anali ataledzera kotheratu. Ndipo mlamu  wakeyo atadikira nthawi yaitali adathamangira kukauza mchemwali wake kuti mwamuna wake wakomedwa kwa mkazi wina. Apo mkazi ndi achibale adathamangira kukaona malodzawo koma pomwe amafika pakhomopo  mwamunayo anathawa  kudzera khomo lakuseri atamva phokoso lomwe anthuwo ankapanga.  Koma patapita tsabata ziwiri mkaziyo nayenso wapezeka patchire akugawana chikondi ndi mwamuna wachibwenzi.  Mikoko yogona itamufunsa iye wayankha wangoti nkhonya yobwezera imawawa. Pakadali pano anthu akuyang’ana banjalo ndi chidwi.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter