You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma28/09/17

28/09/17

Written by  Newsroom

Anjatidwa kamba kogwilira mwana wa zaka khumi
Mwamuna wina wa zaka makumi awiri m’dera la Mfumu Liwonde mboma la Machinga amulamula kuti akakhale ku ndende zaka khumi nzinayi chifukwa chogwilira mulamu wake wa zaka khumi.

28
September

Yemwe watumiza nkhaniyi wati izi zinachitika pamene mwamunayo anapita kukacheza kwa apongozi ake m’mudzi mwa Mjahito komwe pochoka anamuuza mlamu wakeyo kuti amupelekeze. Tsono ali mnjira, mwamunayo akuti anakokera mlamu wakeyo m’munda wa thonje nkumugwilira. Apa mwanayo anakanena nkhaniyi kwa atate ake omwe omwe sanalekelere koma kukauza apolisi. Apolisi anakanjata mkuluyo mpaka kumutsekulira mlandu ku khothi. Popeleka chigamulo, majistreti wa khothilo anati wapeleka chilango chokhwimacho kuti anthu ena omwe ali ndi khalidwe loipali atengerepo phunziro.

 


Asimba lokoma ndi tomato waulele 
Anthu ena anasimba mwayi pa msika wina kwa mfumu yaikulu Mlumbe ku Zomba atapeza tomato waulere. Watitumizira nkhaniyi wati mayi wina yemwe ndi wa pabanja anamva zoti mwamuna wake ali pa chibwenzi ndi mayi wina yemwe amagulitsa tomato mu msika wina m’deralo. Pa tsikulo mwini mwamunayo anauyatsa ulendo wopita ku msikako kuti akamuuze mkazi mzakeyo kuti asiye kuyenda ndi mwamuna wake. Koma atafika kumsikako, mkazi wachibwenziyo anayankhula motumbwa kuti sangasiyane ndi mwamunayo popeza amamukonda kwambiri. Izi sizinasangalase mwini mwamunayo yemwe sanachedwetse koma kupulumutsa bakera kwa mzakeyo. Nayenso mayi wachibwenziyo anadzuka ndikuvula nsalu, kusala ndi buluku lomwe anavala. Kenako ndewu yafumbi inabuka. Anthu ena anathamanga ndikukauza mwamuna yemwe amamenyeranayo. Mwamunayo atafika anayesetsa kuwalekanitsa awiriwo koma sizinatheke. Kenako anaganiza zotenga ndodo ndikuyamba kukwapula awiri onsewo ndipo anasiyana. Apa mwamunayo anatengana ndi mkazi wakeyo ndikumapita kunyumba kwawo. Atangofika kunyumba, anadabwa kuona mkazi wachibwenziyo akubwera ati posamvetsa kuti ndewuyo ipitilirebe. Izi zinakwiyisa mwamunayo yemwe anayamba kuthizimula mkaziyo kenako anapita kumsika ndikukataya madengu asanu a tomato yemwe mkazi wachibwenziyo amagulitsa. Ndiye anthu pamsikapo kunali kulimbirana tomatoyo moti anthu ena omwe anapita kumsikako kukagula tomato ndi ndiwo, amangogula ndiwo zokha koma tomato amatola waulere. Pakadali pano mkazi wachibwenziyo wanenetsa kuti amuonetsa mbwaza mwini mwamunayo ati kamba koti geni yake yaduka.

 

Bishop afuna kuchotsedwa mumpingo

Akuluakulu a mpingo wina ku Thaba m’dera la MFumu Mkanda mboma la Mulanje agwirizana zochotsa paudindo Bishop wa mpingowo ati kamba koti akudzetsa chisokonezo mu mpingo. Masiku apitawa mu nkhani zathu zam’maboma tinalengeza kuti Bishop-yo anasokoneza mwambo wa Paper Sunday pa tchalitchipo ndipo akuluakulu a mpingowo anagwirizana zomuitanitsa kuti akafotokoze chifukwa chomwe anachitira zimenezo. Bishopuyo atamva kuitanako anangodziwiratu kuti yalakwa ndipo sanapiteko. Apa akuluakulu a mpingowo agwirizana zoti angomupitira ku nyumba kwake kwa Masuku mboma lomwelo la Mulanje kuti akangomuchotsa pa udindowo ali ku nyumba komweko.

 


Mayi wa mvano agwidwa njakata
Tili mboma lomwelo la Zomba koma m’mudzi mwa Umi kwa Mfumu Chikowi, Mayi wina wamvano wagwira njakata akwawo atamusasa kuti sakumufuna pakhomopo chifukwa cha khalidwe lake la chimasomaso. Nkhaniyi ikuti mayiyo anakwatiwa zaka zambili zapitazo ndipo ali ndi ana akuluakulu omwe ena mwa iwo ali pa banja. Mayiyo yemwe amakhala ku chitengwa zaka zonsezi, mwamuna wake amapita ku Nyanja kukagula nsomba ndipo amatenga nthawi ali komweko. Pachifukwachi mayiyo anapezerapo mwayi ochita chibwenzi ndi mphongo ina koma amayinamiza kuti alibe mwamuna ndipo kuchitengwa komwe amakhalako ndikwa makolo ake. Izi zinachititsa kuti mwamuna wakubayo athe mantha mpaka kumapita kukagona kunyumba kwa mayiyo. Tsono ana apakhomopo atazindikira mayendedwe a mayi wawoyo zinawayipira koma sanamudzudzule kudikira la 40. Dzana usiku mphongoyo inafikanso panyumbapo mpaka mgonedwe koma m’mawa inaona ngati kutulo ana amayiyo atamuunjilira kumuthibula ndipo wina akuti anamubaya ndi mpeni. Anthu ena anamutengera mwamunayo ku chipatala komwe amugoneka ndipo uthenga utafika kwa mwamuna wake anangolamula kuti mayiyo alongedze katundu wake yense adzipita kwawo. Izi zinachitikadi koma mayiyo atakafika kwawo, abale akenso anamuthamangitsa ponena kuti alibe nyumba ndipo panopa komwe walowera mayiyo sikukudziwika.

Anthu azizidwa ndi imfa ya mwamuna wina

Anthu a m’mudzi mwa Chisamba m’dera la Mfumu Chilooko mboma la Ntchisi azizidwa nkhongono ndi imfa yadzidzidzi ya mwamuna wina yemwe wafa shop yake yomwe amagulitsamonso petulo itabuka moto. Ngoziyo akuti inachitika lolemba lapitali pa sitolo za chisamba mbomalo. Chomwe chinachitika nchoti cham’ma 7 koloko madzulo, malemuyo anayatsa kendulo mu shopumo nkuyamba kupungulira petulo mbotolo kuti agulitse kwa kasitomala yemwe panthawiyo anali kunja kwa shopuyo. Mosayembekezera moto unayaka pamalopo nkutsekereza shop yonseyo yomwe inali ndi potulukira pamodzi pokha ndipo anakanika kutulukamo. Malemuyo akuti anaopsysa kwambili pamodzi ndi katundu yense mu shopumo ndipo mwambo woika malirowo unachitika nthawi yomweyo. Pakadali pano anthu a m’mudzimo awalangiza kuti asiye mchitidwe wosunga mafuta a petulo ndi dizilo m’nyumba pofuna kupewa imfa za mtunduwu.

Adziponya m'madzi kamba kokana chidzudzulo

Anthu a m’mudzi wina kwa Mfumu Maliri mboma la Lilongwe ati ndi okhudzidwa ndi zomwe zachitika mbanja lina pomwe mwamuna wakadziponya m’madzi kamba kokana chidzudzulo. Nkhaniyi ikuti m’mudzimo munali mwamuna wina wapa banja koma anali ndi chizolowezi chomayenda ndi akazi a weni. Masiku apitawa anthu anamupezelera ali ndi chibwenzi ndipo achibale atamva nkhaniyi anamulangiza kuti asiye khalidwelo chifukwa choti ndiwa pa banja. Pokana chidzudzulocho mwamunayo akuti anamwa poizoni kenaka nkukadziponya mu mtsinje wina m’deralo. Mkazi wake atamva izi nayenso akuti anakadzikjweza ncholinga chofuna kutsatira mwamuna wakeyo koma anthu ena achifundo anamutulukira msanga nkumupulumutsa. Pakdali pano mayiyo yemwe akuti ndi woyembekezera amugoneka m’chipatala momwe akulandira thandizo la mankhwala.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter