You are here:CategoriesNkhani Zam'maboma27/09/17

27/09/17

Written by  Newsroom

Amugwilira njoka yake yokawa ndalama

Mkulu wina kwa Mfumu Njolomole mboma la Ntcheu mwina akhoza kulowa m’ntchire, munthu wina atamugwilira njoka yake yomwe imamuthandiza pokawa ndalama za anthu m’deralo.

27
September

Yemwe watitumizira nkhaniyi wati mkuluyo amachita bizinesi pa Tsangano Turn off koma anthu akhala akumuganizira kuti ndi wokhwima. Pachifukwachi nzake yemwe amachita naye bizinesi yofanana anamupita pansi pokatenga zitsamba kwa ng’anga ina yomwe siikudziwika. Masiku apitawa chinjoka cha mkuluyo akuti chinapita kwa nzakeyo ncholinga chokamukawa, koma kumeneko anakachigwira m’matsenga mpaka kukanika kubwelera kwa mbuyache. Zitachitika izi mkuluyo anadziwa kuti njoka yake yagwidwa ndipo atafufuza m’matsenga mwawomo anadziwa komwe kunasakama njoka yakeyo. Apatu sanachitire mwina koma kupita kukamufunsa nzakeyo. Uko nzakeyo anavomeradi kuti akusunga njokayo koma anati sangamupatse pokhapokha atamupatsa 3 point 5 million kwacha. Izi nzomwe zazunguza mutu mkuluyo moti pakadali pano anthu akumumvera chisoni kuti mwina akhoza kudwala matenda a misala. Komabe ngakhale izi zili chomwechi mwamuna yemwe akusunga njoka ya nzakeyo wamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sayitulutsa njokayo mkabati momwe akuyisunga, mpaka mkuluyo atapereka ndalamazo.

Anthu akhumudwa ndi infa ya khanda ku Lilongwe
Anthu a m’dera lina ku Lilongwe akhumudwa ndi imfa ya khanda lina lomwe lapezeka likuyandama m’chimbudzi patadutsa masiku angapo chisowere khandalo. Nkhaniyi ikuti mayi wa mwanayo yemwe ndiwa chaka chimodzi. anachokapo ndipo anasiya khandalo ndi ana anzake okulirapo. Pobwera kumeneko sanampeze mwana wakeyo pakhomopo ndipo atafufuza m’malo onse omwe amaganizira kuti atha kupezeka sanampeze mpaka kufikira tsiku lina pomwe anthu ena anapeza mwanayo akuyandama m’chimbudzi chapafupi ndi nyumba ya mayiyo. Nkhaniyi inakafika ku polisi ndipo mukufufuza kwawo adapeza kuti khandalo linafa chifukwa chobanika. Pakadali pano mwini mwanayo komanso anthu ambili a m’deralo ati sakumvetsa chomwe chinachitika kwa mwanayo kuti akapezeke m’chimbudzimo. Ndipo ena mwa anrthuwo ati mwina nkutheka kuti pali anthu ena osafunira zabwino mayiyo amene achita zachipongwezo. Tili pa nkhani ngati yomweyi, Munthu wina yemwe sakudziwika wapezeka atafa ku Area 25 mu mzinda wa Lilongwe. Anthu a m’deralo ati akuganiza kuti mkuluyo wafa chifukwa cha mowa malinga nkuti thupi lake linapezeka ndi masanzi ononkha mowa mkamwa komanso m’makutu ake. Pakadali pano thupi la malemuyo akulisunga ku nyumba ya chisoni yapa Chipatala cha Kamuzu Central podikira kuti ena alizindikire.

 


Akunthidwa ndi mkazi wake mpaka thapsya
Mkulu wina m’dera la mfumu Changata mboma la Thyolo walumbira kuti sadzamenyanso mkazi wake, mkazi wakeyo atamupanilira tsiku lina mpaka thapsya. Nkhaniyi ikuti mkuluyo ali ndi chizolowezi chomamenya mkazi wake akayambana ndipo khalidweli akuti linakula kwambili. Kenaka mayiyo anamuchalilira kuti akadzangoyerekeza kumumenyanso tsiku lian adzaona polekera. Patsikulo mkangano unayamba m’nyumbamo ndipo mwachizolowezi mwamunayo anayamba kumenya mkazi wakeyo. Koma poti mphuno salota, mayiyo anangotseka chitseko chakuchipinda makiyi nkuika m’thumba kenaka nkumuuza mwamuna wakeyo kuti lero ndiye udziwanso. Apatu chindewu chopanda woleretsa chinabuka ku chipindako ndipo mayiyo anapanilira mwamunayo mpaka kulephera kukuwa. Anthu oyandikana nawo nyumba atadabwa mfuu ya ana anathamangira kunyumbako kukamupempha mayiyo kuti atsegule chitseko chakuchipindacho poopa kuphula ngozi. Atangotsekula chitsekocho mwamunayo anatuluka chothawa m’chipindamo koma ali wefuwefu. Pakadali pano mwamunayo wanenetsa kuti sadzamenyanso mkazi wakeyo ati kamba koti wazindikira kuti amayi ambili samabwezera akamamenyedwa ndi amuna wo pongofuna kupereka ulemu chabe.

 

Apasula banja ndi manja ake
Mayi wina akunong’oneza bondo atapasula banja ndi manja ake kwa Khombedza mboma la Salima. Nkhaniyi ikuti mayiyo analowa mbanja zaka zoposa khumi zapitazo ndipo ali ndi ana anayi. Chiyambire banjalo, mayiyo wakhala akulimbana ndi mwamuna wakeyo pa nkhani yakumwa mowa mwauchidakwa komabe amakhala mopilira momwemo makamaka chifukwa choti mwamunayo amayesetsa kusamalira banja lakelo ngakhale akaledzera amatukwana mayiyo kotheratu. Tsono masiku apitawa m’mudzimo munafika banja lina kuchokera ku tauni ndipo litaona khalidwe la mkuluyo lomatukwana mkazi wakeyo akaledzera, linayamba kumuuza nzeru zina kuti ati achoke pakhomopo adzipita kwawo. Potopa ndi khalidweli, mayiyo analongedzadi katundu wake kumapita kwawo koma akadadziwa sakadachita chifukwa mwamunayo atatsala anangokatenga kanamwali m’mudzi wina nkumanga nako banja. Mayiyo atamva za nkhaniyi kumudzi kwawoko, zinamuwawa kwambili ndipo anavumbuluka kufika pakhomopo pomwe anapeza kanamwaliko katamera mapiko kukanilira pakhomopo. Pakadali pano mayiyo akunong’oneza bondo chifukwa tsopano akukhala panyumbapo ngati mitala mwamunayo atamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sangamuthamangitse namwaliyo chifukwa choti sanayambane naye.

Apulumukira mkamwa mwa mbuzi
Mnyamata wina yemwe ndi mbiyang’ambe ku Chilimba mu mzinda wa Blantyre wapulumukira mkamwa mwa mbuzi pamene galimoto imafuna kumuwomba. Nkhaniyi ikuti mnyamatayo nchizolowezi chake chomwa mowa mwauchidakwa ndipo nthawi zambili amakhala ali ndengu ndengu akamayenda. Patsikulo anakaupapila mowa ndipo akuyenda mu mseu wina galimoto yomwe imabwera kutsogolo kwake imafuna kumuomba koma mwa mwayi anthu omwe anali pafupi anamukokera kumbali. Apa dalaivala wa galimotoyo anayima nkuyamba kumulangiza mnyamatayo kuti asamayende m’miseu yodutsa galimoto akaledzera. Koma m’malo momvera malangizowo anayamba kubweza moto. Izi zinapsyetsa mtima dalaivalayo mpaka anatsika m’galimotoyo nkuyamba kumutuwitsa ndi zibakera. Anthu ena achisoni ndiwo anamuleretsa mnyamatayo ataona kuti akulira momvetsa chisoni. Pakadali anthu ambili amulangiza mnyamatayo kuti achepetse kumwa mowa chifukwa tsiku lina adzaona zakuda.

About us

Malawi Broadcasting Corporation is a public broadcaster mandated and formed by Government under an Act of Parliament in 1964, to enhance the successful implementation of all its social and economic programs...

Social Media

Catch us on these social networks for more information

Facebook Twitter RSS

Get Your Newsletter