21-05-21

Written by  Za M'maboma Desk

Mayi wina kwa Mfumu Mdunga mboma la Kasungu watenga mbili atakalowerera mwamuna wina ati kamba koti amachedwa kumukwatira. Nkhaniyi ikuti mayiyo anali pa banja koma linathapo chifukwa cha khalidwe lake lolongolola komanso kulalata mosamezera malovu. Amuna ambili akhala akumufunsira koma akangomva mbili yake, samapitilizanso maganizo awo ofuna kumanga banja ndi maiyo. Masiku apitawa mwamuna ochokera m’mudzi wina m’deralo, anamufunsira mayiyo ndipo chibwenzi chinayambika mpaka kuyamba kugwirizana za banja. Koma anthu omwe akumudziwa bwino mayiyo anamuchenjeza mwamunayo kuti akalimbe, chifukwa mayiyo ndi olongolola, sadziwa zokambirana nkhani mwa mtendere. Mwamunayo atamva izi, anabwerera m’mbuyo ndipo anadula phazi pakhomo pa mayiyo. Tsono Mayiyo ataona kuti mwamunayo sakufikanso pamudzipo, anangonyamuka ulendo omulondola kwawo komwe anakapeza mwamunayo ali kumunda kokolola chimanga. Apatu anamulondola kumunda komweko nkukamuuza kuti sapitanso kwawo, wabwera kudzalowa banja. Mwamunayo anayesera kumusasa mayiyo koma zinakanika moti tikunena pano, mayiyo adakali kwa mwamunayo ndipo anthu ambiri kumeneko akungopukusa mitu kusowa chonena.

Get Your Newsletter