21-05-21

Written by  Za Mm'aboma Desk

Mai wina wachimasomaso m’dera la Mfumu Chilooko mboma la Ntchisi, waona polekela atamukuntha kolapitsa chifukwa chokhala pa ubwenzi ndi mwamuna wa nzake. Nkhaniyi ikuti mayiyo amagwira ntchito limodzi ndi mwamuna wake ndipo ali pantchitopo anayamba kuzemberana ndi mwamuna wina wapabanja zomwe zinachititsa kuti asiyane banjalo. Mkazi wa mkuluyo atamva nkhaniyi amangowawenderera koma akuti amalephera kuwagwira. Pamenepa mayiyo analephera kuugwira mtima ndipo tsiku lina anapita ku ntchito kwa mayiyo, atamangira nsalu nchiuno koma mkati atavalamo buluku. Atafika uko anafunsa za mayiyo ndipo atamuona anamuthamangira nkuyamba kumuthidzimula kwinaku akumulalatira kuti apeze wake mwamuna. Mwamwai anthu ena analeretsa nkhondoyo koma mai wachimasomasoyo akunenetsa kuti atengana ndi mwamunayo kamba koti wamuvulaza ndipo wati masiku akudzawa apita kwawo ku Kasungu kukatsanzika kuti akukalowa banja. Chokhumudwitsa nchakuti mwamunayo akuvomereza zimenezi ndipo akunenetsa kuti amusiya ukwati mkazi wakeyo ati kamba koti wamuchititsa manyazi.

Get Your Newsletter