21-05-21

Written by  Za Mmaboma Desk

Mwamuna wina kwa Mbela mboma la Balaka amudzudzula chifukwa chomenya mkazi wake osalakwa pomuganizira kuti akuzemberana ndi mphongo ina.   Nkhaniyi ikuti mwamunayo ndi wa nsanje yoopsya moti saafuna kumuona mkazi wakeyo akuyankhulana ndi munthu wa mwamuna. Tsono chomwe chinachitika pa tsikulo nchakuti mkazi wa mkuluyo amagona pa khonde pa nyumba yake pamene mwamuna wake anali m’nyumba kuonera mpira. Mosakhalitsa mu njira yapafupi ndipakhomopo pamadutsa mnyamata wina koma pa nthawiyo nkuti akulankhulana ndi munthu wina pa foni yake ya m’manja. Mwamunayo atamva mau achimuna panjapo anaganiza kuti akuyankhulana ndi mkazi wake ndipo nthawi yomweyo anadzambatuka m’nyumbamo kusiya kuonera mpirawo, nkufikira kutsamwa mkazi wakeyo pakhosi, koma chonsecho mkaziyo anali mtulo. Pamenepa mkaziyo anadzidzimuka mokuwa ndi mantha poganizira kuti ndi wachiwembu. Izi zinachititsa kuti anthu ena apafupi athamangire ku nyumbako kuti akawone chomwe chikuchitika. Mwamunayo ataona anthuwo anadziwa kuti walakwitsa kwambili ndipo anangokokera mkazi wakeyo m’nyumba nkuthamangitsa anthuwo pakhomopo. Pamenepa anayamba kumupepesa mkazi wakeyo ndipo tsiku lotsatira anakamugulira zitenje za Java ziwiri ati ncholinga choti asaganize zopita kwawo. Komabe ngakhale izi zili chomwechi, mayiyo wakadandaula nkhaniyi kwa ankhoswe pamene mwamunayo akumayenda mogwetsa nkhope yake pansi chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.

Get Your Newsletter